Pitani ku nkhani yake

MFUNDO ZOTHANDIZA MABANJA | KULERA ANA

Ubwino wa Masewera Othandiza Kuganiza

Ubwino wa Masewera Othandiza Kuganiza

 Mawu akuti “masewera othandiza kuganiza” amatanthauza zosangalatsa zimene zimathandiza mwana kuti azichita chidwi komanso kuti azitha kuganiza bwino, ndipo zimenezi zimathandiza mwana kuti akule bwino ndiponso kuti akhale ndi luso logwira ntchito zamanja.

 Zitsanzo za masewerawa ndi monga:

  •   Kujambula

  •   Kuphika

  •   Masewera oyerekezera zinazake

  •   Kuimba

  •   Kumanga tinyumba tadothi

  •   Kuseweretsa makatoni

 M’madera ambiri, ana sachita masewera owathandiza kuganiza, koma m’malomwake amangochita masewera amene anthu ena awakonzera.

 Kodi zimenezi zimachitikanso kwanuko?

 Zimene muyenera kudziwa

  •   Masewera othandiza kuganiza amachititsa ana kuti akule bwino. Angathandize kuti ana akhale athanzi, aziganiza bwino, akhale aluso komanso azicheza bwino ndi anthu ena. Angathandizenso ana kuti azikhala oleza mtima, azisankha bwino zinthu, azikhala odziletsa komanso azichita zinthu bwino akamacheza ndi anthu ena pagulu. Mwachidule tingati masewera othandiza kuganiza angakonzekeretse ana anu kuti asadzavutike akadzakula.

  •   Kugwiritsa ntchito kwambiri zipangizo zamakono kukhoza kukhala koopsa. Munthu akamagwiritsa ntchito kwambiri zipangizo zamakono, zimakhala zovuta kuti azisiye ndipo ana amene amakonda kugwiritsa ntchito kwambiri zipangizozi amanenepa kwambiri komanso amakhala ovuta. Limeneli ndi chenjezo kwa makolo amene amakonda kupatsa ana awo zipangizo zamakono kuti aziseweretsa, n’cholinga choti asamawavutitse.

  •   Kuwakonzera ana zochita, nthawi zina kumakhala ndi mavuto. Makolo akamangokhalira kutengera ana awo kumasewera omwe anthu ena akonza, zimalepheretsa anawo kusewera paokha masewera owathandiza kuganiza komanso kupeza luso linalake.

 Zimene mungachite

  •   Muziwapatsa ana anu mwayi woti azichita masewera owathandiza kuganiza. Ngati n’kotheka, muzilola ana anu kusewera panja n’cholinga choti azolowerane ndi chilengedwe. Muziwalola kuti azichita zinthu zimene amakonda komanso kuti azisewera ndi zidole zimene zingawathandize kuganiza bwino. a

     Zoti muganizire: Kodi masewera othandiza kuganiza, angathandize mwana wanga kukhala ndi makhalidwe komanso maluso ati? Nanga zimenezi zingadzamuthandize bwanji akadzakula?

     Mfundo ya m’Baibulo: “Kuchita masewera olimbitsa thupi n’kopindulitsa.”​—1 Timoteyo 4:8.

  •   Muziika malire a nthawi imene ana anu angamagwiritse ntchito zipangizo zamakono. Muziyamba mwaganiza kaye musanapatse mwana wanu tabuleti, foni kapena kumusiya kuti azionera TV, n’cholinga choti inuyo muzichita zinthu zina. Madokotala a ana amalimbikitsa kuti ana omwe sanakwanitse zaka ziwiri asamaonere zinthu pa TV, pa tabuleti kapena pafoni, pomwe ana a zaka zapakati pa ziwiri ndi 5, azingoonera kwa ola limodzi patsiku. b

     Zoti muganizire: Kodi ndingaike malire otani pa nthawi imene mwana wanga amagwiritsa ntchito foni, tabuleti kapena kuonera TV? Kodi ndizionera naye limodzi? Kodi ndingam’patse zinthu ziti kuti aziseweretsa m’malo moti azigwiritsa ntchito zipangizo zamakono?

     Mfundo ya m’Baibulo: “Samalani kwambiri kuti mmene mukuyendera si monga anthu opanda nzeru, koma ngati anzeru. Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.”​—Aefeso 5:15, 16.

  •   Muziganizira mosamala mmene zinthu zimene mwawakonzera ana anu zingawakhudzire. N’zoona kuti zimenezi zingathandize ana anu kuti akhale ndi luso kapena azichita bwino masewera enaake. Komatu nthawi zina, kukonza zochitika zambiri kumapatsa phuma ana komanso makolo omwe amakhala ndi udindo oonetsetsa kuti anawo apita kumene kuli zochitikazo komanso abwerera kwawo. Choncho mfundo ya pa Aefeso 5:15, 16 yokhudza kugwiritsa ntchito nthawi mwanzeru ikugwiranso ntchito pamenepa.

     Zoti muganizire: Kodi ana athu, timawapanikiza ndi zochitika zimene tawakonzera? Ngati ndi choncho, tingasinthe zinthu ziti?

     Mfundo ya m’Baibulo: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”​—Afilipi 1:10.

a Zidole zambiri zimene makampani amapanga, sizithandiza ana kuti akhale ndi luso lochita zinthu. Koma kuwalola kuti aziseweretsa zidole zosavuta kupanga kapena azichita masewera osavuta monga kumanga tinyumba tadothi kapena kuseweretsa makatoni, kungawathandize kuti azigwiritsa ntchito luso lawo lakuganiza.

b Apa tikunena za kuchita zosangalatsa pa zipangizo zamakono, osati kucheza ndi achibale pa vidiyokomfelensi kapena kuonera mapulogalamu auzimu.