Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

FUNSO 18

Kodi Mungatani Kuti Mukhale pa Ubwenzi ndi Mulungu?

“Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.”

Salimo 65:2

“Uzikhulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usamadalire luso lako lomvetsa zinthu. Uzimukumbukira mʼnjira zako zonse, ndipo iye adzawongola njira zako.”

Miyambo 3:5, 6

“Moyo wosatha adzaupeza akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ndi woona, komanso za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.”

Yohane 17:3

“Kwenikweni [Mulungu] sali kutali ndi aliyense wa ife.”

Machitidwe 17:27

“Ine ndikupitiriza kupemphera kuti chikondi chanu chipitirize kukula kwambiri, limodzi ndi kudziwa zinthu molondola komanso kuzindikira zinthu bwino kwambiri.”

Afilipi 1:9

“Ngati wina akusowa nzeru, azipempha kwa Mulungu ndipo adzamupatsa, chifukwa iye amapereka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapereka mosatonza.”

Yakobo 1:5

“Yandikirani Mulungu ndipo iyenso adzakuyandikirani. Yeretsani manja anu ochimwa inu, ndipo yeretsani mitima yanu okayikakayika inu.”

Yakobo 4:8

“Kukonda Mulungu kumatanthauza kutsatira malamulo ake, ndipo malamulo akewo si ovuta kuwatsatira.”

1 Yohane 5:3