NSANJA YA OLONDA February 2014 | Nkhondo Yomwe Inasintha Dziko Lonse

N’chifukwa chiyani nkhondo yoyamba ya padziko lonse inasintha kwambiri dziko? Kodi yankho la funso limeneli limatithandiza kudziwa chiyani zokhudza tsogolo ladzikoli?

NKHANI YAPACHIKUTO

Nkhondo Yomwe Inasintha Dziko Lonse

Kodi nkhondo yoyamba ya padziko lonse, yomwe inkatchedwanso kuti “Nkhondo Yaikulu,” inasintha bwanji dziko lonse m’njira zoti zimatikhudzanso ifeyo?

NKHANI YAPACHIKUTO

Kodi Ndani Amachititsa Nkhondo Komanso Mavuto Ena Padzikoli?

Kodi Baibulo limati pali kugwirizana kotani pakati pa nkhondo imene inachitika kumwamba ndi nkhondo ya padziko lonse?

BAIBULO LIMASINTHA ANTHU

Lonjezo la Paradaiso Linasintha Moyo Wanga

Ivars Vigulis anali katswiri wa mpikisano woyendetsa njinga yamoto. Kodi ataphunzira Baibulo anayamba kuiona bwanji ntchito yakeyi?

Kodi Mukudziwa?

Kodi aloye amene ankagwiritsidwa ntchito kale anali chiyani? Kodi ndi nsembe zotani zimene zinali zovomerezeka pakachisi ku Yerusalemu?

ZIMENE OWERENGA AMAFUNSA

N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Anthu Osauka Aziponderezedwa?

Baibulo limanena zimene Mulungu amachita pa nkhani ya kuponderezana komanso zimene adzachite m’tsogolo.

TSANZIRANI CHIKHULUPIRIRO CHAWO

Anakhalabe Wokhulupirika Ngakhale Kuti Ena Ankachita Zinthu Zopanda Chilungamo

Kodi inuyo munayamba mwachitiridwapo zinthu zopanda chilungamo? Kodi mumafuna Mulungu atathetsa zinthu zopanda chilungamo? Werengani nkhaniyi kuti muone mmene mungatsanzirire chikhulupiriro cha Eliya.

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi pali umboni wosonyeza kuti Baibulo ndi lochokera kwa Mulungu? Kodi linalembedwa bwanji?

Zina zimene zili pawebusaiti

N’chifukwa Chiyani Mtendere Ndi Wosowa M’dzikoli?

Anthu alephera kubweretsa mtendere. Taonani zifukwa zingapo zimene zikuchititsa kuti anthu azilephera kubweretsa mtendere.