Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

NYIMBO 36

Titeteze Mtima Wathu

Titeteze Mtima Wathu

(Miyambo 4:23)

  1. 1. Titeteze mtima wathu

    Tikhale ndi moyo.

    M’lungu amadziwa bwino

    Za mumtima mwathu.

    Mtima ndi wonyenga

    Ungamatisocheretse.

    Choncho tiganize bwino

    Timvere Yehova.

  2. 2. Timafunafuna M’lungu

    Tikamapemphera.

    Timathokozadi zonse

    Zomwe amachita.

    Zomwe amatiphunzitsa

    Timazitsatira

    Ndipo tikhulupirike,

    Timusangalatse.

  3. 3. Titeteze mtima wathu

    Tipewe zoipa.

    Mawu a Yehova M’lungu

    Atitsogolere.

    Anthu okhulupirika

    Amawakondadi.

    Choncho tizimulambira

    Monga bwenzi lathu.