Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 29

Tikhala Monga mwa Dzina Lathu

Tikhala Monga mwa Dzina Lathu

(Yesaya 43:10-12)

  1. 1. Yehova M’lungu ndinu wamuyaya,

    Nchito zanu zonse ni zangwilo.

    Ndinu gwelo la co’nadi na nzelu,

    Inu mulamulila kumwamba.

    Timakondwa kukutumikilani,

    Kulengeza za Ufumu wanu.

    (KOLASI)

    Tinyadila kukhala Mboni zanu,

    Tikhala monga mwa dzina lathu!

  2. 2. Ni mwayi wathu kukuchukitsani

    Pophunzitsa ena coonadi.

    Utumiki umene mwatipatsa,

    Umatibweletsela cimwemwe.

    Lomba tidziŵika na dzina lanu,

    Ticitile umboni za inu.

    (KOLASI)

    Tinyadila kukhala Mboni zanu,

    Tikhala monga mwa dzina lathu!

(Onaninso Deut. 32:4; Sal. 43:3; Dan. 2:20, 21.)