Kalata Yoyamba ya Petulo 3:1-22

  • Akazi komanso amuna apabanja (1-7)

  • Muzimverana chisoni; muziyesetsa kumakhala mwamtendere (8-12)

  • Kuvutika chifukwa chochita zinthu mwachilungamo (13-22)

    • Muzikhala okonzeka kufotokoza za chiyembekezo chanu (15)

    • Ubatizo komanso chikumbumtima chabwino (21)

3  Mofanana ndi zimenezi, inu akazi muzigonjera amuna anu+ kuti ngati safuna kumvera Mawu a Mulungu, akopeke ndi khalidwe lanu, osati ndi mawu anu+  koma chifukwa choti aona khalidwe lanu labwino*+ komanso ulemu wanu waukulu.  Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa kunja kokha monga kumanga tsitsi, kuvala zodzikongoletsera zagolide+ kapena zovala zapamwamba.  Koma kukhalenso kwa munthu wobisika mumtima, atavala zovala zosawonongeka, zomwe ndi mtima wodekha komanso wofatsa+ umene ndi wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.  Ndi mmenenso akazi okhulupirika akale, omwe ankayembekezera Mulungu, ankadzikongoletsera. Akazi amenewa ankagonjera amuna awo.  Mwachitsanzo, Sara ankamvera Abulahamu ndipo ankamutchula kuti “mbuyanga.”+ Tsopano inuyo mwakhala ana ake, ndipo mukhalabe ana ake mukapitiriza kuchita zabwino komanso ngati simukuopa chilichonse.+  Inunso amuna, pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino. Muziwapatsa ulemu+ chifukwa akazi ali ngati chiwiya chosachedwa kusweka. Muzichita zimenezi kuti mapemphero anu asatsekerezedwe, chifukwa mudzalandira nawo limodzi moyo umene Mulungu adzakupatseni+ chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.  Pomaliza, nonsenu mukhale amaganizo amodzi,+ muzimverana chisoni, muzikonda abale, mukhale ndi chifundo chachikulu+ ndiponso mukhale odzichepetsa.+  Munthu akakuchitirani choipa musamabwezere ndi choipa,+ akakuchitirani chipongwe musamabwezere ndi chipongwe.+ Mʼmalomwake muziwachitira zabwino*+ chifukwa Mulungu anakusankhani kuti muzidalitsa ena kuti nayenso adzakudalitseni. 10  Munthu “amene amakonda moyo wake komanso amafuna kumakhala moyo wabwino, ayenera kusamala kuti asamalankhule zoipa ndi lilime lake+ ndiponso kuti asamalankhule zachinyengo ndi milomo yake. 11  Ayenera kusiya kuchita zoipa+ nʼkumachita zabwino.+ Ayeneranso kuyesetsa kumakhala mwamtendere ndi ena komanso kuulimbikitsa.+ 12  Maso a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva mapemphero awo opembedzera,+ koma Yehova* amakwiyira anthu amene amachita zoipa.”+ 13  Ndithudi, ndi ndani angakuchitireni zoipa mukamayesetsa kuchita zabwino?+ 14  Koma ngakhale mutavutika chifukwa chochita zinthu mwachilungamo, mumakhalabe osangalala.+ Musamaope zimene amaopa* ndipo musamade nazo nkhawa.+ 15  Koma muvomereze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera. Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu, koma muziwayankha mofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.+ 16  Muzikhala ndi chikumbumtima chabwino,+ kuti kaya anthu akunenereni zoipa, amene akukunenerani zoipawo adzachite manyazi+ chifukwa cha khalidwe lanu labwino monga otsatira a Khristu.+ 17  Ndi bwino kuvutika chifukwa chochita zabwino,+ ngati Mulungu walola kuti zimenezo zichitike, kusiyana ndi kuvutika chifukwa chochita zoipa.+ 18  Pajatu ngakhale Khristu anafa kamodzi kokha kuti achotse uchimo.+ Munthu wolungamayo anafera anthu osalungama+ kuti akugwirizanitseni ndi Mulungu.+ Iye anaphedwa monga munthu,*+ koma anaukitsidwa monga mzimu.+ 19  Kenako anapita kukalengeza uthenga wachiweruzo* kwa mizimu imene inali mʼndende.+ 20  Mizimuyi sinamvere Mulungu pa nthawi imene ankaleza mtima mʼmasiku a Nowa.+ Pa nthawiyo, Nowa ankapanga chingalawa+ chomwe chinapulumutsa pamadzi anthu owerengeka, anthu* 8 okha basi.+ 21  Tsopano ubatizo, womwe ukufanana ndi chingalawa, ukupulumutsanso inuyo (osati kungochotsa litsiro lamʼthupi, koma kupempha Mulungu kuti akupatseni chikumbumtima chabwino)+ chifukwa mumakhulupirira Yesu Khristu yemwe anaukitsidwa. 22  Iye anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu+ moti anamukweza kuti maulamuliro, mphamvu komanso angelo zikhale pansi pake.+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “loyera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mʼmalomwake muziwadalitsa.”
Mabaibulo ena amati, “Musamaope akamakuopsezani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Iye anaphedwa mʼthupi.”
Kapena kuti, “Kenako anapita kukalalikira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “miyoyo.”