Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 5

Ana Amafunika Munthu Woti Aziwalangiza

Ana Amafunika Munthu Woti Aziwalangiza

ZINTHU ZINANSO ZOFUNIKA POLANGIZA ANA

Ana amafunika kulangizidwa ndi anthu achikulire. Monga makolo muyenera kuzindikira kuti muli ndi udindo wolangiza ana anu. Komabe pali anthu enanso achikulire omwe angakuthandizeni kulangiza anawo.

N’CHIFUKWA CHIYANI MALANGIZO A ACHIKULIRE ALI OFUNIKA?

M’mayiko ambiri ana sakhala ndi nthawi yokwanira yocheza ndi achikulire. Mwachitsanzo taganizirani izi:

  • Pafupifupi tsiku lonse ana amakhala ali kusukulu. Kusukuluko, anawo ndi amene amakhala ambiri kuposa aphunzitsi ndi anthu ena aakulu.

  • Akaweruka ambiri amabwerera kunyumba n’kukapeza kuti makolo onse adakali kuntchito.

  • Kafukufuku wina anasonyeza kuti ku United States kokha, ana a zaka zapakati pa 8 ndi 12 amatha maola 6 akuonera TV kapena kusewera magemu apakompyuta. *

Buku lina linati: “Ana ambiri masiku ano, m’malo mofunsira malangizo kwa amayi, abambo, aphunzitsi kapena anthu ena achikulire, . . . amakafunsa ana anzawo.”​—Hold On to Your Kids.

MUNGATHANDIZE BWANJI ANA ANU KUTI AZIMVERA MALANGIZO?

Muzicheza nawo.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Phunzitsa mwana m’njira yomuyenerera. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.”​—Miyambo 22:6.

Mwachibadwa ana amafuna kuti makolo awo aziwapatsa malangizo komanso kuwathandiza. Moti akatswiri ena amanena kuti ana a zaka 13 mpaka 19, amaonabe kuti malangizo a makolo awo ndi abwino poyerekeza ndi amene anzawo angawapatse. Dr. Laurence Steinberg analemba m’buku lina kuti: “Ana amaonabe kuti malangizo a makolo awo ndi ofunika ngakhale pamene afika potha msinkhu. Iwo amafuna kumva maganizo a makolo awo ngakhale kuti nthawi zambiri sangagwirizane ndi zimene makolowo akunena.”​—You and Your Adolescent.

Choncho popeza mwachibadwa ana amafuna kumva maganizo a makolo awo, mungachite bwino kumawapatsa malangizo pamsinkhu umenewu. Muzipeza nthawi yocheza nawo n’kumawauza mmene mumamvera, zinthu zimene mumaziona kuti n’zofunika kutsatira komanso zimene mwaphunzira pamoyo wanu.

Apezereni munthu wodalirika kuti aziwathandiza.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.”​—Miyambo 13:20.

Kodi pali munthu wina wodalirika amene mukuona kuti angakhale chitsanzo chabwino kwa mwana wanu? Mungamupemphe kuti azicheza ndi mwana wanuyo. Koma simuyenera kumusiyira udindo woti akhale ngati kholo lake. Malangizo a munthu wachikulire amene mwamudalira, angakhale ofunika pamene mukuphunzitsa mwana wanuyo. M’Baibulo muli chitsanzo cha Timoteyo, yemwe ngakhale atakula anapitirizabe kupindula ndi malangizo amene Paulo ankamupatsa. Ndipo nayenso Paulo anapindula kwambiri chifukwa chochita zinthu limodzi ndi Timoteyo.​—Afilipi 2:20, 22.

Masiku ano, mabanja ambiri amakhala kutali ndi achibale awo. Izi zimachititsa kuti ana asazolowerane ndi agogo, amalume, azakhali ndi achibale awo ena. Ngati umu ndi mmenenso zilili ndi inuyo, mungachite bwino kupeza munthu wachikulire wodalirika amene ali ndi makhalidwe amene mumafuna kuti ana anu aphunzire.

^ ndime 9 Kafukufukuyu anasonyezanso kuti ana a zaka zapakati pa 13 ndi 19, amatha maola pafupifupi 9 tsiku lililonse akuonera TV komanso kusewera magemu apakompyuta. Nthawiyi siikuphatikizapo nthawi imene amagwiritsa ntchito intaneti pofufuza zinthu kusukulu kapena akamalemba homuweki.