Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhululukirana kuli ngati kuzimitsa moto, kumathandiza mukasemphana maganizo

MWAMUNA NDI MKAZI WAKE

4: Kukhululukirana

4: Kukhululukirana

ZIMENE ZIMACHITIKA

Munthu akakhululukira mnzake saganiziranso za nkhaniyo kapena kumusungira chifukwa. Kukhululuka sikutanthauza kuchepetsa nkhani imene yachitika kapena kungochita zinthu ngati kuti palibe chomwe chalakwika.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.”​—Akolose 3:13.

Aaron ananena kuti: “Ukamakonda munthu winawake, suganizira kwambiri zomwe amalakwitsa. M’malomwake umangoona zabwino zomwe akuyesetsa kuchita.”

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Kusunga zifukwa kungakudwalitseni komanso kukusokonezani maganizo. Kukhozanso kusokoneza kwambiri banja lanu.

A Julia ananena kuti: “Tsiku lina mwamuna wanga anandikhumudwitsa kenako n’kundipepesa. Zinandivuta kwambiri kuti ndimukhululukire. Koma patapita nthawi ndinamukhululukira. Komabe ndimadziimba mlandu kuti sindinachite zimenezi mofulumira chifukwa zinasokoneza kwambiri ubwenzi wathu.”

ZIMENE MUNGACHITE

YESANI KUCHITA IZI

Ngati nthawi ina mwamuna kapena mkazi wanu atadzalankhula kapena kuchita zinthu zomwe zingadzakukhumudwitseni, mudzadzifunse kuti:

  • Kodi ndakhumudwa pa chifukwa chomveka?

  • Kodi ndi nkhani yaikulu moti ndingafune kuti andipepese kapena ndikhoza kungoinyalanyaza?

ZOTI MUKAMBIRANE

  • Kodi zimatitengera nthawi yaitali bwanji kuti tikhululukirane?

  • Kodi tingatani kuti tizikhululukirana mofulumira tikangolakwirana?

ZIMENE ZINGAKUTHANDIZENI

  • Ngati wina wakukhumudwitsani, musamakwiyire mwamuna kapena mkazi wanu.

  • Muzimumvetsa mwamuna kapena mkazi wanu chifukwa “tonsefe timapunthwa nthawi zambiri.”—Yakobo 3:2.

A Kimberly ananena kuti: “Zimakhala zosavuta kukhululukirana ngati tonse talakwitsa. Koma ngati walakwitsa ndi mmodzi zimakhala zovutirapo. Pamafunika kudzichepetsa kuti uvomereze pamene mnzako akukupepesa komanso kuti umukhululukire.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Thetsa nkhani mofulumira.”​—Mateyu 5:25.

Kusunga zifukwa kungakudwalitseni komanso kukusokonezani maganizo. Kukhozanso kusokoneza kwambiri banja lanu.