Onani zimene zilipo

Kodi a Mboni za Yehova amalalikila nyumba na nyumba kuti akapulumuke?

Kodi a Mboni za Yehova amalalikila nyumba na nyumba kuti akapulumuke?

 Ayi. Kaŵili-kaŵili timalalikila nyumba na nyumba, koma sitikhulupilila kuti tidzapulumuka cifukwa cogwila nchito imeneyi. (Aefeso 2:8) N’cifukwa ciani takamba conco?

 Ganizilani izi: Tiyelekeze kuti munthu wina wacifundo, walonjeza kuti aliyense amene adzapezeka pa malo ena ake, pa deti imene wakamba, adzam’patsa mphatso yamtengo wapatali. Ngati mumam’khulupilila munthuyo, kodi mungatsatile malangizo ake? Mosakaikila mungacite zimenezo! Ndipo mwina mungauzeko mabwenzi anu ndi acibululu anu kuti nawonso apindule na mwayi wapadela umenewo. Ngakhale n’conco, mwalandila mphatsoyo osati cifukwa cakuti mwapezeka pa malo amene munthuyo anakuuzani, koma cifukwa cakuti munthuyo anali kufuna kukupatsani mphatsoyo.

 Mofananamo, Mboni za Yehova zimakhulupilila lonjezo la Mulungu la moyo wosatha, umene adzapeleka kwa onse amene amamumvela. (Aroma 6:23) Timayesetsa kuuzako ena zimene timakhulupilila, kuti naonso akapindule na malonjezo a Mulungu. Koma sitikhulupilila kuti tidzalandila cipulumutso mwa kugwila nchito yolalikila. (Aroma 1:17; 3:28) Kukamba zoona, palibe zimene munthu angacite kuti ayenelele dalitso lamtengo wapatali limeneli locokela kwa Mulungu. Baibo imati, “Iye sanatelo cifukwa ca nchito zolungama zimene tinacita ayi. Koma malinga ndi cifundo cake, anatipulumutsa.”—Tito 3:5.