Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NJILA YOPEZELA CIMWEMWE

Kukhutila Komanso Kupatsa

Kukhutila Komanso Kupatsa

ANTHU AMBILI AMAONA KUTI MUNTHU AMAKHALA WACIMWEMWE AKAKHALA NA CUMA CAMBILI. Cifukwa ca maganizo amene aya, anthu ofika mamiliyoni amagwila nchito ma awazi ambili kuti apeze ndalama zoculuka. Kodi kukhala na ndalama komanso katundu wambili kumabweletsa cimwemwe cokhalitsa? Kodi zocitika zimaonetsa ciani?

Malinga n’zimene linakamba buku lakuti Journal of Happiness Studies, munthu amakhala wacimwemwe akakhala na zinthu zofunikila kweni-kweni mu umoyo, monga cakudya, vovala na pogona. Kukhala na ndalama zambili sikulengetsa munthu kukhala wacimwemwe. Koma sikuti ndalama ndiye vuto. Nkhani ina m’magazini yochedwa Monitor on Psychology inati: Vuto ni “kufunitsitsa [ndalama] n’kumene kumalengetsa munthu kusakhala wacimwemwe.” Mau amenewa ni olingana kwambili na uphungu wa m’Baibo umene unalembewa zaka pafupi-fupi 2000 zapitazo, wakuti: “Pakuti kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo pokulitsa cikondi cimeneci, ena . . . adzibweletsela zopweteka zambili pathupi lawo.” (1 Timoteyo 6:9, 10) Kodi zopweteka kapena kuti zoŵaŵa zimenezi zingaphatikizepo ciani?

NKHAWA NA KUSOŴA TULO POFUNA KUTETEZA CUMA “Wotumikila munthu wina amagona tulo tokoma ngakhale adye zocepa kapena zambili. Koma zambili zimene munthu wolemela amakhala nazo zimamulepheletsa kugona.”—Mlaliki 5:12.

KUKHUMUDWA NGATI SUNACIPEZE CIMWEMWE CIMENE UNALI KUYEMBEKEZELA. M’mau ena tingakambe kuti munthu wotelo amakhumudwa cifukwa ca kusakhutila na ndalama zimene ali nazo. Kukonda ndalama kuli monga njala imene siikutha. Baibo imati: “Munthu wokonda siliva sakhutila ndi siliva, ndipo wokonda cuma sakhutila ndi phindu limene amapeza.” (Mlaliki 5:10) Komanso, kusakhutila kungacititse munthu kunyalanyaza zinthu zofunika kwambili zimene zimacititsa munthu kukhala wacimwemwe, monga kukhala na nthawi yoceza na banja, mabwenzi, komanso kucita zinthu zauzimu.

CISONI NA KUVUTIKA MAGANIZO CUMA CIKASILA. ‘Usamadzitopetse ndi nchito kuti upeze cuma. Leka kudzidalila kuti ndiwe womvetsa zinthu. Kodi maso ako amayang’anitsitsa cuma, pomwe ico sicicedwa kucoka? Cifukwa ndithu, cimadzipangila mapiko ngati a ciwombankhanga n’kuuluka.’—Miyambo 23:4, 5.

MAKHALIDWE OTHANDIZA MUNTHU KUKHALA WACIMWEMWE

KUKHUTILA. “Sitinabwele ndi kanthu m’dziko, ndipo sitingatulukemo ndi kanthu. Conco, pokhala ndi cakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutila ndi zinthu zimenezi.” (1 Timoteyo 6:7, 8) Anthu amene ni okhutila, nthawi zambili sadandaula ndipo zimenezi zimawathandiza kupewa kaduka. Cifukwa cakuti salaka-laka zinthu zimene sangakwanitse, sakhala na nkhawa kwambili komanso savutika maganizo.

KUPATSA. “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” (Machitidwe 20:35) Anthu opatsa amakhala acimwemwe cifukwa amapangitsa ena kukhala acimwemwe, ngakhale kuti angoŵapatsa nthawi cabe kapena kuŵacitila zinthu zina zocepa. Cifukwa cokhala opatsa, nthawi zambili amapeza zoculuka zimene sakanagula na ndalama—anthu amawakonda, na kuŵalemekeza, ndipo amakhala na mabwenzi abwino amene naonso amapatsa moolowa manja!—Luka 6:38.

KUIKA ANTHU PATSOGOLO, ZINTHU PAMBUYO. “Ndi bwino kudya zamasamba koma pali cikondi, kusiyana ndi kudya nyama ya ng’ombe yamphongo yodyetsedwa bwino pali cidani.” (Miyambo 15:17) Pali mfundo yanji? Kukhala paubwenzi wabwino na ena n’kofunika kwambili kuposa cuma coculuka. Monga mmene tidzaonela, cikondi n’cofunika ngako kuti munthu akhale wacimwemwe.

Mayi wina ku South America dzina lake Sabina, anaona kuti mfundo za m’Baibo n’zothandiza. Mwamuna wake atamusiya, Sabina anali kuvutika kupeza zofunikila mu umoyo wake ndi ana ake acitsikana aŵili. Anali kugwila nchito ziŵili ndipo tsiku lililonse anali kuuka 4 koloko m’maŵa. Olo kuti anali wotangwanika kwambili, anayamba kuphunzila Baibo. Kodi panakhala zotulukapo zotani?

Sikuti ndalama zake zinawonjezeka. Koma kaonedwe kake ka zinthu mu umoyo ndiye kanasintha kwambili. Mwacitsanzo: Anayamba kukhala wacimwemwe cifukwa cokhutilitsa zosoŵa zake zauzimu. (Mateyu 5:3) Anapeza mabwenzi abwino pakati pa okhulupilila anzake. Anapezanso cimwemwe cimene cimabwela cifukwa cokhala wopatsa mwa kuuzako ena zimene anaphunzila.

Baibo imati: “Nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca nchito zake.” (Mateyu 11:19) Mogwilizana na mfundo imeneyi, kukhala wokhutila, ndi wopatsa, komanso kuona anthu kukhala ofunika kuposa zinthu, ndiye zimathandiza munthu kukhala wacimwemwe.