Pitani ku nkhani yake

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sachita Nawo Maholide Ena?

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Sachita Nawo Maholide Ena?

 Kodi a Mboni za Yehova amadziwa bwanji ngati holide inayake ndi yovomerezeka?

 A Mboni za Yehova asanasankhe kuchita nawo holide inayake, amafufuza kaye zimene Baibulo limanena. Maholide komanso zikondwerero zina zimaphwanya mfundo za m’Baibulo ndipo a Mboni za Yehova sachita nawo zoterozo. Koma pali maholide ena omwe wa Mboni aliyense amayenera kusankha yekha pochita zinthu ‘mozindikira kuti asapalamule kwa Mulungu kapena kwa anthu.’​—Machitidwe 24:16.

 Ena mwa mafunso omwe a Mboni za Yehova amadzifunsa asanasankhe kuchita nawo holide ndi awa: a

  •   Kodi holide imeneyi ndi yochokera m’Baibulo?

     Mfundo ya m’Baibulo: “‘Tulukani pakati pawo, lekanani nawo,’ watero Yehova. ‘Musakhudze chinthu chodetsedwa.’”​—2 Akorinto 6:​15-​17.

     Pofuna kusonyeza kuti sakufuna kugwirizana ndi ziphunzitso zosemphana ndi zimene Baibulo limanena, a Mboni za Yehova sachita nawo:

     Maholide amene anachokera pa kukhulupirira kapena kulambira milungu. Yesu ananena kuti: “Yehova Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.” (Mateyu 4:10) Potsatira langizo limeneli, a Mboni za Yehova sakondwerera nawo Khirisimasi, Isitala, kapena May Day, chifukwa chiyambi cha maholide amenewa chinali kulambira milungu ina osati Yehova. Kuwonjezera pa maholide amenewa, a Mboni sachita nawonso maholide otsatirawa.

    •  Kwanzaa. Dzina lakuti Kwanzaa “linachokera ku mawu a Chiswahili akuti matunda ya kwanza, ndipo amatanthauza ‘zipatso zoyambirira.’ Zimene zinalembedwa m’mbiri ya anthu a ku Africa, zimasonyeza kuti holideyi inayambika pa nthawi imene ankakolola zipatso zoyambirira.” (Encyclopedia of Black Studies) Ngakhale kuti anthu ena amaona kuti Kwanzaa ndi mwambo wachikunja, buku la Encyclopedia of African Religion limasonyeza kuti zimene zimachitika pamwambowu, n’zofanana ndi zomwe zimachitika pa chikondwerero cha anthu a ku Africa, pomwe zipatso zoyambirira “zimaperekedwa kwa milungu komanso kwa mizimu ya makolo posonyeza ulemu.” Bukuli limawonjezera kuti: “Cholinga cha holideyi ndi kupereka ulemu komanso kuyamikira moyo umene mizimu ya makolo inatipatsa, ndipo anthu a ku Africa omwe amakhala ku America, amaitchula holideyi kuti, Kwanzaa.”

      Kwanzaa

    •  Chikondwerero Chapakati pa Mwezi(Mid-Autumn Festival). Chimenechi ndi chikondwerero “cholemekeza mulungu wamkazi wa mwezi.” (Holidays, Festivals, and Celebrations of the World Dictionary) Pachikondwererochi pamakhala mwambo woti “akazi azigwadira mulungu wawo wamkazi.”​—Religions of the World​—A Comprehensive Encyclopedia of Beliefs and Practices.

    •  Nauruz (Nowruz). Bungwe lina limanena kuti: “Zina mwa zikondwerero zakale kwambiri zinachokera kuchipembedzo za Zoroastrianism, ndipo mu kalendala ya Zoroastrian tsiku la chikondwererochi limaonedwa kuti ndi limodzi mwa masiku opatulikitsitsa. Zikuoneka kuti m’nyengo yozizira, Mzimu wa Kuzizira unagwetsera pansi panthaka Mzimu wa Kutentha dzina lake Rapithwin. Ndiyeno pofuna kuulandira panakonzedwa chikondwerero pa nthawi ya masana a tsiku la Nowruz mogwirizana ndi mwambo wa Zoroastrian.”​—United Nations Educational, Scientific and Cultural Organization.

