Onani zimene zilipo

Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupilila Kuti Ndizo Zokha Zidzapulumuka?

Kodi Mboni za Yehova Zimakhulupilila Kuti Ndizo Zokha Zidzapulumuka?

Iyai. Anthu mamiliyoni ambili amene anakhalapo zaka zambili m’mbuyomu, ndipo amene sanali Mboni za Yehova adzakhala ndi mwai wolandila moyo wosatha. Baibulo limafotokoza kuti m’dziko latsopano limene Mulungu analonjeza, “kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15) Ndiponso anthu ambili amene angayambe kutumikila Mulungu naonso angadzapulumuke. Ngakhale n’conco, si udindo wathu kuweluza munthu kuti adzapulumuka kapena ai. Amene ali ndi udindo woweluza ndi Yesu cabe.