Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO

Kodi Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi?

Kodi Mungatani Kuti Muzigwiritsa Ntchito Bwino Nthawi?

Nthawi zambiri anthufe timanena kuti: “Ndikadakhala ndi nthawi,” ndikanachita zakutizakuti. Kunena zoona palibe amene ali ndi nthawi yochuluka kuposa mnzake. Chifukwa anthu olemera ndi osauka omwe, ali ndi nthawi yofanana. Komanso, anthu olemera ndi osauka akhoza kupeza nthawi posachita zinthu zosafunika kwenikweni. Nthawi ikadutsa, sibwereranso. Choncho, ndi nzeru kugwiritsa ntchito bwino nthawi yomwe tili nayo. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Taonani zinthu 4 zotsatirazi zomwe zathandiza anthu ambiri kuti azigwiritsa ntchito bwino nthawi yawo.

Njira Yoyamba: Muzichita Zinthu Mwadongosolo

Muziyamba ndi zinthu zofunika kwambiri. Baibulo limatilangiza kuti: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.” (Afilipi 1:10) Tsiku lililonse m’mawa, ganizirani za zinthu zimene mukufuna kuchita pa tsikulo. Ndiyeno ganizirani zofunika kwambiri kapena zoyenera kuchitidwa mwamsanga. Koma muzikumbukira kuti zinthu zina zikhoza kukhala zofunika kwambiri, koma si zofunika kuzichita nthawi yomweyo. Mwachitsanzo, kuphika chakudya chamasana n’kofunika kwambiri, koma simungachite zimenezi mutangodzuka. Komanso, kuonera pulogalamu inayake pa TV kapena kumvera pulogalamu inayake ya pa wailesi, kungafune kuti muchite zimenezo pa nthawi imene pulogalamuyo imaonetsedwa kapena kuulutsidwa. Komatu zimenezi si zofunika kwambiri. *

Muzikonzekereratu zimene mukufuna kuchita. Lemba la Mlaliki 10:10 limati: “Ngati nkhwangwa yabuntha ndipo munthu sanainole, adzawononga mphamvu zake pachabe.” Limatinso: “Kugwiritsa ntchito bwino nzeru kumapindulitsa.” Kodi tikuphunzirapo chiyani pamenepa? Kukonzekereratu zinthu, komwe kuli ngati kunola nkhwangwa, kungathandize kuti musawononge nthawi yaitali pochita zinthuzo. Komanso pochita zinthu, musamayambe ndi zinthu zosafunika kwenikweni, apo ayi, muzingozisiya kumene, chifukwa zinthu zoterezi zingangokuwonongerani nthawi ndi mphamvu. Ngati mwaona kuti muli ndi nthawi chifukwa choti mwamaliza msanga kuchita zinazake, yambani kuchita zina zimene munakonza kuti muzichite pa nthawi ina. Mukamakonzekereratu zochita, mumakhala ngati munthu amene wanoleratu nkhwangwa yake asanayambe kuigwiritsa ntchito, ndipo izi zingachititse kuti muzichita zinthu zambiri pa tsiku.

Musamadzichulukitsire zochita. Musamathe nthawi yanu yambiri pa zinthu zosafunika kwenikweni kapenanso zosafunika n’komwe, zomwe zingangokuwonongerani nthawi. Kudzichulukitsira zochita kungapangitse kuti muzikhala ndi nkhawa komanso wosasangalala.