    •  Shab-e Yalda. Buku la Sufism in the Secret History of Persia limanena kuti chikondwerechi chimachitika m’nthawi yozizira ndipo “chimakhudzana ndi kulambira Mithra” yemwe ndi mulungu wa kuwala. Anthu ena amanena kuti holide imeneyi ndi yogwirizananso ndi holide ya Aroma ndi Agiriki omwe amalambira milungu ya dzuwa. b

    •  Kupereka Mphatso Zoyamikira. Mofanana ndi Kwanzaa, holideyi imachokera ku zikondwerero zokolola zomwe zimalemekeza milungu yosiyanasiyana. Buku lina limanena kuti, patapita nthawi, “mipingo ya Chikhristu ndi imene inayamba kuchita miyambo imeneyi.”​—A Great and Godly Adventure​—The Pilgrims and the Myth of the First Thanksgiving.

     Maholide omwe anachokera pa kukhulupirira zamatsenga komanso kukhulupirira mwayi. Baibulo limanena kuti inu amene “mumayalira tebulo mulungu wa Mwayi,” ndiye kuti “mwamusiya Yehova.” (Yesaya 65:11) Poganizira mfundo imeneyi, a Mboni za Yehova sakondwerera nawo maholide otsatirawa:

    •  Ivan Kupala. Buku lina limanena kuti: “Malinga ndi zimene anthu ambiri amakhulupirira, pa chikondwerero cha Ivan Kupala chilengedwe chimatulutsa mphamvu zamatsenga ndipo anthu omwe ndi olimba mtima komanso a mwayi amatha kupezako mphamvuzo.” (The A to Z of Belarus) Poyamba Ivan Kupala inali holide ya anthu achikunja ndipo ankachita chikondwererochi m’nyengo yachilimwe. Komabe, buku la Encyclopedia of Contemporary Russian Culture limanena kuti “chikondwererochi chinasakanikirana ndi holide ya tchalitchi yomwe imatchedwa kuti “holide ya oyera mtima” ya Yohane M’batizi, pambuyo poti anthu achikunja alowa Chikhristu.”

    •  Chikondwerero cha Chaka Chatsopano (Chaka Chatsopano cha ku China kapena Chaka Chatsopano cha ku Korea). Buku lina limanena kuti: “Chikondwerero chimenechi chimachitika pakadutsa mwezi umodzi m’chaka chatsopano. Cholinga chachikulu chimakhala kufunira mafuno abwino anthu a m’banja, anthu ocheza nawo ndiponso achibale kuti apeze mwayi m’chaka chimenecho. Amaperekanso ulemu kwa milungu ndi mizimu.” (Mooncakes and Hungry Ghosts​—Festivals of China) N’chimodzimodzinso ndi chikondwerero cha Chaka Chatsopano cha ku Korea. Buku linanso limanena kuti: “Pa nthawiyi amalambira mizimu ya makolo ndipo pamakhala mwambo wochotsa mizimu yoipa n’kufunirana mafuno abwino m’chaka chatsopanocho ndipo amalosera zomwe zichitike m’chakacho.”​—Encyclopedia of New Year’s Holidays Worldwide.

      Chaka Chatsopano cha ku China

     Maholide omwe anachokera pa chiphunzitso choti pali chinachake chimene chimakhalabe ndi moyo munthu akafa. Baibulo limanena momveka bwino kuti moyo umafa. (Ezekieli 18:4) N’chifukwa chake a Mboni za Yehova sachita nawo maholide otsatirawa:

    •  Tsiku Lokumbukira Oyera Mtima Omwe Anamwalira. Buku la New Catholic Encyclopedia, limanena kuti limeneli ndi tsiku “lokumbukira anthu onse okhulupirika omwe anamwalira. M’zaka za m’ma 500 C.E. mpaka cha m’ma 1500 C.E., anthu ambiri ankakhulupirira kuti patsikuli, mizimu yomwe ili ku purigatoliyo inkabwera kwa anthu omwe ankawachitira zinthu zoipa pa nthawi imene anali ndi moyo. Mizimuyi inkaonekera kwa anthuwa ngati nyali za afiti, mizukwa, achule ndi zinthu zina zambiri.”

