Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NJILA YOPEZELA CIMWEMWE

Ciyembekezo

Ciyembekezo

“Ndikuganizila zokupatsani mtendele osati masoka, kuti mukhale ndi ciyembekezo cabwino ndiponso tsogolo labwino.”Yeremiya 29:11.

“CIYEMBEKEZO . . . N’COFUNIKA KWAMBILI KUTI MUNTHU AKHALE PA UBWENZI WABWINO NA MULUNGU. Ciyembekezo cimathandizanso kwambili kuti munthu athetse maganizo odzipatula na kudziona kuti palibe amene angamuthandize, komanso kuthetsa mantha,” inakamba conco buku yakuti, Hope in the Age of Anxiety.

Baibo imakamba kuti kukhala na ciyembekezo n’kofunika kwambili, ndipo kumatithandiza kupewa kukhala na ziyembekezo zabodza. Lemba la Salimo 146:3 limati: “Musamakhulupilile anthu olemekezeka, kapena mwana wa munthu wina aliyense wocokela kufumbi amene alibe cipulumutso.” M’malo modalila anthu kuti ndiye adzatipulumutsa, timaonetsa kuti ndise anzelu ngati tidalila Mlengi wathu, amene ali na mphamvu zokwanilitsa malonjezo ake onse. Kodi iye watilonjeza ciani? Onani zinthu zotsatilazi.

ZOIPA ZONSE ZIDZATHA; ANTHU OLUNGAMA ADZAKHALA NA MTENDELE WOSATHA: Lemba la Salimo 37:10, 11 limati: “Patsala kanthawi kocepa, woipa sadzakhalakonso . . . Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.” Vesi 29 imaonjezelanso kuti, “Olungama . . . adzakhala mmenemo kwamuyaya.”

NKHONDO ZIDZATHA: “Yehova . . . akuletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.”—Salimo 46:8, 9.

MATENDA, KUVUTIKA, NA IMFA, ZONSE ZIDZATHA: “Cihema ca Mulungu cili pakati pa anthu . . . Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:3, 4.

ALIYENSE ADZAKHALA NA CAKUDYA COKWANILA: “Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.”—Salimo 72:16.

UFUMU WA KHRISTU—BOMA LA PADZIKO LONSE LACILUNGAMO: ‘Yesu Khristu anapatsidwa ulamulilo, ulemelelo, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyana-siyana, olankhula zinenelo zosiyana-siyana azimutumikila. Ulamulilo wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.’—Danieli 7:14.

N’ciani cingatithandize kukhala otsimikiza kuti malonjezo amenewa adzakwanilitsidwa? Pamene Yesu anali padziko, anaonetsa kuti ni Woyenela kukhala Mfumu. Iye anacilitsa odwala, kudyetsa osauka, na kuukitsa akufa. Koma ziphunzitso zake zinali zofunika kwambili, cifukwa zili na mfundo zimene zidzathandiza anthu kukhala amtendele ndi ogwilizana kwamuyaya. Komanso, Yesu anakambilatu zocitika za m’tsogolo, kuphatikizapo zocitika zimene zidzakhala cizindikilo coonetsa kuti mapeto a dzikoli ali pafupi.

MAVUTO, NDIYENO MTENDELE

Yesu anakambilatu kuti cizindikilo ca m’masiku otsiliza sicidzakhala mtendele na citetezo koma mavuto. Cizindikilo ca “mapeto a nthawi ino” cimene anakamba, ciphatikizapo zocitika monga nkhondo pakati pa mitundu, njala, milili, na zivomezi zamphamvu. (Mateyu 24:3, 7; Luka 21:10, 11; Chivumbulutso 6:3-8) Yesu anakambanso kuti: “Cifukwa ca kuwonjezeka kwa kusamvela malamulo, cikondi ca anthu ambili cidzazilala.”—Mateyu 24:12.

Mlembi wina wa Baibo anakambilatu za kuzilala kumeneku, kumene kuonekela bwino m’njila zambili. Pa 2 Timoteyo 3:1-5 timaŵelenga kuti ‘m’masiku otsiliza,’ anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, ndi okonda zosangalatsa. Adzakhalanso odzikuza, ndi aukali. M’mabanja mudzakhala mulibe cikondi cacibadwa, ana sadzamvela makolo awo. Komanso cinyengo m’zipembedzo cidzaculuka.

Mavuto amenewa aonetsa kuti dzikoli lili kumapeto ake. Aonetsanso kuti Ufumu wa mtendele uli pafupi. Ponena za ulosi wa m’masiku otsiliza, Yesu anakambanso motsimikiza kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mateyu 24:14.

Uthenga wabwino umenewu umapeleka cenjezo kwa anthu ocita zoipa, komanso ciyembekezo kwa anthu olungama, kuŵatsimikizila kuti madalitso amene ayembekezela adzafika posacedwa. Kodi mungakonde kudziŵa zambili za madalitso amenewa? Ngati n’conco, onani peji yothela ya magazini ino.