Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Ngati Mwana Wanu Wamkazi Akuvutika Maganizo

Ngati Mwana Wanu Wamkazi Akuvutika Maganizo

VUTO LIMENE LIMAKHALAPO

Mwana wanu wazaka 13 wakuuzani kuti akuvutika maganizo. Inu simukukhulupirira zimenezi ndipo mukuganiza kuti, ‘Mwana wazaka 13 angavutike maganizo? N’zosatheka zimenezo, ameneyu adakali mwana.’ Koma musanamuuze mwana wanu zimenezi, ganizirani kaye zinthu zina zimene zingachititse mtsikana wazaka zimenezi, kuyamba kuvutika maganizo.

ZIMENE ZIMACHITITSA

Kukula. Mtsikana akamakula angayambe kukhala ndi nkhawa, makamaka ngati watha msinkhu mochedwa kapena mofulumira kuposa atsikana a msinkhu wake. Mtsikana wina, yemwe pano ali ndi zaka 20 dzina lake Anna, * ananena kuti: “Ndinali m’gulu la atsikana oyamba kuvala khamisolo ndipo zimenezi zinkandisowetsa mtendere kwabasi. Ndikadziyerekeza ndi atsikana azaka zanga, ndinkangodziona ngati mbewu ya haibulidi pakati pa mbewu za makolo.”

Kusinthasintha. Mtsikana wina, yemwe panopa ali ndi zaka 17 dzina lake Karen, anati: “Zimene zinkandichitikira zinkandinyasa kwambiri. Ndinkakhala wosangalala kwambiri masana koma kukangoda ndinkakhala wokhumudwa kwambiri mpaka kuyamba kulira. Sindinkadziwa kuti chinkandichitikira n’chiyani. Ndinkangoona kuti ndikulephera kudzigwira.”

Kutha msinkhu. Mtsikana wina, dzina lake Kathleen, ananena kuti: “Ngakhale kuti mayi anga anandiuziratu zimene zidzachitike ndikadzatha msinkhu, zitandichitikira ndinasokonezeka maganizo. Ndinkapita kubafa kukasamba kambirimbiri chifukwa ndinkangodziona ngati wauve. Komanso azichimwene anga atatu ankangokhalira kundiseka. Ankangoona ngati zimene zandichitikirazo n’zoseketsa.”

Kusowa anthu ocheza nawo. Mtsikana wina, dzina lake Marie yemwe panopa ali ndi zaka 18, ananena kuti: “Ndili ndi zaka 12 mpaka 14, anzanga ankandikakamiza kuti ndizichita zomwe iwowo amachita. Ana akusukulu kwathu ankadana ndi aliyense amene ankachita zosiyana ndi zimene iwo ankachita.” Mtsikana winanso wazaka 14, dzina lake Anita, anati: “Kwa mtsikana wa msinkhu wangawu, kukhala ndi anzako ocheza nawo ndi nkhani yaikulu, ndipo zimakhala zowawa kwambiri ukamasowa wocheza naye.”

 ZIMENE MUNGACHITE

Mulimbikitseni mwana wanuyo kuti azikuuzani zimene zikumuvutitsa maganizo. Poyamba sangakhale womasuka kukuuzani zimene zikumudetsa nkhawa. Komabe lezani mtima ndipo tsatirani malangizo a m’Baibulo akuti tizikhala ‘ofulumira kumva, odekha polankhula.’—Yakobo 1:19.

Mwana wanu akakuuzani kuti akuvutika maganizo, musaone ngati zachibwana. Kumbukirani kuti iyeyo sanakumane ndi zambiri ngati inuyo, choncho sakudziwa zoyenera kuchita akakumana ndi vuto.—Lemba lothandiza: Aroma 15:1.

Musamamupanikize ndi ntchito zambiri. Mogwirizana ndi zimene buku lina linanena (Teach Your Children Well), achinyamata amene amakhala ndi zochita zambiri “kawirikawiri amakhala ndi zizindikiro za kuvutika maganizo monga kupweteka kwa mutu komanso m’mimba.”—Lemba lothandiza: Afilipi 1:9, 10.

Muzionetsetsa kuti mwana wanuyo akugona mokwanira. Achinyamata ambiri sagona mokwanira. Koma wachinyamata akamapanda kugona mokwanira, amaiwalaiwala zinthu komanso zimachititsa kuti azivutika maganizo kwambiri.—Lemba lothandiza: Mlaliki 4:6.

Muthandizeni kudziwa zimene angachite akamavutika maganizo. Kwa atsikana ena, kuchita masewera olimbitsa thupi kumathandiza kuti asamavutike maganizo kwambiri. Baibulo limanena kuti “kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.” (1 Timoteyo 4:8) Pamene kwa atsikana ena, kulemba zimene zikuwavutitsa maganizo kumawathandiza. Mtsikana wina wa zaka 22, dzina lake Brittany, ananena kuti: “Ndinkalemba vuto lililonse limene likundisautsa. Zimenezi zinkandithandiza kudziwa mmene zinthu zililidi, ndipo ndinkatha kupeza njira yabwino yothetsera vutolo kapena kuona kuti ndingalipirire bwanji.”

Muzisonyeza chitsanzo chabwino. Kodi inuyo mumatani mukamavutika maganizo? Kodi mumachita zinthu zambirimbiri nthawi imodzi, zimene zimangochititsa kuti mukhale wopanikizika kwambiri? Kodi mumatanganidwa mpaka kufika polephera kupeza nthawi yochita zinthu zofunika kwambiri? Lemba la Afilipi 4:5 limanena kuti: “Anthu onse adziwe kuti ndinu ololera.” Muyenera kudziwa kuti mwana wanu amaona zimene mumachita, kaya ndi zabwino kapena zoipa ndipo nayenso amatengera zomwezo.

^ ndime 6 Tasintha mayina m’nkhaniyi.