    •  Chikondwerero cha Qingming (Ch’ing Ming) komanso Chikondwerero cha Mizukwa ya Njala. Zikondwerero ziwiri zonsezi zimachitika pofuna kulemekeza mizimu ya makolo. Buku lina limanena kuti pa nthawi ya chikondwerero cha Ch’ing Ming, “zakudya, zakumwa komanso ndalama za mapepala zimaotchedwa n’cholinga choti mizimu ya akufa isakhale ndi njala, ludzu komanso kuti isakhale yopanda ndalama.” Bukuli limanenanso kuti: “Pa nthawi ya Chikondwerero cha Mizukwa ya Njala, chomwe nthawi zambiri chimachitika usiku womwe mwezi wathunthu watuluka, ochita mwambowu amakhulupirira kuti pa usiku wa tsiku limeneli pamakhala mgwirizano wapadera kwambiri pakati pa anthu akufa ndi anthu a moyo. Choncho pamafunika kupeza njira zabwino zothandizira kuti akufa asakhumudwe komanso zosonyezera ulemu ku mizimu ya makolo.”​—Celebrating Life Customs Around the World​—From Baby Showers to Funerals.

    •  Chuseok. Buku lina limanena kuti pa chikondwererochi pamakhalanso “kupereka chakudya komanso mowa kwa mizimu ya akufa.” Zoperekazi zimasonyeza kuti anthuwo ali ndi “chikhulupiriro choti munthu akafa, chinachake chimakakhalabe ndi moyo kwinakwake.”​—The Korean Tradition of Religion, Society, and Ethics.

     Maholide okhudzana ndi zamatsenga. Baibulo limanena kuti: “Wolosera, wochita zamatsenga, woombeza, wanyanga, kapena wolodza ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu, wolosera zam’tsogolo kapena aliyense wofunsira kwa akufa . . . ndi wonyansa kwa Yehova.” (Deuteronomo 18:10-12) Choncho pofuna kupewa chilichonse chokhudzana ndi zamatsenga, kuphatikizaponso kukhulupirira nyenyezi komwenso kumakhudzana ndi kulosera zam’tsogolo, a Mboni za Yehova sachita nawo chikondwerero cha Halowini kapenanso maholide otsatirawa:

    •  Chaka Chatsopano cha Sinhala komanso Tamil. Buku lina limanena kuti “pamwambowu . . . anthu amakhulupirira kuti kuchita zinthu ndendende pa nthawi imene okhulupirira nyenyezi alosera, kumabweretsera mwayi.”​—Encyclopedia of Sri Lanka.

    •  Songkran. Buku lina limanena kuti limeneli ndi dzina la chikondwerero cha ku Asia “ndipo linatengedwa ku mawu akale omwe panopa amagwiritsidwa ntchito pa zachipembedzo. . . Mawuwo amatanthauza ‘kuyenda’ kapena ‘kusintha.’ Anthu amakhulupirira kuti pa nthawiyi, dzuwa limasintha n’kukhala ngati gulu la nyenyezi zolosera zam’tsogolo zomwe zikakhala pamodzi, zimaoneka ngati nyanga ya nkhosa.”​—Food, Feasts, and Faith​—An Encyclopedia of Food Culture in World Religions.

     Miyambo yokhudzana ndi kulambira yomwe inali pansi pa Chilamulo cha Mose, yomwe inatha ndi nsembe ya Yesu. Baibulo limanena kuti: “Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo.” (Aroma 10:4) N’zoona kuti Akhristu amagwiritsabe ntchito mfundo za m’Chilamulo cha Mose zomwe Aisiraeli ankatsatira. Komabe sachita nawo zikondwerero zomwe zinkachitika nthawi imeneyo, makamaka zokhudzana ndi kubwera kwa Mesiya, yemwe Akhristu amakhulupirira kuti anabwera kale. Baibulo limanena kuti: “Zinthu zimenezo ndi mthunzi wa zimene zinali kubwera, koma zenizeni zake zili mwa Khristu.” (Akolose 2:​17) Popeza kuti cholinga cha zikondwererozo chinakwaniritsidwa kale komanso kuti panopa zikondwerero zoterezi zikumaphatikizidwa ndi miyambo ina yosemphana ndi Malemba, zina mwa zikondwerero zomwe a Mboni za Yehova sachita nawo ndi zimene zili m’munsizi:

    •  Hanukkah. Pachikondwererochi amakumbukira kubwezeretsedwa kwa kachisi wa Ayuda ku Yerusalemu. Komabe Baibulo limanena kuti Yesu atabwera anakhala Mkulu wa Ansembe “m’chihema chachikulu ndi changwiro kwambiri chimene sichinapangidwe ndi manja a anthu, kutanthauza kuti, sichili mbali ya chilengedwe chapansi pano.” (Aheberi 9:​11) Kwa Akhristu, kachisi wauzimuyu analowa m’malo mwa kachisi weniweni wa ku Yerusalemu.

