Pitani ku nkhani yake

KUFOTOKOZA MAVESI A M’BAIBULO

Aroma 12:12—“Kondwerani ndi Chiyembekezocho. Pirirani Chisautso. Limbikirani Kupemphera”

Aroma 12:12—“Kondwerani ndi Chiyembekezocho. Pirirani Chisautso. Limbikirani Kupemphera”

 “Kondwerani ndi chiyembekezocho. Pirirani chisautso. Limbikirani kupemphera.”—Aroma 12:12, Baibulo la Dziko Latsopano.

 “Kondwereni m’chiyembekezo, pirirani m’masautso, limbikani chilimbikire m’kupemphera.”—Aroma 12:12, Buku Lopatulika Ndilo Mau a Mulungu.

Tanthauzo la Aroma 12:12

 Muvesili, Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu a ku Roma kuchita zinthu zitatu zomwe zikanawathandiza kuti akhalebe okhulupirika ngakhale kuti ankazunzidwa komanso kukumana ndi mavuto ena.

 “Kondwerani ndi chiyembekezocho.” Akhristu ali ndi chiyembekezo chosangalatsa kwambiri chodzakhala ndi moyo wosatha. Ena adzakhala ndi moyowu kumwamba pomwe ambiri adzakhala ndi moyowu m’paradaiso padziko lapansi. (Salimo 37:29; Yohane 3:16; Chivumbulutso 14:1-4; 21:3, 4) Akhristu amayembekezeranso kudzaona Ufumu wa Mulungu a ukuthetsa mavuto onse omwe anthu akuvutika nawo. (Danieli 2:44; Mateyu 6:10) Atumiki a Mulungu akhoza kukhalabe osangalala ngakhale pomwe akukumana ndi mavuto chifukwa amakhulupirira kuti zomwe akuyembekezerazo zidzachitikadi. Komanso amadziwa kuti akakhalabe opirira, amakhala ovomerezeka kwa Mulungu.—Mateyu 5:11, 12; Aroma 5:3-5.

 “Pirirani chisautso.” M’Baibulo, mawu a Chigiriki omwe anawamasulira kuti ‘kupirira,’ nthawi zambiri amatanthauza “kukhalabe pomwepo m’malo mothawa” kapena “kukhalabe wolimba.” Otsatira a Khristu si ali “mbali ya dziko,” b choncho amayembekezera kuzunzidwa. Ichi n’chifukwa chake amafunika kupirira. (Yohane 15:18-20; 2 Timoteyo 3:12) Ngati Mkhristu akutumikira Mulungu mopirira pomwe akukumana ndi mayesero, chikhulupiriro chake mwa Mulungu chimalimba chifukwa amadziwa kuti Mulungu adzamudalitsa. (Mateyu 24:13) Chikhulupiriro chomwe amakhala nachochi chimamuthandiza kupirira moleza mtima komanso mosangalala, mavuto omwe angakumane nawo.—Akolose 1:11.

 “Limbikirani kupemphera.” Akhristu amalimbikitsidwa mobwerezabwereza kuti azipemphera ndi cholinga choti akhalebe okhulupirika kwa Mulungu. (Luka 11:9; 18:1) Kuchita zimenezi kumawapatsa mwayi wopitiriza kutsogoleredwa ndi Mulungu komanso kumudalira pa mbali zosiyanasiyana za moyo wawo.(Akolose 4:2; 1 Atesalonika 5:17) Iwo sakayikira kuti Mulungu ayankha mapemphero awo chifukwa amamvera malamulo ake komanso amayesetsa kuchita zinthu zomwe zimamusangalatsa. (1 Yohane 3:22; 5:14) Amadziwanso kuti akalimbikira kupemphera, Mulungu adzawapatsa mphamvu zomwe zingawathandize kuti akhalebe okhulupirika ngakhale atakumana ndi mayesero otani.—Afilipi 4:13.

Nkhani yonse ya pa Aroma 12:12

 Paulo analemba kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma cha m’ma 56 C.E. Muchaputala 12 cha kalatayi, iye anawapatsa malangizo a mmene angasonyezere makhalidwe achikhristu, mmene angachitire zinthu ndi Akhristu anzawo ndiponso anthu ena, komanso mmene angachitire zinthu mwamtendere pomwe akuzunzidwa. (Aroma 12:9-21) Malangizowa anali apanthawi yake, chifukwa pasanapite nthawi yaitali, Akhristu a ku Roma anayamba kuzunzidwa kwambiri.

 Patangopita nthawi yochepa mu 64 C.E., moto woopsa unawononga mbali yaikulu ya mzinda wa Roma. Kenako kunamveka mphekesera yoti Mfumu Nero ndi amene anayatsa motowo. Wolemba mbiri wina wa ku Roma dzina lake Tacitus ananena kuti, pofuna kudziteteza, Mfumu Nero anayamba kuimba mlandu Akhristu kuti ndiwo anayatsa motowo. Chifukwa cha zimenezi, Akhristu anayamba kuzunzidwa kwambiri. Malangizo omwe Paulo anaperekawa, anathandiza Akhristuwa kuti akhalebe okhulupirika pa nthawi yovutayi. (1 Atesalonika 5:15; 1 Petulo 3:9) Chimenechi ndi chitsanzo chabwino kwambiri kwa atumiki a Mulungu a masiku ano.

 Onerani vidiyo yaifupiyi kuti muone mfundo zokhudza buku la Aroma.

a Ufumu wa Mulungu ndi boma lakumwamba lomwe linakhazikitsidwa ndi Mulungu kuti cholinga chake chomwe analengera dziko lapansili chidzakwaniritsidwe. Kuti mudziwe zambiri, werengani nkhani yakuti, “Kodi Ufumu wa Mulungu N’chiyani?

b M’Baibulo, mawu akuti “dziko,” amathanso kutanthauza anthu otalikirana ndi Mulungu.