 Njira Yachiwiri: Muzipewa Zinthu Zimene Zingakuwonongereni Nthawi

Kuzengereza ndiponso kulephera kusankha zochita. Lemba la Mlaliki 11:4 limati: “Woyang’ana mphepo sadzabzala mbewu, ndipo woyang’ana mitambo sadzakolola.” Kodi tikuphunzira chiyani palembali? Kuzengereza kuchita zinthu kungatiwonongere nthawi komanso sitingachite zambiri pa tsiku. Mlimi amene amadikira kuti zinthu zonse zikhale bwino asanayambe kulima, sangadzale komanso kudzakolola mbewu zake. Choncho tisamalole zinthu zosayembekezereka pamoyo kutipangitsa kuti tilephere kusankha zochita. Kapena tingaone kuti tiyenera kudikira kaye mpaka titapeza mfundo zonse zimene tikufuna tisanasankhe zochita. N’zoona kuti, tisanasankhe zochita pa zinthu zofunika kwambiri, tiyenera kuganizira kaye kwambiri nkhaniyo komanso kufufuza zinthu zina. Lemba la Miyambo 14:15 limati: “Wochenjera amaganizira za mmene akuyendera.” Komabe tiyenera kudziwa kuti pali zinthu zina zoti sitingazidziwiretu. Choncho tisamalephere kusankha zochita chifukwa cha zinthu ngati zimenezi.—Mlaliki 11:6.

Kufuna kuchita zinthu mosalakwitsa. Lemba la Yakobo 3:17 limati: “Nzeru yochokera kumwamba, [kapena kuti kwa Mulungu] . . . ndi yoyera.” N’zoona kuti aliyense amafuna kuti azichita bwino zinthu. Komabe kuganizira kwambiri zimenezi kungachititse kuti tizifunitsitsa kuchita chilichonse popanda kulakwitsa, ndipo zimenezi zingangochititsa kuti tizikhala okhumudwa nthawi zonse. Mwachitsanzo, munthu amene akuphunzira chinenero china sayenera kukhumudwa akalakwitsa. Ayenera kudziwa kuti zimenezo zingamuthandize kuti aphunzirepo kanthu. Koma munthu amene amafuna kuchita zinthu mosalakwitsa, akhoza kulephera kulankhula chinenero chatsopano chifukwa choopa kulakwitsa. Choncho ndi bwino kukhala odzichepetsa pochita zinthu. Lemba la Miyambo 11:2 limati: “Nzeru zimakhala ndi anthu odzichepetsa.” Ndipotu anthu odzichepetsa sadziganizira kwambiri, ndipo anthu akamawaseka pa zimene alakwitsa, sadandaula nazo.

“Kuti tipeze chinthu, sikuti timakhala kuti tagwiritsa ntchito ndalama zokha. Timakhalanso kuti tagwiritsa ntchito nthawi.”—What to Do Between Birth and Death.

 Njira Yachitatu: Musamachite Zinthu Monyanyira

Muzipezanso nthawi yochita zosangalatsa. “Kupuma pang’ono kuli bwino kuposa kugwira ntchito mwakhama ndi kuthamangitsa mphepo.” (Mlaliki 4:6) Anthu amene amagwira ntchito monyanyira, nthawi zambiri sakhala ndi mpata wosangalala ndi zotsatira za ntchito yawoyo chifukwa nthawi zonse amangokhala otopa. Pamene anthu aulesi nawonso, m’malo moti azigwira ntchito amawononga nthawi pa zinthu zosafunika. Koma Baibulo limatilangiza kuti tisamagwire ntchito monyanyira komanso tisakhale aulesi. Limati tiyenera kugwira ntchito mwakhala n’kusangalala ndi zotsatira za ntchito yathuyo. Kusangalala koteroko ndi “mphatso yochokera kwa Mulungu.”—Mlaliki 5:19.

Muzigona Mokwanira. Munthu wina amene analemba nawo Baibulo ananena kuti: “Ndidzagona pansi ndi kupeza tulo mu mtendere.” (Salimo 4:8) Nthawi zambiri munthu wamkulu amafunika kugona maola 8 kuti thupi lake lizigwira ntchito bwino. Kugona mokwanira n’kofunika kwambiri chifukwa kumathandiza kuti munthu azitha kukumbukira zinthu komanso kuti aziphunzira zinthu msanga. Choncho kugona sikuwononga nthawi. Munthu amene sagona mokwanira saphunzira msanga zinthu, angathe kuchita ngozi, sachedwa kukhumudwa komanso amalakwitsa zinthu.