    •  Rosh Hashanah. Chikondwererochi chimachitika pa tsiku loyamba la chaka cha Ayuda. Kale, pamwambowu anthu ankaperekanso nsembe zapadera kwa Mulungu. (Numeri 29:​1-6) Komabe Yesu Khristu monga Mesiya ‘anathetsa nsembe zanyama ndi nsembe zina zoperekedwa ngati mphatso,’ kusonyeza kuti ndi zopanda ntchito kwa Mulungu.​—Danieli 9:​26, 27.

  •   Kodi holideyi imalimbikitsa kuti anthu a m’zipembedzo zosiyanasiyana azichitira zinthu pamodzi?

     Mfundo ya M’Baibulo: “Munthu wokhulupirira angagawane chiyani ndi wosakhulupirira? Ndipo pali kumvana kotani pakati pa kachisi wa Mulungu ndi mafano?”​—2 Akorinto 6:15-17.

     Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amayesetsa kukhala mwamtendere ndi anzawo komanso kulemekeza ufulu wa aliyense wosankha chipembedzo chomwe angafune, sachita nawo zikondwerero zomwe zimalimbikitsa kuti anthu azipembedzo zosiyanasiyana azichitira zinthu limodzi, pochita zinthu zotsatirazi.

     Zikondwerero zokhudzana ndi kulambira chinthu chinachake kapena zochitika zomwe zimalimbikitsa anthu azipembedzo zosiyanasiyana kuti azipempherera pamodzi. Pa nthawi imene Mulungu anatsogolera anthu ake akale kupita kudera latsopano komwe kunali anthu olambira milungu ina, anawauza kuti: “Usachite pangano ndi iwo kapena milungu yawo. . . . Udzakhala msampha kwa iwe.” (Ekisodo 23:32, 33) N’chifukwa chake a Mboni za Yehova sachita maholide otsatirawa.

    •  Loy Krathong. Buku lina limanena kuti chikondwererochi chimachitika ku Thailand ndipo anthu “amakonza mbale zopangidwa ndi masamba, n’kuikamo makendulo kapenanso timitengo tonunkhiritsa ndipo kenako amaika mbalezo m’madzi. Anthuwa amakhulupirira kuti boti likamadutsapo limachotsa tsoka m’madziwo. Mwachidule tinganene kuti anthu amachita chikondwererochi pokumbukira madindo oyeretsedwa omwe Buddha anasiya.”​—Encyclopedia of Buddhism.

    •  Tsiku Lolapa Machimo. Mogwirizana ndi zomwe mkulu wa boma ananena mu nyuzipepala ina ya ku Papua New Guinea, anthu amene amatenga nawo mbali pachikondwererochi “amakhala omwe anavomereza kutsatira mfundo zachikhristu.” Ananenanso kuti limeneli ndi tsiku loti “anthu m’dziko lonselo alimbikitsidwe kuti azitsatira mfundo zachikhristu.”​—The National.

    •  Vesak. Buku lina limanena kuti “limeneli ndi tsiku lopatulikitsitsa pa masiku oyera Achibuda ndipo amakondwerera kubadwa kwa Buddha, imfa yake komanso kuti anabweretsa kuwala kwauzimu.”​—Holidays, Festivals, and Celebrations of the World Dictionary.

      Vesak

     Miyambo yomwe inachokera pa ziphunzitso zachipembedzo zosagwirizana ndi Baibulo. Yesu anauza atsogoleri achipembedzo kuti: “Mwasandutsa mawu a Mulungu kukhala opanda pake chifukwa cha miyambo yanu.” Anawauzanso kuti kulambira kwawo n’kopanda phindu chifukwa “amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.” (Mateyu 15:6, 9) A Mboni za Yehova amamvera chenjezo limeneli ndipo sachita nawo miyambo yokhudza zipembedzo yotsatirayi.

