Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndasangalala Kuti Sindinagonje

Ndasangalala Kuti Sindinagonje

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Pamakhala mayesero

    Ena tsiku ndi tsiku​—tsiku ndii tsiku.

    Sindingadziwiretudi,

    Koma mulimonsemo, ndingapeze njira.

    Ndikalimba ndidzapirira.

    Ndizikonzekereratu​​—

    Zochita ndi zonena

    Chiyeso chikafika.

    Pena kwa ine n’zovuta.

    Ndizipemphera kwa M’lungu.

    (KOLASI)

    Nipempha n’sagonje

    Ndipirire chiyeso.

    Ndipempha n’sagonje

    Ndikhulupirikebe.

  2. 2. Ndikozanso kukopeka

    N’kucheza ndi oipa​—zingachitike.

    Pena ndingaone ena

    Akuchita zoipa​—zinthu zoipa.

    Kutengekanso maganizo

    Ndi anthu osayenera.

    M’pomwe ndimakumbuka

    Ndisachite zoipa.

    Ndidzakhulupirikabe

    Palibe choti ndiope.

    (KOLASI)

    Ndasangalalatu,

    Kuti sindinagonje.

    Ndasangalalatu,

    Ndakhulupirika.