Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 134

Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

Ana Ndi Mphatso Yochokera kwa Mulungu

(Salimo 127:​3-5)

  1. 1. Mwamuna ndi mkazi wake

    Akalandira mphatso ya mwana,

    Ayenera kukumbukira

    Mwanayo si wawo okha.

    Ndi mphatso yochoka kwa M’lungu.

    Amapatsa chikondi ndi moyo.

    Amapereka malangizo

    Othandizadi kwa makolo.

    (KOLASI)

    Mphatsoyi ndi yopatulika

    Ndipo muisamalire.

    Muphunzitseni choonadi

    Ndipo mudzamuthandiza.

  2. 2. Mawu onse a Mulungu

    Azikhalatu mumtima mwanu.

    Muziuzanso ana anu,

    Uwu ndi udindo wanu.

    Muziwaphunzitsa poyenda,

    Podzuka ndi pa nthawi yopuma.

    Akamakula saiwala.

    Azilandira madalitso.

    (KOLASI)

    Mphatsoyi ndi yopatulika

    Ndipo muisamalire.

    Muphunzitseni choonadi

    Ndipo mudzamuthandiza.