    •  Epiphany (Tsiku Lokumbukira Mafumu Atatu, Timkat kapena kuti Los Reyes Magos). Anthu ochita chikondwererochi amakumbukira okhulupirira nyenyezi omwe anapita kukaona Yesu kapenanso kukumbukira ubatizo wa Yesu. Buku lina limanena kuti chikondwererochi “chinatembenuza zikondwerero zachikunja n’kukhala zachikhristu. Poyamba zikondwerero zachikunjazi zinkalemekeza milungu ya mitsinje.” (The Christmas Encyclopedia) Pamene chikondwerero cha Timkat, “chimakhudzana kwambiri ndi chikhalidwe.”​—Encyclopedia of Society and Culture in the Ancient World.

    •  Phwando Lokumbukira Kuti Mariya Virigo Anapita Kumwamba. Anthu ochita phwandoli amakhulupirira kuti amayi a Yesu anakwera kumwamba ndi thupi lawo lenileni. Buku lina limanena kuti “Akhristu oyambirira sankadziwa za mwambo umenewu ndipo supezeka m’Baibulo.”​—Religion and Society​—Encyclopedia of Fundamentalism.

    •  Phwando Lokumbukira Kuti Mariya Anabadwa Wopanda Tchimo. Buku lina limanena kuti: “Baibulo silimafotokoza zoti Mariya analibe tchimo, . . . koma chimenechi ndi chiphunzitso cha tchalitchi.”​—New Catholic Encyclopedia.

    •  Kusala Kudya. Panyengo imeneyi anthu amalapa komanso kusala kudya. Buku la New Catholic Encyclopedia limati chikondwererochi chinakhazikitsidwa “m’zaka za m’ma 300 C.E.” ndipo pa nthawiyi panali patadutsa zaka zoposa 200 kuchokera pomwe Baibulo linamalizidwa kulembedwa. Ponena za tsiku loyamba la mwambo wa Kusala Kudya, bukuli limanenanso kuti: “Pachikondwererochi anthu okhulupirika amajambulidwa mtanda pachipumi ndi phulusa, pa Tsiku Lowaza Phulusa. Mwambowu womwe unachokera ku Benevento, ndipo unayamba mu 1091, wakhala ukuchitika padziko lonse.”

    •  Meskel (Maskal). Buku lina limanena kuti chimenechi ndi chikondwerero cha ku Ethiopia pomwe amakumbukira “kupezeka kwa Mtanda Weniweni (mtanda umene Khristu anapachikidwapo), ndipo amayatsa moto n’kumavina mozungulira motowo.” (Encyclopedia of Society and Culture in the Medieval World) Koma a Mboni za Yehova sagwiritsa ntchito mtanda polambira.

  •   Kodi holideyi imapereka ulemu wapadera kwa munthu, bungwe kapena chizindikiro chinachake choimira dziko?

     Lemba lothandiza: “Yehova wanena kuti: ‘Wotembereredwa ndi munthu aliyense wokhulupirira mwa munthu aliyense wochokera kufumbi. Wotembereredwa ndi munthu amene amadalira mphamvu za dzanja la munthu, komanso amene mtima wake wapatuka kuchoka kwa Yehova.’”​—Yeremiya 17:5.

     Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amayamikira anzawo komanso kuwapempherera, sachita nawo zochitika ndiponso zikondwerero zotsatirazi:

     Maholide omwe amalemekeza wolamulira kapena munthu wina wolemekezeka. Baibulo limanena kuti: “Kuti zinthu zikuyendereni bwino, musadalire munthu wochokera kufumbi amene mpweya wake uli m’mphuno mwake, pakuti palibe chifukwa choti mum’ganizire iyeyo.” (Yesaya 2:22) N’chifukwa chake a Mboni za Yehova sachita nawo zinthu monga kukondwerera tsiku lobadwa la mfumu kapena mfumukazi.

     Zikondwerero za mbendera ya dziko. N’chifukwa chiyani a Mboni za Yehova samakondwerera nawo Tsiku Lokumbukira Mbendera? Baibulo limanena kuti: “Pewani mafano.” (1 Yohane 5:​21) Anthu ena masiku ano sazindikira kuti kulemekeza mbendera n’chimodzimodzi ndi kulambira mafano. Koma wolemba mbiri wina dzina lake Carlton J. H. Hayes analemba kuti: “Chizindikiro chosonyeza kuti munthu amakonda kwambiri dziko lake komanso kulikhulupirira ndi kulambira mbendera.”

