Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 130

Khalani Wokhululuka

Khalani Wokhululuka

(Salimo 86:5)

  1. 1. Atate Yehova,

    Anapeleka Yesu

    Kuti iye atifele,

    Acotsepo na imfa.

    Tikasintha na kulapa,

    Tikasiya zoipa,

    Mu dzina la Yesu Khristu

    Tidzakhululukidwa.

  2. 2. Monga ‘tate wathu,

    Tikhale na cifundo;

    Tikhululukile ena;

    Tionetse cikondi.

    Ticitilane ulemu,

    Ndipo tipililane.

    Ngati tikhululukila

    Tidzakhululukidwa.

  3. 3. Tonse tionetse

    Mkhalidwe wa cifundo.

    Tisadane na abale,

    Tiŵakomele mtima.

    Tikatengela Yehova

    Wopambana m’cikondi,

    Tidzakhululukiladi

    Monga Atate wathu.

(Onaninso Mat. 6:12; Aef. 4:32; Akol. 3:13.)