Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NYIMBO 85

Tilandilane Wina ndi Mnzake

Tilandilane Wina ndi Mnzake

(Aroma 15:7)

  1. 1. Inu nonse takulandilani,

    Mwabwela kuti muphunzile,

    Mau a M’lungu, na njila zake.

    Tiyamike Yehova potiitana.

  2. 2. Tiyamika Atate Yehova,

    Tili na ‘bale acikondi.

    Nthawi zonse amatilandila,

    Tilandile obwela kudzasonkhana.

  3. 3. Yehova afuna anthu onse,

    Aphunzile co’nadi cake.

    Mwa Mwana wake atiitana.

    Tilandile onse mocoka mu’mtima.

(Onaninso Yoh. 6:44; Afil. 2:29; Chiv. 22:17.)