Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

1 Kodi N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupemphela?

1 Kodi N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupemphela?

PEMPHELO. Ni nkhani zocepa m’Baibo zimene zimakopa cidwi ca anthu ambili monga pemphelo. Mwacitsanzo, ganizilani mafunso 7 amene tikambilane m’nkhani zino, onena za pemphelo, amene anthu amafunsa kaŵili-kaŵili. Kenako tifufuzile limodzi mayankho ake m’Baibo. Nkhani zimenezi zakonzedwa kuti zikuthandizeni pa nkhani ya pemphelo. Zikuthandizani kuti muyambe kupemphela kapena zikuthandizani kuti mapemphelo anu azikhala ocokela mumtima.

PADZIKO lonse lapansi anthu amakhalidwe komanso zipembedzo zosiyana-siyana amapemphela. Iwo amapemphela pa okha kapena pagulu. Amapemphela m’chalichi, m’kacisi, m’sunagoge mu mzikiti, kapenanso pamalo olambilila mizimu ya makolo. Popemphela, ena amagwada pa kansalu kopemphelelapo, kapena amagwilitsa nchito korona. Enanso amagwilitsa nchito cinthu cozungulila cimene mkati mwake amaikamo timapepala timene alembapo mapemphelo. Ena amaŵelenga mapemphelo awo m’mabuku, kapena amawalemba patimatabwa timene amatipacika pena pake.

Anthu okha ndiwo amapemphela ndipo palibe zolengedwa zinanso padziko lapansi pano zimene zimapemphela. N’zoona kuti anthufe timafanana na nyama pa zinthu zambili. Mwacitsanzo, nyama zimafunika cakudya, mpweya, komanso madzi. N’cimodzi-modzinso anthufe. Mofanana na nyama, ifenso timabadwa, timakhala na moyo, kenako timafa. (Mlaliki 3:19) Koma mosiyana na nyama, anthu amapemphela. Kodi n’cifukwa ciani zili conco?

Mwina yankho lacidule n’lakuti tiyenela kupemphela. Anthu ambili amaona kuti pemphelo ni njila yolankhulilana na munthu kapena cinthu cinacake cauzimu cimene amaciona kuti ni copatulika, coyela komanso cosatha. Baibo imasonyeza kuti tinalengedwa na mtima wofuna kupemphela. (Mlaliki 3:11) Pa nthawi ina Yesu Khristu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosowa zawo zauzimu.”—Mateyu 5:3.

Anthu amanga nyumba zopemphelelamo zambili-mbili ndipo amatha maola ambili akupemphela. Zimenezi zikusonyeza kuti anthu alidi na ‘zosowa zauzimu.’ Ena amaona kuti okha angathe kupeza zosowa zawo zauzimu kapena munthu wina akhoza kuwapatsa zimenezo. Koma anthu sangatipatse zosowa zathu zauzimu. Anthufe tili na mphamvu zocepa, moyo wathu ni waufupi ndipo sitingadziŵe zonse za m’tsogolo. Pakufunika winawake wanzelu ndiponso wamphamvu kwambili, amenenso moyo wake ni wautali kwambili kuti azitipatsa zimene tikufunikila. Zosowa zauzimu n’zimene zimaticititsa kuti tizifuna kupemphela. Koma kodi zosowa zauzimu zimenezi n’ciani?

Taganizilani mfundo iyi: Kodi mumalakalaka winawake atamakutsogolelani, kukupatsani nzelu kapena kukuthandizani kupeza mayankho pa mafunso amene munthu sangathe kuwayankha? Kodi nthawi ina munalakalaka wina atakulimbikitsani cifukwa ca cisoni cimene munali naco mutafeledwa? Kapena munalakalaka wina atakutsogolelani kuti musankhe zinthu mwanzelu pa nkhani inayake imene inakuvutitsani maganizo kwambili? Kapena kodi nthawi ina munalakalaka mutakhululukidwa chimo linalake limene linakuvutitsani maganizo kwambili?

Baibo imanena kuti zonsezi ni zifukwa zabwino zopemphelela. Baibo ni buku yothandiza kwambili pa nkhani ya pemphelo, ndipo lili na mapemphelo amene amuna na akazi ambili okhulupilika anapemphela. Anthu amenewo anapemphela pofuna kulimbikitsidwa, kutsogoleledwa, komanso kupeza mayankho a mafunso ovuta kwambili.—Salimo 23:3; 71:21; Danieli 9:4, 5, 19; Habakuku 1:3.

Ngakhale kuti mapemphelo amenewo ni osiyana kwambili, anthu amene anapemphela mapemphelo amenewa anafanana pa cinthu cimodzi. Iwo anali kudziŵa cimene cimafunika kuti pemphelo iyankhidwe. Onse amadziŵa kuti ayenela kupemphela kwa ndani. Koma anthu ambili masiku ano sadziŵa mfundo imeneyi kapenanso amainyalanyaza.