Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zimene Mungacite Kuti Muzisangalala Paukalamba Wanu

Zimene Mungacite Kuti Muzisangalala Paukalamba Wanu

KODI mumamva bwanji mukaganizila za ukalamba? Anthu ambili amakhala ndi nkhawa komanso mantha akaganizila nkhaniyi. Zili conco cifukwa nthawi zambili ukalamba umabwela ndi zinthu zokhumudwitsa monga kusaoneka bwino, kufooka kwa thupi, vuto la kuiŵalaiŵala ndi matenda osatha.

Komabe, anthu amakalamba m’njila zosiyanasiyana. Acikulile ena amakhala ndi thanzi la bwinoko ndipo sakhala ndi vuto loiŵalaiŵala. Kupita patsogolo kwa zamankhwala kwathandiza ena kuthetsa kapena kucepetsa vuto lodwaladwala. Ndipo zimenezi zapangitsa kuti anthu ambili m’maiko ena, azikhala ndi thanzi labwino komanso moyo wautali.

Koma n’zotheka kukhala osangalala paukalamba wanu kaya muli ndi vuto lobwela cifukwa ca ukalamba kapena ai. Kodi zimenezi zingatheke bwanji? Zingatheke ngati muli ndi maganizo oyenela, wokonzeka ndi wofunitsitsa kusintha. Tsopano tiyeni tione mfundo za m’Baibulo zimene zingakuthandizeni.

KHALANI WODZICEPETSA: “Nzelu zimakhala ndi anthu odzicepetsa.” (Miyambo 11:2) Pa lembali mau akuti “anthu odzicepetsa,” angaimile anthu acikulile amene amazindikila kuti sangakwanitse kucita zonse zimene anali kucita poyamba. Mwacitsanzo, Charles wa ku Brazil wa zaka 93 anati: “Ukakhala ndi moyo nthawi yaitali, umakalamba. Ndipo kunena zoona nthawi sibwelela m’mbuyo.”

Kukhala wodzicepetsa sikutanthauza kukhala ndi maganizo olakwika monga akuti, “Ndine wacikulile ndipo palibe cimene ndingacite.” Maganizo otele angacititse munthu kukhala wosasangalala. Ndipo lemba la Miyambo 24:10 limati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zocepa.” Conco, munthu wodzicepetsa amakhala ndi maganizo oyenela ndipo amayesetsa kucita zimene angathe.

Mwacitsanzo, Corrado wa ku Italy, wa zaka 77 anati: “Mukamayendetsa galimoto pokwela makata mumasintha magiya osati kuzimitsa galimotoyo. Kunena zoona, munthu akamakalamba amafunika kusintha zinthu zina ndi zina. Corrado ndi mkazi wake asintha zina ndi zina pa kagwilidwe ka nchito zapakhomo mogwilizana ndi kuculuka kwa nchitozo. Iwo acita zimenezi n’colinga cakuti asamakhale otopa kwambili kumapeto kwa tsiku. Nayenso Marian wa zaka 81 wa ku Brazil, anazindikila kuti afunika kusintha zina ndi zina pa umoyo wake. Iye anati: “Ndimagwila nchito mogwilizana ndi thanzi langa, ndipo ndimapuma mobwelezabweleza. Nthawi zina ndimapumula ndili cogona uku ndikuŵelenga kapena kumvetsela nyimbo. Ndazindikila kuti pali zinthu zina zimene ndinali kucita poyamba zimene tsopano sindingathe kuzicita.”

CITANI ZINTHU MWANZELU: Akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenela, povala mwaulemu ndi mwanzelu, osati kudzikongoletsa ndi masitayilo omangila tsitsi, golide, ngale, kapena zovala zamtengo wapatali.” (1 Timoteyo 2:9) Pa lembali mau akuti “zovala zoyenela,” akutanthauza zaulemu ndi zooneka bwino. Barbara wa ku Canada wa zaka 74 anakamba kuti: “Ndimayesetsa kuti ndizioneka bwino. Sindifuna kuoneka wadothi ngakhale kuti ndine wacikulile, ndipo ndimapewa maganizo akuti, ‘zilibe kanthu ndi mmene ndimaonekela.’” Nayenso Fern wa zaka 91, wa ku Brazil anati: “Pakapita nthawi ndimagula zovala zatsopano n’colinga cakuti ndizioneka bwino.” Nanga bwanji za amuna acikulile? Antônio wa zaka 73, wa ku Brazil, anakamba kuti: “Ndimayesetsa kuti ndizioneka bwino ndipo ndimavala zovala zaudongo ndi zoyenela.” Iye anaonjezela kuti: “Ndimasamba ndi kumeta ndevu tsiku lililonse.”

Citani zinthu mwanzelu

Komabe, simuyenela kudela nkhawa kwambili ndi maonekedwe anu mpaka kufika polephela kucita zinthu “mwanzelu.” Mwacitsanzo, Bok-im wa ku South Korea wa zaka 69 ali ndi maganizo oyenela pa nkhani ya zovala. Iye anati: “Ndimadziŵa bwino kuti sindiyenela kuvala zovala zimene ndinali kuvala ndili wacinyamata.”

KHALANI NDI MAGANIZO OYENELA: “Masiku onse a munthu wosautsika amakhala oipa, koma munthu wamtima wosangalala amacita phwando nthawi zonse.” (Miyambo 15:15) N’zoona kuti mukamakalamba, mungayambe kukhumudwa mukaganizila masiku anu aunyamata ndi zinthu zambili zimene munali kucita. Komabe muziyesetsa kupewa maganizo otelo kuti musafooke. Kuganizila kwambili zinthu zimene munali kucita kale kungakufooketseni ndi kukulepheletsani kucita zimene mungakwanitse. Mwacitsanzo Joseph wa zaka 79, wa ku Canada anati: “Ndimayesetsa kucita zimene ndingakwanitse m’malo moganizila kwambili zimene ndinali kucita poyamba.”

