Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 12

Yehova Mulungu Wamkulu

Yehova Mulungu Wamkulu

(Ekisodo 34:​6, 7)

  1. 1. Inu Yehova M’lungu Wamkulu,

    Wabwino m’zinthu zonse,

    Tizikutamandani.

    Muli ndi mphamvu, chikondi, nzeru.

    Mulungu wathu ndinu.

  2. 2. Tikumaona chifundo chanu.

    Ngakhale ndife fumbi

    Tikapempha mumamva.

    Mumatidyetsa, kutiphunzitsa,

    Mumatithandizadi.

  3. 3. Tikutamanda inu Yehova.

    Tikukuimbirani

    Mosangalala ndithu.

    Muyeneradi kutamandidwa

    Kuchokera mumtima.