Kalata Yoyamba Yopita kwa Timoteyo 4:1-16

  • Chenjezo lokhudza zomwe ziwanda zimaphunzitsa (1-5)

  • Kukhala mtumiki wabwino wa Khristu (6-10)

    • Kulimbitsa thupi ndiponso kudzipereka kwa Mulungu (8)

  • Uzisamala ndi zimene umaphunzitsa (11-16)

4  Komabe mawu ouziridwa amanena momveka bwino kuti nthawi ina mʼtsogolo, chikhulupiriro cha anthu ena chidzatha chifukwa chomvetsera mawu ouziridwa omwe ndi osocheretsa,+ ndiponso zinthu zimene ziwanda zimaphunzitsa.  Zimenezi zidzachitikanso chifukwa cha chinyengo cha anthu olankhula mabodza,+ amene chikumbumtima chawo chili ngati chipsera chobwera chifukwa chopsa ndi chitsulo chamoto.  Anthuwa amaletsa kukwatira,+ ndipo amalamula anthu kuti azisala zakudya+ zimene Mulungu anazilenga kuti anthu amene ali ndi chikhulupiriro+ ndiponso odziwa choonadi molondola azidya+ nʼkuyamikira Mulungu.  Chifukwa chilichonse cholengedwa ndi Mulungu nʼchabwino,+ ndipo palibe chimene chiyenera kukanidwa+ ngati munthu wayamika Mulungu pakudya,  popeza chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndiponso pemphero.  Ukamapereka malangizowa kwa abale, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu. Ndipo udzakula bwino ndi mawu a chikhulupiriro ndiponso chiphunzitso chabwino chimene wachitsatira mosamala.+  Koma uzipewa nkhani zonama zosalemekeza Mulungu+ ngati zimene amayi ena okalamba amakamba. Mʼmalomwake, uzidziphunzitsa nʼcholinga choti ukhalebe wodzipereka kwa Mulungu.  Chifukwa kuchita masewera olimbitsa thupi ndi kothandiza pangʼono, koma kukhala wodzipereka kwa Mulungu ndi kothandiza pa zinthu zonse, chifukwa kumakhudza lonjezo la moyo wathu panopa ndi moyo umene ukubwerawo.+  Mawu amenewa ndi oona ndipo ndi oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse. 10  Nʼchifukwa chake tikugwira ntchito mwakhama ndiponso mwamphamvu,+ chifukwa chiyembekezo chathu chili mwa Mulungu wamoyo, amene ndi Mpulumutsi+ wa anthu onse, koma makamaka okhulupirika.+ 11  Pitiriza kuwaphunzitsa ndi kuwalamula kuti azichita zimenezi. 12  Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamngʼono. Mʼmalomwake, ukhale chitsanzo kwa okhulupirika pa zimene umalankhula, makhalidwe ako, chikondi, chikhulupiriro ndi khalidwe loyera. 13  Pamene ukundiyembekezera, pitiriza kukhala wodzipereka powerenga pagulu,+ polimbikitsa* anthu ndiponso pophunzitsa. 14  Usamanyalanyaze mphatso yomwe unapatsidwa mwaulosi pamene bungwe la akulu linaika manja pa iwe.+ 15  Uziganizira mozama* zinthu zimenezi ndipo uzizichita modzipereka kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo. 16  Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.+ Pitiriza kuchita zimenezi, chifukwa ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “podandaulira.”
Kapena kuti, “Uzisinkhasinkha.”