Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

ilbusca/E+ via Getty Images

KHALANI MASO!

N’cifukwa Ciyani Anthu Akulephela Kukhazikitsa Mtendele?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

N’cifukwa Ciyani Anthu Akulephela Kukhazikitsa Mtendele?—Kodi Baibo Ikutipo Ciyani?

 Atsogoleli a dziko komanso mabungwe a padziko lonse alephela kubweletsa mtendele pa dziko. Masiku ano, nkhondo komanso zaciwawa zawonjezeka kwambili kuposa mmene zinalili kucokela pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse. Anthu ambili padziko lapansi, okwana pafupifupi 2 biliyoni, amakhala m’madela omwe mukucitika nkhondo komanso zaciwawa zimenezi.

 N’cifukwa ciyani anthu sangabweletse mtendele? Kodi Baibo ikutipo ciyani?

Zifukwa zitatu zimene zimalepheletsa anthu kubweletsa mtendele

  1.  1. Anthu ali na makhalidwe amene amawalepheletsa kukhazikitsa mtendele. Baibo inakambilatu kuti m’nthawi yathu ino, “anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, odzikweza, . . . osakhulupilika, . . . osafuna kugwilizana ndi ena, . . . osadziletsa, oopsa, . . . odzitukumula cifukwa ca kunyada.”—2 Timoteyo 3:2-4.

  2.  2. Anthu, aliyense payekha-payekha kapena monga gulu, sangakwanitse kuthetsa mavuto awo popanda thandizo la Mlengi wawo, Yehova a Mulungu. Baibo imaonetsa kuti “munthu amene akuyenda alibe ulamulilo wowongolela mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

  3.  3. Dziko lapansi likulamulidwa na Satana Mdyelekezi, amene ni wolamulila wamphamvu komanso woipa. Iye “akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Malinga ngati “dziko lonse lili mʼmanja mwa woipayo,” nkhondo na zaciwawa zidzakhalapobe.—1 Yohane 5:19.

Kodi ndani angabweletsa mtendele?

 Baibo imatitsimikizila kuti anthu sangabweletse mtendele, koma Mulungu yekha.

  •   “‘Ndikudziwa bwino zimene ndikuganiza zokhudza inu. Ndikuganiza zokupatsani mtendele osati masoka ndiponso zokupatsani tsogolo labwino ndi ciyembekezo cabwino, akutelo Yehova.’”—Yeremiya 29:11.

 Kodi Mulungu adzakwanilitsa bwanji lonjezo limeneli? “Mulungu amene amapeleka mtendele [adzaphwanya] Satana.” (Aroma 16:20) Mulungu adzaseŵenzetsa boma la kumwamba pobweletsa mtendele pa dziko lonse lapansi. Baibo imachula bomalo kuti “Ufumu wa Mulungu.” (Luka 4:43) Mu ulamulilo wa Yesu Khristu, Mfumu ya Ufumu umenewo, anthu adzaphunzitsidwa mmene angakhalile pamtendele.—Yesaya 9:6, 7.

a Yehova ndilo dzina la Mulungu.—Salimo 83:18.