Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mawu Anu ni Osatha

Mawu Anu ni Osatha

Mawu a Nyimbo:

  1. 1. Anayamikila

    Mocokela mumtima

    Cikondi ca Yehova

    Poŵadziŵitsa za iye.

    Mwaŵapatsa dzina

    Iwo ni mboni zanu.

    Alengeze za inu

    Kuti ise tikudziŵeni.

    Iwo anakondwa

    Kuteteza mawu anu.

    Analemba zokhudza inu

    Kuti’se tikudziŵeni.

    (KOLASI)

    Mawu anu Yehova

    Indedi ni osatha.

    Uthenga wabwino

    Umanilimbitsa.

    Nidzasungadi mawu anu.

  2. 2. Ena sanali kufuna

    Kuti mudziŵike.

    Anthu anu anayesa

    Kuteteza mawu anu.

    Iwo sanayope kuphedwa

    Poteteza mawu anu.

    Anali olimba

    M’cikhulupililo,

    Anacitila umboni.

    (KOLASI)

    Mawu anu ni a muyaya.

    Mfundo zanu n’zozama.

    Uthenga wabwino

    Umanilimbitsa.

    Nidzasungadi mawu anu.

  3. 3. Mwatiphunzitsa za dzina lanu

    Kuti ndimwe Yehova.

    Mudzakwanilitsa

    Zonse mwalonjeza.

    Tidzakutamandanibe.

    (KOLASI)

    Mawu anu ni osatha.

    Mfundo zanu n’zozama.

    Uthenga wabwino

    Umanilimbitsa.

    Nidzasungadi mawu anu

    Nthawi zonse.