Onani zimene zilipo

Kodi Mboni za Yehova Zimalemekeza Zipembedzo Zina?

Kodi Mboni za Yehova Zimalemekeza Zipembedzo Zina?

Timatsatila malangizo a m’Baibulo akuti: ‘Lemekezani anthu onse,’ kaya ndi acipembezo cotani. (1 Petulo 2:17) Mwacitsanzo, m’maiko ena muli Mboni za Yehova masauzande ambili. Koma sitikakamiza andale kapena opanga malamulo kuti aletse nchito ya zipembedzo zina. Ndiponso sitipempha boma kuti likhazikitse malamulo amene angakakamize anthu kutsatila zikhulupililo zathu. M’malo mwake timalemekeza anthu a zipembedzo zina ndipo timayamikila ionso akamatilemekeza.—Mateyu 7:12.