Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | NKHONDO YOMWE INASINTHA DZIKO LONSE

Kodi Ndani Amachititsa Nkhondo Komanso Mavuto Ena Padzikoli?

Kodi Ndani Amachititsa Nkhondo Komanso Mavuto Ena Padzikoli?

Nkhondo yoyamba ya padziko lonse inatha pa November 11, 1918. Anthu anasiya ntchito zawo n’kumavina m’misewu chifukwa chosangalala. Koma chisangalalo chimenechi sichinakhalitse chifukwa pasanapite nthawi, kunagwanso vuto lina lalikulu kwambiri kuposa nkhondoyo.

Mliri wa chimfine choopsa unali utayambika kumalo omenyera nkhondo a ku France mu June 1918. Anthu ambiri anayamba kufa ndi mliriwu. Mwachitsanzo m’miyezi yochepa yokha, mliriwu unapha asilikali a ku America amene anali ku France ambiri zedi kuposa anthu amene anaphedwa pa nkhondoyo. Asilikali amene anabwerera kwawo nkhondoyi itatha, anali ndi matendawa ndipo izi zinapangitsa kuti matendawa afalikire m’mayiko ambiri m’kanthawi kochepa.

Komanso nkhondoyi itatha, m’mayiko ambiri munali njala ndi mavuto azachuma. Mwachitsanzo patapita zaka zingapo nkhondoyi itatha, anthu a m’mayiko ambiri a ku Ulaya ankavutikabe ndi njala. Pomafika mu 1923, ndalama ya ku German inali itatheratu mphamvu. Patangotha zaka 6, chuma cha padziko lonse chinalowa pansi kwambiri. Mu 1939, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inayambika ndipo nkhondoyi inangokhala ngati ikupitiriza nkhondo yoyamba ija. Kodi n’chiyani chinapangitsa mavuto onsewa?

CHIZINDIKIRO CHA MASIKU OTSIRIZA

Maulosi a m’Baibulo amatithandiza kudziwa chimene chinapangitsa mavutowa, makamaka nkhondo yoyamba ya padziko lonse. Yesu Khristu ananeneratu za nthawi pamene “mtundu udzaukirana ndi mtundu wina.” Ananenanso kuti kudzakhala njala komanso miliri yambiri. (Mateyu 24:3, 7; Luka 21:10, 11) Iye anauza ophunzira ake kuti mavuto amenewa adzakhala chizindikiro cha masiku otsiriza. Zambiri zafotokozedwa m’buku la  Chivumbulutso, lomwe limasonyeza kuti pali kugwirizana pakati pa mavuto a padzikoli ndi nkhondo imene inachitika kumwamba.—Onani bokosi lakuti  “Nkhondo Yapadziko Lapansi Ndiponso Nkhondo Yakumwamba.”

Buku la Chivumbulutso limatchulanso za anthu 4 okwera pamahatchi. Atatu a anthu amenewa akuimira nkhondo, njala komanso miliri zimene Yesu analosera zija. (Onani bokosi lakuti,  “Kodi Ulosi wa Okwera Pamahatchi 4 Ukukwaniritsidwadi?”) Choncho n’zodziwikiratu kuti mavuto amene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayambitsa akupitirirabe. Ndipotu Baibulo limasonyeza kuti Satana ndi amene anapangitsa kuti nkhondo imeneyi ichitike. (1 Yohane 5:19) Kodi iye adzapitirizabe kuyambitsa mavuto padzikoli?

Buku la m’Baibulo la Chivumbulutso limatiuza kuti Satana “wangotsala ndi kanthawi kochepa.” (Chivumbulutso 12:12) N’chifukwa chake Satana ndi wokwiya kwambiri ndipo akubweretsa mavuto osaneneka padzikoli. Choncho mavuto amene akuchitika padzikoli ndi umboninso wakuti Satana watsala ndi nthawi yochepa.

NTCHITO ZA MDYEREKEZI ZIWONONGEDWA POSACHEDWAPA

Ndithudi nkhondo yoyamba ya padziko lonse inasintha zinthu kwambiri padzikoli. Inachititsa kuti mayiko ambiri  amenye nkhondo, anthu aukire maboma awo komanso kuti anthu asiye kukhulupirira atsogoleri awo. Komanso nkhondoyi ndi umboni wakuti Satana anathamangitsidwa kumwamba. (Chivumbulutso 12:9) Wolamulira wosaoneka wa dziko ameneyu, anachita zinthu ngati wolamulira wolusa amene akudziwa kuti nthawi yake yoti alamulire yatsala pang’ono kutha. Nthawi yakeyo ikadzatha, mavuto onse amene nkhondo yoyamba ya padziko lonse inabweretsa adzatha.

Maulosi a m’Baibulo angakuthandizeni kukhulupirira kuti posachedwapa Yesu Khristu, yemwe ndi Mfumu ya kumwamba, ‘adzawononga ntchito za Mdyerekezi.’ (1 Yohane 3:8) Pali anthu ambiri amene amapemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere. Kodi inunso mumapemphera kuti Ufumuwu ubwere? Ufumu umenewu ndi umene udzathandize kuti chifuniro cha Mulungu, osati cha Satana, chichitike padzikoli. (Mateyu 6:9, 10) Ufumu wa Mulungu ukamadzalamulira padzikoli, sipadzachitikanso nkhondo ya padziko lonse, kapena nkhondo iliyonse. (Salimo 46:9) Tikukupemphani kuti muphunzire zambiri zokhudza Ufumu umenewu kuti mudzakhalepo pamene uzidzalamulira. Pa nthawi imeneyo padziko lonse padzakhala mtendere.—Yesaya 9:6, 7.