Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulangiza mwana kuli ngati kuwongolera boti kuti lisalowere kolakwika

MAKOLO

6: Kulangiza

6: Kulangiza

ZIMENE ZIMACHITIKA

Mawu akuti kulangiza angatanthauzenso kutsogolera kapena kuphunzitsa. Nthawi zina mawuwa amanena za kudzudzula mwana akayamba kupulupudza. Koma nthawi zambiri, amanena za kuphunzitsa mwana makhalidwe abwino kuti azitha kusankha zinthu mwanzeru.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUGANIZIRA NKHANIYI N’KOFUNIKA?

Zaka zaposachedwapa, makolo ambiri asiya kulangiza ana poopa kuti akawadzudzula anawo angamadzione ngati osafunika. Komabe makolo oganiza bwino amaikira ana awo malamulo komanso kuwathandiza kutsatira malamulowo.

A Pamela ananena kuti: “Ana amafunika kuwauza zoti azichita ndi zomwe sakufunika kuchita kuti adzakhale anthu odalirika akadzakula. Ana omwe salangizidwa ndi makolo awo amakhala ngati sitima yopanda chiwongolero yomwe imangolowera kulikonse mpaka kuchita ngozi.”

ZIMENE MUNGACHITE

Musamasinthesinthe. Ngati mwana sakutsatira malamulo omwe munakhazikitsa, muzimpatsa chilango. Koma muzimuyamikira akamatsatira zomwe munamuuza.

A Christine ananena kuti: “Nthawi zambiri ndimayamikira ana anga chifukwa amandimvera. Zimandisangalatsa chifukwa masiku ano ana ambiri sachita zimenezi. Mwana amene mumamuyamikira, savutika kulandira malangizo akalakwitsa zinazake.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”​—Agalatiya 6:7.

Chilango chizigwirizana ndi msinkhu wa mwana. Mukamapereka chilango kwa mwana, muziganizira msinkhu wake, zomwe amakwanitsa kuchita komanso kukula kwa zomwe walakwitsazo. Mwachitsanzo, ngati sakugwiritsa ntchito bwino foni yake, mungamulande kuti asaigwiritsenso ntchito kwa kanthawi kapena mungamuletse kuchita zinthu zina pa foniyo. Komanso musaiwale kuti si bwino kukulitsa nkhani yaing’ono.

A Wendell ananena kuti: “Ndisanapereke chilango, ndimafunika kutsimikizira ngati mwanayo wachita zinthu mwadala kapena ngati kunali kulakwitsa chabe. Ngati akuchita zolakwikazo mobwerezabwereza angafunike kumpatsa chilango. Koma ngati kunangokhala kuganiza mwachibwana, ukhoza kungomulangiza basi.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Inu abambo, musamakwiyitse ana anu, kuti angakhale okhumudwa.”​—Akolose 3:21.

Muzisonyeza chikondi. Ana savutika kulandira chilango komanso kutsatira zomwe auzidwa akadziwa kuti bambo kapena mayi awo akuchita zimenezo chifukwa chowakonda.

A Daniel ananena kuti: “Mwana wathu akalakwitsa zinazake, tinkamuuza kuti timasangalala ndi zabwino zomwe amachita. Tinkamuuzanso kuti ngati sakonza zomwe walakwitsazo, akhoza kuwononga mbiri yake. Ndipo tinkamutsimikizira kuti ndife okonzeka kumuthandiza.”

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Chikondi n’choleza mtima ndiponso n’chokoma mtima.”​—1 Akorinto 13:4.