2 Mbiri 26:1-23

  • Uziya, mfumu ya Yuda (1-5)

  • Nkhondo zimene Uziya anamenya (6-15)

  • Uziya anachititsidwa khate chifukwa chodzikuza (16-21)

  • Imfa ya Uziya (22, 23)

26  Kenako anthu onse a ku Yuda anatenga Uziya,+ yemwe pa nthawiyo anali ndi zaka 16, nʼkumuika kuti akhale mfumu mʼmalo mwa bambo ake Amaziya.+  Mfumuyo,* mofanana ndi makolo ake, itamwalira, Uziya anamanganso mzinda wa Eloti+ nʼkuubwezera ku Yuda.+  Uziya+ anakhala mfumu ali ndi zaka 16, ndipo analamulira ku Yerusalemu zaka 52. Amayi ake anali a ku Yerusalemu ndipo dzina lawo linali Yekoliya.+  Iye ankachita zoyenera pamaso pa Yehova ngati mmene anachitira Amaziya bambo ake.+  Uziya anapitiriza kufunafuna Mulungu mʼmasiku a Zekariya yemwe ankamuphunzitsa kuti aziopa Mulungu woona. Pa nthawi imene iye ankafunafuna Yehova, Mulungu woonayo anachititsa kuti zinthu zizimuyendera bwino.+  Iye anapita kukamenyana ndi Afilisiti+ ndipo anagumula mpanda wa ku Gati,+ wa ku Yabine+ ndi wa ku Asidodi. Kenako anamanga mizinda mʼchigawo cha Asidodi+ ndiponso pakati pa Afilisiti.  Mulungu woona anapitiriza kumuthandiza kugonjetsa Afilisiti, Aluya+ amene anali kukhala ku Gurubaala ndiponso Ameyuni.  Aamoni+ anayamba kupereka msonkho kwa Uziya. Patapita nthawi, iye anatchuka mpaka ku Iguputo chifukwa anakhala wamphamvu kwambiri.  Komanso Uziya anamanga nsanja+ ku Yerusalemu pafupi ndi Geti la Pakona,+ Geti la Kuchigwa+ ndiponso pafupi ndi Mchirikizo wa Khoma ndipo nsanjazo anazilimbitsa. 10  Iye anamanganso nsanja+ mʼchipululu ndipo anakumba* zitsime zambiri (popeza anali ndi ziweto zambiri). Anapanganso zomwezo ku Sefela ndi kudera lafulati. Anali ndi alimi komanso anthu osamalira minda ya mpesa kumapiri ndi ku Karimeli poti iye ankakonda ulimi. 11  Komanso Uziya anali ndi gulu la asilikali okonzeka kumenya nkhondo. Iwo ankapita kunkhondo mʼmagulumagulu. Asilikaliwa anawerengedwa komanso kulembedwa mayina+ ndi Yeyeli mlembi+ ndiponso Maaseya womuthandiza wake. Awiriwa ankayangʼaniridwa ndi Hananiya mmodzi wa akalonga a mfumu. 12  Atsogoleri onse a nyumba za makolo awo, amene ankayangʼanira asilikali amphamvuwa, analipo 2,600. 13  Atsogoleri amenewa ankayangʼanira asilikali okwana 307,500, okonzeka kumenya nkhondo. Limeneli linali gulu lamphamvu la asilikali lomwe linkathandiza mfumu kulimbana ndi adani.+ 14  Uziya anaonetsetsa kuti gulu la asilikali lonselo lili ndi zishango, mikondo ingʼonoingʼono,+ zipewa, zovala zamamba achitsulo,+ mauta ndi miyala yoponya ndi gulaye.*+ 15  Komanso ku Yerusalemu iye anapangako makina ankhondo opangidwa ndi anthu aluso. Makinawa anawaika pansanja+ ndi mʼmakona a mpanda ndipo ankatha kuponya mivi ndi miyala ikuluikulu. Choncho anatchuka kulikonse, chifukwa ankathandizidwa kwambiri ndipo anakhala wamphamvu. 16  Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unayamba kudzikuza mpaka kufika pomʼpweteketsa. Iye anachita zosakhulupirika kwa Yehova Mulungu wake ndipo anapita mʼkachisi wa Yehova kukapereka nsembe zofukiza paguwa lansembe.+ 17  Nthawi yomweyo wansembe Azariya komanso ansembe ena a Yehova olimba mtima okwanira 80, anamutsatira. 18  Iwo anapita pamene panali Mfumu Uziya kukamuletsa. Anamuuza kuti: “Mfumu Uziya, si zoyenera kuti inuyo mupereka nsembe zofukiza kwa Yehova.+ Ansembe okha ndi amene ayenera kupereka nsembe zofukiza chifukwa ndi mbadwa za Aroni+ ndipo anayeretsedwa. Tulukani mʼnyumba yopatulikayi popeza mwachita zosakhulupirika ndipo zimenezi sizikubweretserani ulemerero wochokera kwa Yehova Mulungu.” 19  Koma Uziya, amene anali atanyamula choperekera nsembe, anawakwiyira kwambiri+ ansembewo. Zitatero, anachita khate+ pachipumi pake. Anachita khatelo ansembewo ali pompo mʼnyumba ya Yehova pafupi ndi guwa lansembe zofukiza. 20  Wansembe wamkulu Azariya ndi ansembe ena onse atamuyangʼana, anangoona kuti wachita khate pachipumi. Choncho anayamba kumutulutsa msangamsanga ndipo mwiniwakeyonso anatuluka mofulumira chifukwa Yehova anali atamuchititsa khate. 21  Mfumu Uziya anakhala wakhate mpaka tsiku limene anamwalira. Iye ankakhala mʼnyumba yayekha chifukwa cha khatelo+ popeza anali atamuchotsa mʼnyumba ya Yehova. Yotamu mwana wake ndi amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu komanso kuweruza anthu amʼdzikolo.+ 22  Nkhani zina zokhudza Uziya, kuyambira pachiyambi mpaka pamapeto, zinalembedwa ndi mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi. 23  Kenako Uziya, mofanana ndi makolo ake, anamwalira ndipo anaikidwa mʼmanda a makolo ake, koma anamuika kunja kwa manda a mafumu chifukwa anati: “Ndi wakhate.” Ndiyeno mwana wake Yotamu+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.

Mawu a M'munsi

Ameneyu ndi Amaziya, bambo ake.
Ayenera kuti ankachita kuboola thanthwe.
Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala chimene amachita kupukusa ndi dzanja.