     Maholide kapena zikondwerero zomwe cholinga chake ndi kulemekeza oyera mtima. Munthu wina woopa Mulungu atagwadira mtumwi Petulo, Baibulo limanena kuti: “Petulo anamuimiritsa, ndi kunena kuti: ‘Imirira, inenso ndine munthu chabe.’” (Machitidwe 10:25, 26) Popeza kuti Petulo komanso atumwi ena onse sanavomereze kulandira ulemu wapadera kapena kulambiridwa, nawonso a Mboni za Yehova sachita zikondwerero zolemekeza anthu omwe amati ndi oyera mtima, monga zotsatirazi:

    •  Tsiku la Oyera Mtima. Buku lina limanena kuti: “Phwandoli limachitika pofuna kulemekeza oyera mtima onse. . . . Ndipo chiyambi chake sichidziwika.”​—New Catholic Encyclopedia.

    •  Chikondwerero cha Mayi Woyera wa ku Guadalupe(Fiesta of Our Lady of Guadalupe). Chikondwererochi chimalemekeza “woyera mtima wamkazi wa ku Mexico,” amene anthu ena amakhulupirira kuti ndi Mariya, mayi ake a Yesu. Anthuwo amanena kuti mayiyu anaonekera mozizwitsa kwa mlimi wosauka mu 1531.​—The Greenwood Encyclopedia of Latino Literature.

      Fiesta of Our Lady of Guadalupe

    •  Tsiku Lopereka Dzina. Buku lina limanena kuti: “Limeneli ndi tsiku la oyera mtima ndipo anthu amachita phwando pambuyo poti mwana wapatsidwa dzina, pamene wabatizidwa kapena pambuyo poti wasonyeza kuti ali ndi chikhulupiriro pamwambo wa tchalitchi.” Limawonjezeranso kuti: “Pa tsikuli anthu amachita zinthu zokhudzana ndi chipembedzo.”​—Celebrating Life Customs Around the World​—From Baby Showers to Funerals.

     Zikondwerero za andale kapena zofuna kukonza zinthu m’dziko. Baibulo limanena kuti: “Kuthawira kwa Yehova n’kwabwino kusiyana ndi kudalira munthu wochokera kufumbi.” (Salimo 118:8, 9) Pofuna kusonyeza kuti amakhulupirira kuti Mulungu ndi amene adzathetse mavuto osati anthu, a Mboni za Yehova satenga nawo mbali pa zikondwerero zokhudzana ndi Tsiku la Achinyamata kapena Tsiku la Amayi, zomwe cholinga chake ndi kuthandizira zandale kapena kukonza zinthu m’dziko. A Mboni za Yehova satenganso mbali pa Tsiku Lokondwerera Kutha Kwa Ukapolo kapena zikondwerero zina zofanana ndi zimenezi. M’malomwake amayembekezera kuti Ufumu wa Mulungu ndi umene udzathetse mavuto obwera chifukwa cha kusankhana mitundu.​—Aroma 2:11; 8:21.

  •   Kodi holideyi imachititsa anthu kuona kuti mtundu wina ndi wofunika kwambiri kuposa unzake?

     Lemba lothandiza: “Mulungu alibe tsankho, Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.”​—Machitidwe 10:34, 35.

     Ngakhale kuti a Mboni za Yehova ambiri amakonda dziko lawo, iwo amapewa zikondwerero zomwe zingachititse kuti mtundu wawo kapena dziko lawo lizioneka lapamwamba kwambiri. Zikondwerero zake ndi monga:

     Zochitika zomwe zimalemekeza asilikali. M’malo molimbikitsa nkhondo, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Pitirizani kukonda adani anu ndi kupempherera amene akukuzunzani.” (Mateyu 5:44) Choncho a Mboni za Yehova sachita nawo zikondwerero zomwe zimalemekeza asilikali, kuphatikizapo maholide otsatirawa:

    •  Anzac Day. Buku lina limanena kuti “Anzac ndi mawu achidule a Australian and New Zealand Army Corps,” ndipo “pang’ono ndi pang’ono tsiku la Anzac linasanduka tsiku lokumbukira anthu amene anaphedwa pankhondo.”​—Historical Dictionary of Australia.

    •  Tsiku Lokumbukira Asilikali (Remembrance Day, Remembrance Sunday, or Memorial Day). Pamaholide amenewa anthu amakumbukira “asilikali a m’dzikolo omwe anapuma pantchito komanso amene anaphedwa kunkhondo.”​—Encyclopædia Britannica.

