Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Ndingapite Kwa Ndani?

Ndingapite Kwa Ndani?

Pangani Dawunilodi:

  1. 1. Ndimamveratu Yesu,

    Ngakhale zivute.

    Samandisiya.

    Amandithandiza.

    Ndi m’busa wabwino

    Amakhala nane,

    Amandipatsa,

    Nzeru zabwinodi.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Ndimuthokoze bwanji?

    Ndisamvere otsutsawa.

    Samvera Yehova

    Angandisocheretse.

    (KOLASI)

    Ndingapite kwa ndani?

    Angandithandize ndi ndani?

    Ndingapite kwa ndani?

    Mzimu wa dzikoli,

    Umasocheretsa.

    Ndizimvera mawu a Yesu.

  2. 2. Pano ndilibe nkhawa

    Yesu ali nane,

    Abale anga,

    Amandikondanso.

    Posachedwa pompa,

    M’dziko latsopano

    M’lungu atipatsa

    Moyo wosatha.

    (KUKONZEKERA KOLASI)

    Ndim’thokoze bwanji?

    Ndisamvere otsutsawa.

    Chida chilichonse

    Sichidzapambanadi.

    (KOLASI)

    Ndingapite kwa ndani?

    Angandithandize ndi ndani?

    Ndingapite kwa ndani?

    Mzimu wa dzikoli,

    Umasocheretsa

    Ndizimvera mawu a Yesu.

    (KOLASI)

    Ndingapite kwa ndani?

    Angandithandize ndi ndani?

    Ndingapite kwa ndani?

    Mzimu wa dzikoli,

    Umasocheretsa

    Ndizimvera mawu a Yesu.

    Ndingapite kwa ndani?

    Yesu yekha ndizimumvera.