Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Baibulo Limanena?

Zimene Baibulo Limanena?

Kodi Mdyerekezi ndi ndani?

KODI MUNGAYANKHE KUTI Mdyerekezi ndi . . .

  • Mngelo?

  • Maganizo oipa a mumtima mwa munthu?

  • Munthu wongoyerekezera?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

Nthawi ina Mdyerekezi analankhulapo ndi Yesu ndipo ‘anamuyesa.’ (Mateyu 4:1-4) Choncho Mdyerekezi si munthu wongoyerekezera kapenanso maganizo oipa amene amakhala mumtima mwa munthu. Iye ndi mngelo woipa.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Poyamba Mdyerekezi anali mngelo wabwinobwino koma kungoti “sanakhazikike m’choonadi.” (Yohane 8:44) Kenako anakhala wabodza ndiponso anaukira Mulungu.

  • Angelo enanso anakhala kumbali ya Satana poukira Mulungu.​—Chivumbulutso 12:9.

  • Mdyerekezi amachititsa anthu ambiri kuganiza kuti iye kulibeko.​—2 Akorinto 4:4.

Kodi Mdyerekezi angalamulire zochita za anthu?

ANTHU ENA AMAKHULUPIRIRA kuti n’zosatheka kulamuliridwa ndi Mdyerekezi, pomwe ena amachita mantha kwambiri kuti akhoza kugwidwa ndi mizimu yoipa. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO LIMANENA

“Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Mdyerekezi amalamulira kwambiri zochita za anthu, koma sikuti amalamulira zochita za munthu aliyense.

MFUNDO ZINANSO ZOMWE TIKUPHUNZIRA M’BAIBULO

  • Mdyerekezi amagwiritsa ntchito chinyengo pofuna kupusitsa anthu.​—2 Akorinto 11:14.

  • Nthawi zina mizimu yoipa ikhoza kulamulira zochita za anthu.​—Mateyu 12:22.

  • Mulungu angakuthandizeni ‘kutsutsa Mdyerekezi.’​—Yakobo 4:7.