Muzikhala ndi zolinga zimene mungazikwaniritsedi. Baibulo limati: “Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima.” (Mlaliki 6:9) Apa mfundo ndi yoti, munthu wanzeru salola kuti azingotsogoleredwa ndi zolakalaka za mtima wake, makamaka zimene sangazikwanitse kapenanso sizingachitike n’komwe. Choncho satengeka ndi zomwe otsatsa malonda amanena kapena kutengeka ndi zoti atha kupeza ngongole mosavuta. M’malomwake amaganizira kwambiri za zinthu zimene angathedi kuzipeza, kapena kuti zimene ‘amaziona ndi maso ake.’

 Njira ya 4: Muziyendera Mfundo za Makhalidwe Abwino

Ganizirani mfundo zimene mumayendera. Kuti muone kuti chinthu ichi ndi chabwino, chofunika komanso choyenera kuwonongerapo nthawi, zimadalira mfundo zimene mumayendera. Ngati pali chinthu chinachake chimene mukufuna kukwaniritsa pa moyo wanu, mfundo zimene mumayendera zimakhala zogwirizana ndi cholinga chimenecho. Choncho, ngati mumayendera mfundo zabwino, zingakuthandizeni kuti muzichita zinthu zofunika kwambiri komanso kuti nthawi zonse, muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu. Kodi mfundo zimenezi mungazipeze kuti? Anthu ambiri amaona kuti mfundo zoterezi zimapezeka m’Baibulo.—Miyambo 2:6, 7.

Khalidwe lanu lalikulu lizikhala chikondi. Lemba la Akolose 3:14 limanena kuti chikondi “chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.” Kuti tikhaledi osangalala makamaka m’banja, tiyenera kukhala ndi chikondi. Anthu amene amanyalanyaza mfundo imeneyi, n’kumangoganizira kwambiri ntchito yawo kapena kupeza chuma, amakhala osasangalala. N’chifukwa chake Baibulo limanena kuti khalidwe lofunika kwambiri ndi chikondi, ndipo limatchula khalidweli kambirimbiri.—1 Akorinto 13:1-3; 1 Yohane 4:8.

Muzipeza nthawi yochita zinthu zauzimu. Munthu wina, dzina lake Geoff, ali ndi mkazi wabwino, ana awiri, anzake abwino komanso ntchito yabwino ya kuchipatala. Koma akamagwira ntchito yakeyi ankaona anthu akuvutika komanso kumwalira. Iye ankadzifunsa kuti: “Kodi umu ndi mmene moyo uyenera kukhalira?” Ndiye tsiku lina anawerenga magazini othandiza kuphunzira Baibulo omwe amafalitsidwa ndi Mboni za Yehova, ndipo anapeza mayankho ogwira mtima.

Geoff anafotokozera mkazi ndi ana ake zimene anawerenga m’magaziniwo, ndipo nawonso anachita chidwi. Banjali linayamba kuphunzira Baibulo ndipo zimenezi zinathandiza kuti azisangalala kwambiri komanso kuti azigwiritsa ntchito bwino nthawi yawo. Kuphunzira Baibulo kunawathandizanso kukhala ndi chiyembekezo chodzakhala ndi moyo wosatha m’dziko limene simudzakhala mavuto alionse.—Chivumbulutso 21:3, 4.

Zimene zinachitikira Geoff zikutikumbutsa mawu a Yesu Khristu akuti: “Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyu 5:3) Inunso mungachite bwino kumapeza nthawi yochita zinthu zauzimu. Kunena zoona, palibe njira yabwino yogwiritsa ntchito nthawi kuposa kuchita zimenezi. Izi zidzakuthandizani kuti mukhale ndi moyo wabwino.

^ ndime 5 Onani nkhani yakuti, “Mfundo 20 Zothandiza Kuti Muzikhala ndi Nthawi Yokwanira” mu Galamukani! ya April 2010.