Pitani ku nkhani yake

Ndimakopeka ndi Amuna Kapena Akazi Anzanga. Kodi Zimenezi Zikutanthauza Kuti Ndidzayamba Kugonana ndi Amuna Kapena Akazi Anzanga?

Ndimakopeka ndi Amuna Kapena Akazi Anzanga. Kodi Zimenezi Zikutanthauza Kuti Ndidzayamba Kugonana ndi Amuna Kapena Akazi Anzanga?

 Mwina mungadzifunse kuti: “Kodi zimenezi zikutanthauza kuti ndidzayamba kugonana ndi amuna kapena akazi anzanga?” Ayi, si choncho.

 Zoona zake: Nthawi zambiri, kukopeka ndi amuna kapena akazi anzanu kumangochitika kwa kanthawi kochepa pa moyo wa munthu.

 Mtsikana wina dzina lake Lisette, yemwe ali ndi zaka 16, amene pa nthawi ina anakopeka ndi mtsikana mnzake, anazindikira zimenezi. Iye anati: “Kusukulu, pa phunziro la sayansi, ndinaphunzira kuti pakati pa zaka 13 ndi 19, thupi la achinyamata limakhala likusinthasintha. Ndikukhulupirira kuti achinyamata ambiri akanakhala kuti amamvetsa zimene zikuchitika m’thupi mwawo, bwenzi akudziwa kuti kukopeka ndi mkazi kapena mwamuna mnzawo nthawi zina kumangochitika kwa kanthawi basi. Akanadziwa zimenezi, si bwenzi akumaganiza kuti ali m’gulu la anthu amene angagonane ndi amuna kapena akazi anzawo.”

Achinyamata onse amafunika kusankha, kaya kutsatira maganizo oipa a anthu a m’dzikoli pa nkhani ya kugonana kapena kutsatira mfundo za makhalidwe abwino zopezeka m’Mawu a Mulungu

 Nanga bwanji ngati zikuoneka kuti kwa nthawi yaitali, mwakhala mukukopeka ndi amuna kapena akazi anzanu ndipo khalidweli likupitirirabe? Kodi tinganene kuti Mulungu ndi wankhanza chifukwa amauza munthu amene amakopeka ndi amuna kapena akazi anzake kuti apewe kugonana nawo?

 Ngati mwayankha kuti inde pa funso lachiwirili, dziwani kuti maganizo amenewa ndi ochokera kwa anthu amene amaganiza molakwika kuti munthu ali ndi ufulu wogonana ndi aliyense amene iye akufuna. Koma m’Baibulo muli mfundo zosonyeza kuti Mulungu amalemekeza anthu. Iye anatipatsa mwayi woti tizitha kupewa kuchita zimene mtima wathu ukutilimbikitsa kuchita pa nkhani yokhudza kugonana.—Akolose 3:5.

 Zimene Baibulo limanena pa nkhaniyi n’zoti anthu angakwanitse kuzitsatira. Baibulo limalimbikitsa anthu onse kuti “thawani dama,” kaya akhale amene amafuna kugonana amuna kapena akazi okhaokha, kapenanso amuna ndi akazi amene amafuna zachiwerewere. (1 Akorinto 6:18) Ndipo zoona zake n’zakuti anthu mamiliyoni ambirimbiri amene sakopeka ndi amuna kapena akazi anzawo, omwe akufuna kutsatira mfundo za m’Baibulo, amayesetsa kukhala odziletsa ngakhale kuti akukumana ndi mayesero osiyanasiyana. Choncho nawonso anthu amene amakopeka ndi amuna kapena akazi anzawo, amene akufunadi kukondweretsa Mulungu, akhoza kukwanitsa kudziletsa.—Deuteronomo 30:19.