Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu

Kukhala pa Ubwenzi ndi Mulungu

Nkhani yoyamba ija, inasonyeza kuti anthu ambiri amaona kuti Baibulo ndi buku lothandiza pa nkhani zachipembedzo. Amaona kuti akamawerenga Baibulo komanso kutsatira mfundo zake, amamvetsa cholinga cha moyo komanso amakhala anthu auzimu.

Baibulo likamanena za munthu “wauzimu” limakhala likutanthauza munthu amene amaona kuti kulambira Mulungu n’kofunika pamoyo wake. (Yuda 18, 19) Mosiyana ndi munthu wakuthupi, yemwe amangochita zinthu zimene akufuna, anthu auzimu amaona kuti kutsatira mfundo za Mulungu ndi kofunika kwambiri.​—Aefeso 5:1.

CHIYEMBEKEZO

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zochepa.”—Miyambo 24:10.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Zinthu zofooketsa zingatilepheretse kulimbana ndi mavuto. Koma tikakhala ndi chiyembekezo, timapezanso mphamvu. Zimakhala zolimbikitsa kudziwa kuti mavuto amene timakumana nawo ndi a kanthawi komanso kuti nthawi zina tikhoza kuphunzirapo kanthu pa mavutowo.

ZIMENE MUNGACHITE: Muziganizira zinthu zabwino zimene zikubwera m’tsogolo. M’malo modera nkhawa za mavuto amene mungakumane nawo kapena kungokhala n’kumadikirira kuti zinthu zidzayamba kuyenda bwino, muzichita khama kuti mukwaniritse zolinga zanu. Komabe ngakhale titachita zimenezi, nthawi zina tikhoza kukumana ndi “zinthu zosayembekezereka.” (Mlaliki 9:11) Nthawi zinanso zinthu zimatha kusintha n’kuyamba kuyenda bwino mosiyana ndi mmene timaganizira. N’chifukwa chake Baibulo limatiuza kuti: “Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo, chifukwa sukudziwa pamene padzachite bwino, kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzachite bwino.”​—Mlaliki 11:6.

MAYANKHO A MAFUNSO OFUNIKA KWAMBIRI

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Ndithandizeni kukhala wozindikira . . . Mawu anu onse ndi choonadi.”​—Salimo 119:144, 160.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Baibulo limapereka mayankho a mafunso amene anthu ambiri amadzifunsa. Mwachitsanzo, lingatithandize kupeza mayankho a mafunso ngati awa:

  • Kodi tinachokera kuti?

  • N’chifukwa chiyani tili ndi moyo?

  • Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

  • Kodi moyo ndi wokhawu umene ulipo, kapena palinso wina?

Moyo wa anthu ambiri padzikoli wasintha kwambiri atapeza mayankho a mafunso amenewa komanso ena kuchokera m’Baibulo.

ZIMENE MUNGACHITE: Fufuzani nokha kuti mudziwe zimene Baibulo limaphunzitsa. Mukhozanso kufunsa wa Mboni za Yehova kuti akuthandizeni kumvetsa zimene Baibulo limanena. Komanso mungathe kupita pawebusaiti yathu ya jw.org, kapena kupita kumisonkhano yathu. Misonkhanoyi imakhala yaulere ndipo aliyense akhoza kupitako.

MFUNDO ZINA ZA M’BAIBULO

Onerani vidiyo yakuti N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? Vidiyoyi ikupezeka m’zinenero zoposa 880

MUZIZINDIKIRA ZOSOWA ZANU ZAUZIMU.

“Odala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.”​—MATEYU 5:3.

MUZIPHUNZIRA BAIBULO KUTI MUDZIWE ZAMBIRI ZOKHUDZA MULUNGU.

“Anachita zimenezi kuti anthuwo afunefune Mulungu, amufufuzefufuze ndi kumupezadi, . . . iye sali kutali ndi aliyense wa ife.”​—MACHITIDWE 17:27.

MUZIWERENGA BAIBULO KOMANSO KUGANIZIRA ZIMENE MWAWERENGAZO.

“Amakondwera ndi chilamulo cha Yehova, * ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku. . . . ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.”​—SALIMO 1:2, 3.

^ ndime 23 Yehova ndi dzina la Mulungu ndipo limapezeka m’Baibulo.