Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

PHUNZIRO 2

Muziwaphunzitsa Kukhala Odzichepetsa

Muziwaphunzitsa Kukhala Odzichepetsa

KODI MUNTHU WODZICHEPETSA AMATANI?

Munthu wodzichepetsa amakhala waulemu, samachita zinthu modzikuza ndipo samayembekezera kuti ena azimuona kuti ndi wofunika kwambiri. Komanso amachita chidwi ndi ena ndipo amaona kuti akhoza kuphunzira zinthu zina kuchokera kwa iwo.

Anthu ena amaona kuti munthu wodzichepetsa ndi wofooka, koma zimenezi si zoona. Kudzichepetsa kumathandiza munthu kuzindikira zimene amalephera komanso zomwe sangakwanitse kuchita.

N’CHIFUKWA CHIYANI KUDZICHEPETSA N’KOFUNIKA?

  • Kumathandiza kuti munthu azigwirizana ndi ena. Buku lina limanena kuti: “Anthu ambiri odzichepetsa savutika kupeza anzawo.” Bukuli limanenanso kuti “anthu amenewa savutika kuchita zinthu ndi anthu ena.”​—The Narcissism Epidemic.

  • Kudzichepetsa kungadzathandize mwana wanu m’tsogolo. Ngati mwana wanu ataphunzira kukhala wodzichepetsa panopo, sangadzavutike kupeza ntchito. Dr. Leonard Sax analemba m’buku lake lina kuti: “Mwana amene ndi wodzimva komanso amene sadziwa zofooka zake, sangatengedwe akamafunsira ntchito. Koma mwana wodzichepetsa amamvetsera mwachidwi zimene omulemba ntchito akufuna ndipo savutika kupeza ntchito.” *

MUNGAPHUNZITSE BWANJI ANA ANU KUKHALA ODZICHEPETSA?

Muziwathandiza kuti azidziona moyenerera.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotero, akudzinyenga.”​—Agalatiya 6:3.

  • Musamawauze zinthu zomwe sizingatheke. Makolo ena amakonda kuuza ana awo kuti: “Zonse zimene umafuna zidzatheka” kapena akuti “Ukhoza kukhala chilichonse chimene ukufuna.” koma nthawi zambiri amenewa amangokhala maloto chabe. Ana anu akhoza kudzachita bwino ngati atakhala ndi zolinga zoyenerera n’kuyesetsa kuchita khama kuti azikwaniritse.

  • Mukamawayamikira muzitchula zimene achita bwino. Kungouza mwana wanu kuti “ndiwe mwana wabwino” sikungamuthandize kuti akhale wodzichepetsa. Mumafunika kutchula chinthu chimene wachita bwinocho.

  • Asamangokhalira kucheza ndi anthu pa intaneti. Nthawi zambiri anthu akamacheza pa intaneti amakonda kuuza anzawo za luso lawo komanso zomwe achita. Koma izi sizingathandize munthu kukhala wodzichepetsa.

  • Muziwalimbikitsa kuti azipepesa mwansanga akalakwitsa zinazake. Muziphunzitsa ana anu kudziwa zimene alakwitsa n’kuvomereza zolakwa zawo.

Muziwalimbikitsa kuti aziyamikira.

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.”​—Akolose 3:15.

  • Aziyamikira zachilengedwe. Ana ayenera kumayamikira chilengedwe chifukwa chimatithandiza kuti tikhale ndi moyo. Timafunika mpweya, madzi komanso chakudya. Muziwafotokozera kufunika kwa zinthuzi kuti muwathandize kuchita chidwi komanso kuyamikira zinthu zodabwitsa zimene zili m’chilengedwe.

  • Aziona ena kukhala owaposa. Muzimuthandiza kudziwa kuti munthu aliyense amamuposa m’njira inayake. Choncho m’malo moti azichita nsanje munthu wina akachita bwino, muzimuthandiza kuona kuti akhoza kuphunzira zinazake kwa munthuyo.

  • Aziyamikira ena. Muzimuphunzitsa kunena kuti zikomo wina akamuchitira zabwino ndipo azichita zimenezi kuchokera pansi pa mtima. Kuyamikira zimene ena achita kumathandiza kuti munthu akhale wodzichepetsa.

Muziwaphunzitsa kufunika kothandiza ena.

MFUNDO YA M’BAIBULO: ‘Modzichepetsa, muziona ena kukhala okuposani. Musamaganizire zofuna zanu zokha, koma muziganiziranso zofuna za ena.’​—Afilipi 2:3, 4.

  • Muziwaphunzitsa ntchito zapakhomo. Mukamapewa kupatsa mwana wanu ntchito zapakhomo mumakhala ngati mukumuuza kuti ‘ndiwe wofunika kwambiri, sukufunika kugwira ntchito ngati zimenezi.’ Choncho muzimuthandiza kudziwa kuti kugwira ntchito zapakhomo n’kofunika kwambiri kuposa kusewera. Mungachitenso bwino kumufotokozera kuti kugwira ntchitozi kumathandiza anthu ena komanso kumachititsa kuti ena azikuyamikira ndiponso kukulemekeza.

  • Muziwathandiza kudziwa kuti kuthandiza ena n’kofunika. Mwana akamathandiza ena amaphunzira kuchita zinthu ngati munthu wamkulu. Choncho muzimuthandiza kuona mmene angadziwire anthu amene akufunika thandizo. Kenako muzikambirana naye zimene angachite kuti awathandize. Nthawi zonse muzimuyamikira komanso kumuthandiza akamafuna kuthandiza ena.

^ ndime 8 Kuchokera m’buku lakuti The Collapse of Parenting.