Pitani ku nkhani yake

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupezeka Pamisonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu?

N’chifukwa Chiyani Ndiyenera Kupezeka Pamisonkhano ya pa Nyumba ya Ufumu?

 Mlungu uliwonse, a Mboni za Yehova amakumana kawiri pa nyumba yomwe amalambirira yotchedwa Nyumba ya Ufumu. Kodi kumeneko kumachitika zotani, nanga mungapindule bwanji ngati mutapezeka pamisonkhano yawo?

 Kodi ku Nyumba ya Ufumu kumachitika zotani?

 Ku Nyumba ya Ufumu, anthu amakhala ndi mwayi wophunzira mfundo zothandiza za m’Baibulo. Misonkhano yomwe imachitika kumeneko ingakuthandizeni kuti:

  •   muphunzire ndi kumudziwa bwino Mulungu.

  •   mudziwe chifukwa chake zinthu zafika poipa kwambiri chonchi.

  •   mukhale munthu wa makhalidwe abwino.

  •    mupeze anthu abwino omwe angakhale anzanu.

 Kodi Mukudziwa? Malo olambirira a Mboni za Yehova amatchedwa kuti Nyumba ya Ufumu, chifukwa mfundo zambiri zomwe amaphunzira kumeneko zimakhala zokhudza Ufumu wa Mulungu.​—Mateyu 6:9, 10; 24:14; Luka 4:43.

 N’chifukwa chiyani muyenera kupezeka pamisonkhano imeneyi?

 Zimene mungakaphunzire zingakuthandizeni. Mfundo za m’Baibulo zomwe anthu amaphunzira pamisonkhano ya Mboni za Yehova, zingakuthandizeni kuti mupeze “nzeru.” (Miyambo 4:5) Zimenezi zikusonyeza kuti mfundo za m’Baibulo zingakuthandizeni kusankha bwino zoti muchite pa moyo wanu. Zingakuthandizeninso kupeza mayankho amafunso ofunika kwambiri monga akuti:

 Onani mitu ya nkhani zina zomwe zimakambidwa kumapeto kwa mlungu uliwonse. Nkhani zake ndi monga:

  •   Chifukwa Chiyani Tiyenera Kutsatira Malangizo a m’Baibulo?

  •   Kodi Mungapeze Kuti Thandizo pa Nthawi ya Masautso?

  •   Zimene Ufumu wa Mulungu Ukutichitira Panopa.

 Brenda ananena kuti: “Tsiku lina mnzanga wa kusukulu anabwera pamisonkhano yathu. Anakhala limodzi ndi banja lathu ndipo ndinkawerenga naye limodzi mabuku. Misonkhano itatha, anandiuza kuti anasangalala kwambiri ndi ndemanga zomwe abale ndi alongo ankapereka. Ananenanso kuti waona zosiyana ndi kutchalitchi kwawo chifukwa sakhala ndi mabuku ogwiritsa ntchito pophunzira.”

 Kodi Mukudziwa? Mukafika ku Nyumba ya Ufumu mutha kukhala paliponse ndipo sikuyendetsedwa mbale ya zopereka.

 Mudzalimbikitsidwa ndi anthu omwe mukakumane nawo kumeneko. Baibulo limanena kuti chifukwa chimodzi chimene Akhristu ayenera kusonkhanira limodzi ndi chakuti azitha ‘kulimbikitsana.’ (Aheberi 10:24, 25) Kumeneko, mukakumana ndi anthu amene amakonda kwambiri Mulungu komanso omwe amachita zinthu moganizira ena. Zimenezi ndi zosowa kwambiri m’dzikoli.

 Elisa ananena kuti: “Ndikachoka kuntchito ndimakhala wotopa komanso wokhumudwa. Koma ndikapita ku Nyumba ya Ufumu ndimakumana ndi anthu omwe amandilimbikitsa kwambiri. Misonkhano ikatha, ndimabwerera kunyumba ndili wosangalala moti kukacha ndimapita kuntchito ndilibe nkhawa iliyonse.”

 Kodi Mukudziwa? Padziko lonse pali mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 120,000 yomwe imasonkhana m’malo oposa 60,000. Popeza kuti chiwerengero cha anthu osonkhana  a chikuwonjezekabe, pa avereji Nyumba za Ufumu pafupifupi 1,500 zimamangidwa chaka chilichonse.

a Kuti mupeze malo a misonkhano, pitani pawebusaiti yathu pomwe alemba kuti “Misonkhano ya Mpingo ya Mboni za Yehova” ndipo dinani pomwe alemba kuti “Fufuzani Malo Apafupi.”