Khalani ndi maganizo oyenela

Kuŵelenga ndi kuphunzila kungakuthandizeni kukhala wosangalala ndiponso kutulukila zinthu zina. Conco, muziyesetsa kupeza nthawi yoŵelenga ndi kuphunzila zinthu zatsopano. Mwacitsanzo, Ernesto wa zaka 74 wa ku Philippines, amapita ku laibulale ndi kusankha buku losangalatsa lakuti aŵelenge. Iye anati: Ndimakondwela kuŵelenga nkhani zokhudza maulendo cifukwa ndikamaziŵelenga zimakhala ngati ndapita kudziko lina.” Nayenso Lennart wa ku Sweden wa zaka 75 pofuna kuphunzila zinthu, anayamba kuphunzila cinenelo cina.

KHALANI WOPATSA: “Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.” (Luka 6:38) Khalani ndi cizoloŵezi copeza nthawi yoceza ndi ena ndi kugawana nao zinthu zimene muli nazo. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kukhala wokhutila ndi wacimwemwe. Mwacitsanzo, Hosa wa ku Brazil wa zaka 85, amayesetsa kuthandiza ena ngakhale kuti ndi wacikulile. Iye anati: “Ndimatumila foni anzanga amene ndi odwala kapena amene alefulidwa ndi zinthu zina ndipo ndimawalembela makalata.” Nthawi zina ndimawatumizila tumphatso tung’onotung’ono. Ndimakondanso kuphikila odwala cakudya.”

Khalani wopatsa

Tikakhala opatsa, anthu enanso amalimbikitsidwa kukhala opatsa. Jan wa ku Sweden wa zaka 66 anati: “Ukamakonda ena, ionso amayamba kukukonda kwambili.” Kunena zoona, munthu wopatsa amalimbikitsa cikondi ndipo anthu ena amasangalala kukhala naye.

KHALANI WAUBWENZI: “Wodzipatula amafunafuna zolakalaka zake zosonyeza kudzikonda. Iye amacita zosemphana ndi nzelu zonse zopindulitsa.” (Miyambo 18:1) Ngakhale kuti pali nthawi imene mungafune kukhala nokha, musakhale ndi cizolowezi codzipatula. Mwacitsanzo, Innocent wa ku Nigeria wa zaka 72 amakonda kuceza ndi anzake. Iye anati: “Ndimakonda kuceza ndi anthu amisinkhu yosiyanasiyana.” Nayenso Börje wa ku Sweden wa zaka 85 anati: “Ndimayesetsa kukhala pamodzi ndi acinyamata. Zimene io amacita zimandicititsa kudzimva ngati ndikali wacinyamata.” Conco, nthawi zina muzipatula nthawi yoitana anzanu. Han-sik wa ku South Korea wa zaka 72 anati: “Ine ndi mkazi wanga timakonda kuitana anzathu a misinkhu yosiyanasiyana, acikulile ndi acicepele omwe, kuti ticeze nao kapena kudya nao cakudya camadzulo.”

Khalani waubwenzi

Anthu aubwenzi umatha kulankhula nao. Popeza kukhala waubwenzi kumatanthauza kulankhula ndi ena komanso kuwamvetsela akamalankhula, muzionesetsa kuti mumacita cidwi ndi anthu ena. Mwacitsanzo, Helena wa zaka 71, wa ku Mozambique anakamba kuti: “Ndine waubwenzi ndipo ndimalemekeza anthu ena. Ndimawamvetsela akamakamba n’colinga cakuti ndidziŵe maganizo ao ndi zinthu zimene amakonda. Nayenso José wa zaka 73, wa ku Brazil anati: “Anthu amakondwela kukhala ndi munthu amene amawamvetsela, kuwaganizila, kuwayamikila komanso amene ndi wansangala.”

Mukamafotokoza maganizo anu, muzisankha bwino mau kuti akhale “okoma ngati kuti mwawathila mcele.” (Akolose 4:6) Khalani woganizila ena ndi wolimbikitsa.

KHALANI WOYAMIKILA: “Sonyezani kuti ndinu oyamikila.” (Akolose 3:15) Mukalandila thandizo, muziyamikila. Kukamba mau oyamikila kungakuthandizeni kupeza anzanu abwino. Mwacitsanzo, Marie-Paule wa zaka 74, wa ku Canada anati: “Ine ndi mwamuna wanga posacedwapa tinasamuka kucoka m’nyumba yaikulu kupita mu yaing’ono ndipo anzathu ambili anatithandiza. Panthawiyo sitinawayamikile mokwanila, koma tinalemba makalata aciyamikilo kwa aliyense payekha ndipo ena a io tinawaitana kuti adzadye nafe cakudya.” Nayenso Jae-won wa zaka 76 wa ku South Korea amayamikila abale amene amamunyamula pa galimoto kupita ku Nyumba ya Ufumu. Iye anati: “Ndimayamikila kwambili thandizo limeneli ndipo ndimapeleka ndalama ya mafuta. Nthawi zina ndimakonza tumphatso tung’onotung’ono ndi kulemba kakalata kaciyamikilo.”

Kuonjezela apo, muziyamikila moyo umene muli nao. Mfumu ya nzelu Solomo inatikumbutsa kuti: “Galu wamoyo ali bwino kuposa mkango wakufa.” (Mlaliki 9:4) Inde, zingatheke kusangalala pa ukalamba wanu ngati muli ndi maganizo oyenela komanso kukhala wofunitsitsa kusintha.

Khalani woyamikila