Yobu 5:1-27

  • Mawu oyamba a Elifazi akupitirira (1-27)

    • ‘‘Mulungu amachititsa kuti anzeru agwere mʼmisampha yawo’ (13)

    • ‘Yobu asakane chilango cha Mulungu’ (17)

5  “Taitana! Kodi pali aliyense amene akukuyankha? Ndipo kodi utembenukira kwa mngelo* uti?   Chifukwa kusunga chakukhosi kudzapha wopusa,Ndipo nsanje idzapha munthu amene sachedwa kukopeka.   Ine ndaonapo wopusa atazika mizu,Koma mwadzidzidzi malo ake okhala anatembereredwa.   Ana ake ndi osatetezeka,Ndipo amaponderezedwa pageti la mzinda,+ popanda wowapulumutsa.   Munthu wanjala amadya zimene munthu wopusa wakolola,Iye amatenga ngakhale zimene zamera paminga,Ndipo chuma cha munthu wopusayo ndi ana ake chimalandidwa.   Zinthu zoipa siziphuka kuchokera mufumbi,Ndipo mavuto satuluka munthaka.   Chifukwa munthu amabadwa kuti akumane ndi mavuto,Ngati mmene moto umathethekera kupita mʼmwamba.   Koma ndikanakhala ine, ndikanakadandaula kwa Mulungu,Ndipo ndikanakatula mlandu wanga kwa Mulunguyo,   Kwa Iye amene amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,Zinthu zodabwitsa zosawerengeka. 10  Iye amapereka mvula padziko lapansi,Ndipo amapititsa madzi kuminda. 11  Iye amakweza munthu wonyozeka pamwamba,Ndipo amapulumutsa munthu amene akuvutika. 12  Iye amalepheretsa zolinga za anthu ochenjera,Nʼcholinga choti ntchito ya manja awo isayende bwino. 13  Iye amachititsa kuti anzeru agwere mʼmisampha yawo,+Kuti mapulani a anthu ochenjera alephereke. 14  Iwo amakumana ndi mdima masana,Ndipo amapapasa masana ngati kuti ndi usiku. 15  Iye amapulumutsa munthu ku lupanga lochokera mʼkamwa mwa oipa,Amapulumutsa wosauka mʼmanja mwa munthu wamphamvu, 16  Kuti wonyozeka akhale ndi chiyembekezo,Koma pakamwa pa anthu opanda chilungamo pamatsekedwa. 17  Tamvera! Wosangalala ndi munthu amene Mulungu amamudzudzula.Choncho usakane chilango* cha Wamphamvuyonse. 18  Chifukwa iye amapangitsa kuti munthu amve kupweteka, koma amamanga chilonda chopwetekacho.Amaphwanya anthu, koma amawachiritsa ndi manja ake. 19  Adzakupulumutsa ku masoka 6,Ndipo ngakhale tsoka la 7 silidzakuvulaza. 20  Pa nthawi yanjala adzakupulumutsa* ku imfa,Ndipo adzakupulumutsa ku mphamvu ya lupanga pa nthawi yankhondo. 21  Mulungu adzakuteteza ku lilime lomenya ngati chikwapu,+Ndipo sudzachita mantha tsoka likadzafika. 22  Sudzada nkhawa ndi masoka kapena njala,Ndipo sudzaopa nyama zakutchire. 23  Miyala yakutchire sidzakuvulaza,*Ndipo nyama zakutchire zidzakhala nawe mwamtendere. 24  Udzaona kuti tenti yako ndi yotetezeka,*Ndipo ukamayendera malo ako odyetserako ziweto, udzaona kuti palibe chimene chikusowa. 25  Udzasangalala kuona ana ako atachuluka,Ndipo mbadwa zako zidzakhala zochuluka ngati zomera za padziko lapansi. 26  Udzakhalabe ndi mphamvu ukamadzalowa mʼmanda,Mofanana ndi ngala za tirigu zimene zakololedwa pa nyengo yake. 27  Izi nʼzimene tafufuza ndipo zilidi choncho. Imva zimenezi ndipo uzivomereze.”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “woyera.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “chilango” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakuwombola.”
Kapena kuti, “idzachita pangano (mgwirizano) ndi iwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “tenti yako ili pa mtendere.”