Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 13

Titsanzire Yesu

Titsanzire Yesu

(1 Petulo 2:​21)

  1. 1. Yehova Mulungu

    Anatikondadi,

    Anapereka Yesu monga dipo.

    Yesu analola

    Kudzakhala munthu.

    Anayeretsa dzina la M’lungu.

  2. 2. Yesu ankakonda

    Mawu a Mulungu.

    Ndi amene ankamupatsa nzeru.

    Ankatumikira

    Mokhulupirika

    Ndipo anasangalatsa M’lungu.

  3. 3. Titsanzire

    Yesu Potamanda M’lungu

    Komanso muzochita zathu zonse.

    Tizimutsanzira

    M’moyo wathu wonse

    Ndipo tizisangalatsa M’lungu.