Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi cholinga cha kubweranso kwa Yesu n’chiyani?

Yesu asanakwere kumwamba mu 33 C.E., analonjeza otsatira ake kuti adzabweranso. Anadziyerekezera ndi munthu wa m’banja lachifumu amene anapita kudziko lakutali, ndipo patapita nthawi anabweranso atakhala mfumu. Choncho cholinga cha kubweranso kwa Yesu, ndi kudzakhazikitsa ulamuliro wabwino kwa anthu.—Werengani Luka 19:11, 12.

Yesu adzabweretsa ulamuliro wabwino padzikoli

Kodi Yesu adzabweranso ndi thupi ngati la munthu? Kumbukirani kuti iye anaukitsidwa ndi thupi lauzimu. (1 Petulo 3:18) Kenako anapita kumwamba ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu. (Salimo 110:1) Patapita nthawi yaitali, Yesu anafika pafupi ndi “Wamasiku Ambiri,” yemwe ndi Yehova Mulungu, ndipo anam’patsa mphamvu zolamulira anthu. Choncho Yesu adzabwera, osati ngati munthu, koma monga Mfumu yosaoneka.—Werengani Danieli 7:13, 14.

Kodi Yesu akadzabweranso adzachita chiyani?

Yesu akadzabweranso ndi angelo ake mosaoneka, adzaweruza anthu. Adzawononga anthu oipa, koma anthu amene amam’mvera monga Mfumu yawo, adzawapatsa moyo wosatha.—Werengani Mateyu 25:31-33, 46.

Ulamuliro wa Yesu udzasintha dzikoli kukhala paradaiso. Komanso iye adzaukitsa anthu amene anamwalira kuti asangalale ndi moyo m’Paradaiso padziko lapansili.—Werengani Luka 23:42, 43.