Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Ubwino Wotsatila Malangizo a Yehova

Ubwino Wotsatila Malangizo a Yehova

WACICEPELE WINA KU POLAND ANASANKHA MWANZELU

N’NABATIZIKA nili na zaka 15. Patapita miyezi 6, n’nayamba upainiya wothandiza. Pambuyo pa caka cimodzi, n’nafunsila upainiya wanthawi zonse. N’tasiliza sukulu ya sekondale, n’napempha kuti nikatumikile kumalo osoŵa. N’nafuna kusamuka n’colinga cakuti nisakhale m’tauni yathu, ndi kuti nisakhalenso na ambuya amene sanali a Mboni za Yehova. Koma woyang’anila dela ananiuza kuti nizayamba kutumikila m’tauni imene n’nabadwila. Nitamva zimenezo, n’nakhumudwa koma sininamuuze mmene n’nali kumvelela. Conco, n’nangoyang’ana pansi ndi kucoka pamene tinali kuti nikaganizilepo pa zimene ananiuza. Ndiyeno, n’nauza mnzanga amene n’nali kulalikila naye kuti: “Nikuona kuti nayamba kuganiza ngati Yona. Koma pambuyo pake, Yona anamvela ndi kupita ku Nineve. Motelo, inenso nifunika kutumikila kumene aniuza.”

“Tsopano, natumikila monga mpainiya m’tauni yathu kwa zaka 4, ndipo nazindikila kuti n’nacita bwino kutsatila malangizo amene ananipatsa. Vuto langa lalikulu linali kunyalanyaza kumvela malangizo. Koma tsopano ndine wokondwela kwambili. Ndipo m’mwezi wina ninakwanitsa kutsogoza maphunzilo a Baibulo 24. Nikuthokoza kwambili Yehova cifukwa ninayamba kuphunzila Baibulo na ambuya amene anali kutsutsa coonadi.”

ZOTULUKAPO ZABWINO KU FIJI

Wophunzila Baibulo wina ku Fiji anafunika kusankha kaya kupita ku msonkhano wa cigawo, kapena kupita na mwamuna wake ku cikondwelelo ca tsiku la kubadwa la wacibale. Anapempha mwamuna wake kuti apite ku msonkhano coyamba, pambuyo pake adzabwela ku cikondwelelo. Mwamuna wake anamulola. Atacoka ku msonkhano, mkaziyo anaona kuti si canzelu kupita ku cikondwelelo cimene cingaike moyo wake wauzimu paciswe.

Mwamuna wake anauza abululu ŵake kuti mkazi wake wapempha kupita ku “msonkhano wa Mboni,” ndiyeno adzabwela ku cikondwelelo msonkhano ukatha. Iwo anakamba kuti, “Basi sabwela, cifukwa Mboni za Yehova sizicita cikondwelelo ca tsiku la kubadwa.” *

Mwamunayo anakondwela kwambili ataona kuti mkazi wake wakhala wokhulupilika, ndi kuti wamvela cikumbumtima cake. Kukhulupilika kwake kunacititsa kuti akhale na mwayi wolalikila mwamuna wake ndi anthu ena. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Mwamuna wake anayamba kuphunzila Baibulo ndi kusonkhana na mkazi wake.

^ par. 7 Onani “Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga” mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 2001.