Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 150

Funani Cipulumutso ca Mulungu

Funani Cipulumutso ca Mulungu

(Zefaniya 2:3)

  1. 1. Mitundu ya dziko

    Itsutsana na Yesu.

    Nthawi ya kulamulila,

    Kwa anthuwo inatha.

    Tsopano Ufumu

    Wa Yehova wafika.

    Khristu adzaŵafafaniza

    Adani ake onse.

    (KOLASI)

    Funani Yehova M’lungu,

    Na cipulumutso cake.

    Imwe imani

    Ku mbali yake,

    Ndipo khulupilikani.

    Adzakupulumutsani

    Na dzanja lake.

  2. 2. Tsopano ni nthawi,

    Yoti anthu asankhe.

    Kumvela olo kukana

    Za uthenga wabwino.

    Mayeselo athu

    Olo ativutitse

    Yehova ‘dzatisamalila.

    Amamva mapemphelo.

    (KOLASI)

    Funani Yehova M’lungu,

    Na cipulumutso cake.

    Imwe imani

    Ku mbali yake,

    Ndipo khulupilikani.

    Adzakupulumutsani

    Na dzanja lake.

(Onaninso 1 Sam. 2:9; Sal. 2:2, 3, 9; Miy. 2:8; Mat. 6:33.)