Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

“Ndimayesetsa Kuti Ndisamangoganizira za Matenda Anga”

“Ndimayesetsa Kuti Ndisamangoganizira za Matenda Anga”

“Ndili ndi zaka 10, ndinadwala kwambiri ndipo ndinkalephera kugona komanso kudzuka ndekha. Ndikamayenda ndinkamva kupweteka komanso pakhosi pankandiwawa kwambiri moti ndinkalephera kumeza mankhwala. Kenako ndinatuluka zilonda zosapola ndipo zinayamba kuwola. Ndinalinso ndi zilonda za m’mimba komanso ndinkamva kutentha pamtima. Pa nthawiyi sindinkadziwa kuti chikundichitikira n’chiyani.”—Elisa.

Ngakhale kuti Elisa satha kuchita zambiri, amasangalala akamaphunzitsa anthu Baibulo

ELISA amadwala matenda enaake otchedwa Scleroderma. Matendawa amaumitsa khungu ndipo ndi ofala padziko lonse moti pafupifupi anthu 2.5 miliyoni ali nawo. Matendawa alipo a mitundu iwiri. Mtundu woyamba umatchedwa localized scleroderma ndipo umakonda kugwira ana.

Koma Elisa amadwala mtundu wachiwiri womwe umatchedwa systemic scleroderma. Matendawa samangoumitsa khungu koma amawononganso ziwalo zam’kati monga impso, mtima, mapapo komanso matumbo. Elisa anamupeza ndi matendawa ali ndi zaka 10. Madokotala anamupatsa chithandizo koma anamuuza kuti akhala ndi moyo zaka 5 zokha basi. Koma patatha zaka 5 Elisa sanamwalire ndipo tsopano padutsa zaka 14. Ngakhale kuti sanachire, amayesetsa kuti asamangoganizira za matenda akewo. Mtolankhani wa Galamukani! anacheza naye kuti adziwe zokhudza matenda ake komanso zimene zimamuthandiza kupirira.

Ndi liti pamene unayamba kumva kuti m’thupi mwako simuli bwino?

Ndili ndi zaka 9, ndinavulala pachigongono ndipo pankapweteka kwambiri. Balalo silinkapola ndipo linkangokula. Atandiyeza magazi anapeza kuti ndili ndi matenda otchedwa scleroderma. Chifukwa choti matenda anga ankangokulirakulirabe, ine ndi makolo anga tinaganiza zopeza dokotala amene amadziwa bwino za matendawa.

Ndiye munamupeza dokotalayo?

Tinangopeza dokotala amene amadziwako za matendawa. Dokotalayu anandipatsa chithandizo champhamvu cha mankhwala. Anauza makolo anga kuti zimenezi zithandiza kuti matendawa asafalikire mwamsanga m’thupi komanso kuti ndikhalebe ndi moyo zaka zina 5. Koma anatiuzanso kuti chithandizochi chichititsa kuti chitetezo cha m’thupi mwanga chitsike. Zimenezi zinapangitsa kuti ndikhale bwenzi la mphasa.

Koma zaka 5 ananenazo zinadutsatu, si choncho?

Zoona. Si ine ndili moyo mpaka pano? Komabe, ndili ndi zaka 12 ndinayamba kumva kupweteka kwambiri pamtima ndipo nthawi zina pankandipweteka kawiri tsiku lililonse kwa maminitsi 30. Ululu wake unali wosapiririka moti ndinkalira mokuwa.

Chinkachititsa zimenezi n’chiyani?

Madokotala anapeza kuti magazi anga anali ochepa kwambiri ndipo mtima wanga unkapopa magazi movutikira kuti akafike kuubongo. Mankhwala amene anandipatsa anandithandiza ndithu, moti patatha milungu ingapo ndinayamba kupezako bwino. Chifukwa cha zimene zinachitikazi ndinayamba kuona kuti nthawi iliyonse zinthu zikhoza kusintha pa moyo wanga. Ndinkaona kuti palibe chimene ndingachite kuti ndisamadwale.

Tsopano patha zaka 14 chikupezere ndi matendawa. Kodi panopa ukupeza bwanji?

Ndimamvabe ululu komanso vuto langali limachititsa kuti ndizidwaladwala. Ndimadwala matenda monga zilonda za m’mimba, vuto la m’mapapo komanso ndimamva kutentha kwambiri pamtima. Koma ndimayesetsa kupeza zochita zina m’malo momangoganizira za matenda angawa.

Ndiye umachita chiyani?

Ndimakonda kujambula, kusoka komanso kupanga zibangili. Komanso popeza ndine wa Mboni za Yehova, ndimaphunzitsa anthu Baibulo ndipo zimenezi zimandithandiza kwambiri. Ndipotu pali anthu angapo amene ndaphunzira nawo Baibulo. Nthawi zina ndimalephera kupita kunyumba za anthu kukaphunzira nawo. Zikatere ndimathandiza a Mboni anzanga akamaphunzira Baibulo ndi anthu a m’dera lathu. Kuphunzitsa anthu Baibulo kumandithandiza kukhala wosangalala kwambiri.

Munthu woti umadwaladwala, n’chifukwa chiyani umadzivutitsanso kugwira ntchito imeneyi?

Ndimadziwa kuti ntchitoyi ndi yofunika komanso yothandiza kwambiri. Komanso ndikamagwira ntchitoyi ndimasangalala kwambiri ndipo ndimaiwala za matenda anga.

Baibulo limakuthandiza bwanji kuti usamadandaule kwambiri?

Limandikumbutsa kuti mavuto anga komanso a anthu onse atha posachedwapa. Lemba la Chivumbulutso 21:4 limati pa nthawi yake, Mulungu ‘adzapukuta misozi yonse ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka.’ Kuganizira vesi limeneli ndi enanso kumandithandiza kukhulupirira kwambiri malonjezo a Mulungu akuti anthu omwe ali ndi matenda aakulu komanso anthu ena onse sazidzavutikanso.