     Zikondwerero za mbiri ya dziko kapena tsiku limene dziko linalandira ufulu. Ponena za otsatira ake, Yesu ananena kuti: “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:16) Ngakhale kuti a Mboni za Yehova amasangalala kudziwa mbiri ya dziko lawo, iwo sachita nawo zikondwerero zotsatirazi:

    •  Australia Day. Pa tsikuli anthu amakumbukira kuti “mu 1788 asilikali a ku Britain anakweza mbendera zawo n’kulengeza kuti ayamba kulamulira dziko la Australia.”​—Worldmark Encyclopedia of Cultures and Daily Life.

    •  Guy Fawkes Day. Pa tsikuli anthu “amakumbukira za chiwembu chimene chinalephereka m’chaka cha 1605, chomwe Guy Fawkes ndi anthu ena Achikatolika omwe ankamuthandizira anapanga, chofuna kupha Mfumu James I komanso akuluakulu a boma la England.”​—A Dictionary of English Folklore.

    •  Tsiku Lokumbukira Ufulu Wodzilamulira. M’mayiko ambiri limeneli ndi “tsiku lokhazikitsidwa ndi boma ndipo pachikondwererochi anthu amakumbukira tsiku limene dziko lawo linalandira ufulu n’kuyamba kudzilamulira.”—Merriam-Webster’s Unabridged Dictionary.

  •   Kodi holideyi imadziwika ndi makhalidwe oipa?

     Lemba lothandiza: “Nthawi imene yapitayi inali yokwanira kwa inu kuchita chifuniro cha anthu a m’dzikoli pamene munali kuchita zinthu zosonyeza khalidwe lotayirira, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitirira muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”​—1 Petulo 4:3.

     Potsatira mfundo imeneyi, a Mboni za Yehova sapita ku zikondwerero komwe anthu amaledzera komanso kumaphwando a phokoso. Komabe amasangalala kucheza ndi anzawo, ndipo ngati akufuna, amatha kusankha kumwa mowa pang’ono. Iwo amayesetsa kutsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.”​—1 Akorinto 10:31.

     Choncho a Mboni za Yehova sachita nawo zikondwerero zimene zimalimbikitsa makhalidwe oipa amene Baibulo limaletsa. Zimenezi zikuphatikizapo phwando la Ayuda la Purim. Ngakhale kuti kwa zaka zambiri Ayuda akhala akuchita mwambo wa Purimu pokumbukira tsiku limene anamasulidwa ku ukapolo zaka za m’ma 400 B.C.E., buku la Essential Judaism limanena kuti: “Masiku ano mwambowu si odziwikanso kwambiri ndipo ukulowedwa m’malo ndi chikondwerero chachiyuda cha Mardi Gras kapena kuti Carnival.” Bukuli limapitirizanso kuti paphwandoli, “nthawi zambiri amuna amavala zovala za akazi, pamachitika zipolowe, anthu amaledzera, ndiponso pamakhala phokoso lokhalokha.”

 Kodi a Mboni za Yehova amene sachita nawo maholide enaake, amakonda mabanja awo?

 Inde. Baibulo limaphunzitsa kuti anthu onse m’banja ayenera kukondana komanso kulemekezana, mosatengera zimene wina amakhulupirira. (1 Petulo 3:​1, 2, 7) N’zoona kuti wa Mboni za Yehova akasiya kuchita nawo zikondwerero zinazake, achibale ake ena akhoza kukhumudwa. Komabe zikatero, a Mboni za Yehova ambiri amayesetsa kusonyeza kuti amakonda achibale awowo powafotokozera mwaulemu chifukwa chake asankha kusachita nawo zikondwerero zinazake ndipo amapita kukawaona pakakhala zochitika zina.

 Kodi a Mboni za Yehova amakakamiza anthu kuti asamachite nawo maholide ena?

 Ayi. Iwo amakhulupirira kuti aliyense ayenera kusankha yekha zochita. (Yoswa 24:15) A Mboni za Yehova ‘amalemekeza anthu, kaya akhale amtundu wotani,’ posatengera zimene amakhulupirira.​—1 Petulo 2:17.

a Nkhaniyi sinafotokoze za maholide onse omwe a Mboni za Yehova sachita nawo komanso sinafotokoze mfundo zonse za m’Baibulo zomwe zingagwire ntchito posankha holide.

b Buku la Mithra, Mithraism, Christmas Day & Yalda, lolembedwa ndi K.E. Eduljee, tsamba 31-33.