Onani zimene zilipo

N’cifukwa Ciani Mboni za Yehova Zimalalikila Kunyumba ndi Nyumba?

N’cifukwa Ciani Mboni za Yehova Zimalalikila Kunyumba ndi Nyumba?

Yesu anauza otsatila ake kuti ‘aziphunzitsa anthu a mitundu yonse.’ (Mateyu 28:19, 20) Pamene Yesu anatuma ophunzila ake oyambilila, anawauza kuti apite ku nyumba za anthu. (Mateyu 10:7, 11-13) Ndipo pambuyo pa imfa yake, Akristu a m’nthawi ya atumwi anapitiliza kufalitsa uthenga wabwino “poyela komanso kunyumba ndi nyumba.” (Machitidwe 5:42; 20:20) Masiku ano, timatengela citsanzo ca Akristu oyambilila, ndipo taona kuti kulalikila kunyumba ndi nyumba ndi njila yabwino yofikila anthu.