Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NJILA YOPEZELA CIMWEMWE

Thanzi Labwino na Kupilila

Thanzi Labwino na Kupilila

MATENDA AAKULU NA KULEMALA ZIMASINTHA KWAMBILI UMOYO WA MUNTHU. Munthu wina dzina lake Ulf, amene poyamba anali na thanzi labwino, anazizila ziwalo. Iye anati: “N’navutika maganizo kwambili. Mphamvu zanga zonse zinathelatu . . . N’nadzimva kuti ndine ‘woonongekelatu.’”

Zimene zinacitikila Ulf, zimatikumbutsa mfundo yakuti tilibe mphamvu zonse zoteteza thanzi lathu. Ngakhale n’conco, pali zimene tingaciteko kuti titeteze thanzi lathu. Koma bwanji ngati thanzi lathu likufookela-fookela? Kodi izi ziyenela kutisoŵetsa cimwemwe? Monga mmene tidzaonela, yankho ni iyayi. Koma coyamba tiyeni tikambilane mfundo za m’Baibo zimene zingatithandize kukhala na thanzi labwino.

‘MUSAMACITE ZINTHU MOPITILILA MALILE.’ (1 Timoteyo 3:2, 11) Kukhala na cizoloŵezi ca kudya na kumwa kwambili kumaononga thanzi lathu komanso ndalama zathu. “Usakhale pakati pa anthu omwa vinyo kwambili, ndiponso pakati pa anthu odya nyama mosusuka. Cifukwa cidakwa ndiponso munthu wosusuka adzasauka.”—Miyambo 23:20, 21.

MUSADETSE THUPI LANU. “Tiyeni tidziyeletse ndipo ticotse cinthu ciliconse coipitsa thupi kapena mzimu.” (2 Akorinto 7:1) Anthu amaipitsa matupi awo ngati amatafuna kapena kupepa fwaka, komanso ngati akumwa moŵa mwaucidakwa na kuseŵenzetsa amkola bongo. Mwacitsanzo, bungwe lina loona pa zakapewedwe ka matenda lochedwa, U.S. Centers for Disease Control and Prevention linati: “Kupepa fwaka kumabweletsa matenda ndipo kumaononga pafupifupi ziwalo zonse zathupi.”

MUZIONA THUPI LANU NA MOYO WANU KUKHALA MPHATSO YAMTENGO WAPATALI. “Cifukwa ca [Mulungu] tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Machitidwe 17:28) Kuzindikila mfundo imeneyi kumatithandiza kupewa kuika moyo wathu paciswe, kaya tikuseŵenza, kuyendetsa motoka, kapena kucita zosangalatsa. Tisalole cisangalalo ca ka nthawi kutionongela umoyo wathu.

MUSAMAKHAZIKIKE PA ZINTHU ZOKUVUTITSANI MAGANIZO. Zimene timaganiza zimakhudzanso thupi lathu. Conco, yesetsani kupewa kukhala na nkhawa kwambili, mkwiyo wosalamulilika, kaduka, na maganizo ena oononga. Lemba la Salimo 37:8 limati: “Usapse mtima ndipo pewa kukwiya.” Baibo imakambanso kuti: “Musamade nkhawa za tsiku lotsatila, cifukwa tsiku lotsatila lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso.”—Mateyu 6:34.

MUZIGANIZILA ZINTHU ZABWINO. Lemba la Miyambo 14:30 limati: “Mtima wodekha ndiwo moyo wa munthu.” Baibo imakambanso kuti: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ocilitsa.” (Miyambo 17:22) Ngakhale asayansi amakamba zimenezi. Dokota wina ku Scotland, dzina lake Derek Cox anati: “Munthu wacimwemwe amadzadwala matenda ocepa m’tsogolo kusiyana na anthu amene alibe cimwemwe.”

MUZIPILILA. Mofanana ndi Ulf amene tam’chula kuciyambi, nthawi zina tingakumane na mayeselo okhalitsa, cakuti sitingacitile mwina koma kuwapilila. Ngakhale n’conco, tifunika kusankha njila yabwino yowapililila. Ena amasoŵa cocita ndipo amafooka. Zimenezi zingapangitse vutolo kukulila-kulila. Lemba la Miyambo 24:10 limati: “Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zocepa.”

Ena poyamba amavutika maganizo, koma amapilila ndipo amayamba kumvelako bwino. Iwo amavomeleza zinthu zikasintha. Amapezanso njila zowathandiza kupilila. Izi ni zimene Ulf anacita. Iye anakamba kuti pambuyo popemphela mobweleza-bweleza na kusinkha-sinkha mfundo zolimbikitsa za m’Baibo, anayamba “kuona mavuto kukhala mwayi osati zopinga.” Mwacitsanzo, monga mmene zimakhalila ndi anthu ambili amene anakumanapo na mavuto akulu-akulu, nayenso Ulf anaphunzila kukhala wacifundo ndi wokoma mtima. Izi zinam’sonkhezela kuti aziuzako ena uthenga wolimbikitsa wa m’Baibo.

Munthu wina amene anavutika kwambili ni Steve. Ali na zaka 15, anagwa mu mtengo ndipo ziwalo zake zinazizila kuyambila m’khosi mpaka ku mendo. Atafika zaka 18, manja ake anakhalanso bwino. Kenako anapita ku yuniveziti. Kumeneko umoyo wake unasokonezeka kwambili cakuti anayamba kumwa amkola bongo, kumwa moŵa mwaucidakwa, na kucita zaciwelewele. Anafika potailatu mtima. Koma atayamba kuphunzila Baibo, anayamba kuona zinthu mosiyana ndipo zinamuthandiza kugonjetsa zizoloŵezi zake zoipa. Iye anati: “Kwa nthawi yaitali n’nali kudziona kuti ndine wacabe-cabe. Koma lomba umoyo wanga ni wamtendele, wacimwemwe, ndi wokhutila.”

Zimene anakamba Steve na Ulf, zitikumbutsa mau a pa Salimo 19:7, 8, amene amati: “Cilamulo ca Yehova ndi cangwilo, cimabwezeletsa moyo. . . . Malamulo ocokela kwa Yehova ndi olungama, amasangalatsa mtima. Cilamulo ca Yehova ndi coyela, cimatsegula maso.”