Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 81

Umoyo wa Mpainiya

Umoyo wa Mpainiya

(Mlaliki 11:6)

  1. 1. Kukaca kuseni, tikali na tulo,

    Timayenda

    kulalikila anthu kulikonse.

    Timamwetulila poŵalalikila,

    Ndipo sitileka,

    ngakhale ena samvetsela.

    (KOLASI)

    Uyu ni umoyo

    umene tasankha;

    Kucita zofuna za M’lungu.

    M’dzuŵa na mu mvula

    Ise tipilila.

    Timaonetsa kuti M’lungu tim’konda.

  2. 2. Pofika m’madzulo, tikhala olema,

    Koma timakhala

    na cisangalalo mumtima

    Uyu ni umoyo ise tinasankha

    Tiyamika Yehova

    cifukwa watidalitsa.

    (KOLASI)

    Uyu ni umoyo

    umene tasankha;

    Kucita zofuna za M’lungu.

    M’dzuŵa na mu mvula

    Ise tipilila.

    Timaonetsa kuti M’lungu tim’konda.

(Onaninso Yos. 24:15; Sal. 92:2; Aroma 14:8.)