Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 20

Munapeleka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

Munapeleka Mwana Wanu Wobadwa Yekha

(1 Yohane 4:9)

  1. 1. Yehova, Atate,

    Tikuyamikani

    Potuma Yesu

    Kuti atifele.

    Timadzipeleka

    Na mtima umodzi.

    Tidziŵitse ena,

    Cifunilo canu.

    (KOLASI)

    Mwana wanu Yesu,

    Munamupeleka.

    Tidzakutamandani,

    potipatsa Mwana wanu.

  2. 2. Poona cifundo

    Na kukoma mtima,

    Tifuna kukhala

    Mabwenzi anu.

    Yopambana zonse

    Ni mphatso ya Yesu.

    Anadzipeleka

    Cifukwa ca ise.

    KOLASI)

    Mwana wanu Yesu,

    Munamupeleka.

    Tidzakutamandani,

    potipatsa Mwana wanu.

    (KUTSILIZITSA)

    Yehova, Atate, tikuyamikani.

    Cifukwa copeleka Mwana wanu Yesu.

(Onaninso Yoh. 3:16; 15:13.)