Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Buku la Masalimo

Machaputala

Mitu

  • 1

    • Kusiyanitsa njira ziwiri

      • Wowerenga chilamulo cha Mulungu amakhala wosangalala (2)

      • Olungama ali ngati mtengo wobala zipatso (3)

      • Oipa ali ngati mankhusu amene amauluzika ndi mphepo (4)

  • 2

    • Yehova ndi wodzozedwa wake

      • Yehova adzaseka mitundu ya anthu (4)

      • Yehova anasankha mfumu yake (6)

      • Lemekezani mwanayo (12)

  • 3

    • Kudalira Mulungu ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto

      • ‘Nʼchifukwa chiyani adani achuluka chonchi?’ (1)

      • “Chipulumutso chimachokera kwa Yehova” (8)

  • 4

    • Pemphero losonyeza kuti tikudalira Mulungu

      • “Ngati mwakwiya, musachimwe” (4)

      • ‘Ndidzagona mwamtendere nʼkupeza tulo’ (8)

  • 5

    • Yehova ndi malo othawirako a anthu olungama

      • Mulungu amadana ndi zoipa (4, 5)

      • “Ndinu wachilungamo, nditsogolereni” (8)

  • 6

    • Kupempha kuti atikomere mtima

      • Akufa satamanda Mulungu (5)

      • Mulungu amamva tikamupempha kuti atikomere mtima (9)

  • 7

    • Yehova ndi Woweruza wolungama

      • “Ndiweruzeni inu Yehova” (8)

  • 8

    • Ulemerero wa Mulungu komanso ulemu wa munthu

      • “Dzina lanu ndi lalikulu!” (1, 9)

      • “Munthu ndi ndani kuti muzimuganizira?” (4)

      • Munthu munamuveka ulemerero ngati chisoti chachifumu (5)

  • 9

    • Kulengeza ntchito zodabwitsa za Mulungu

      • Yehova ndi malo othawirako otetezeka (9)

      • Anthu odziwa dzina la Mulungu adzamukhulupirira (10)

  • 10

    • Yehova amathandiza anthu ovutika

      • Anthu oipa amanena modzikuza kuti: “Kulibe Mulungu” (4)

      • Anthu ovutika amayangʼana kwa Yehova (14)

      • “Yehova ndi Mfumu mpaka muyaya” (16)

  • 11

    • Kuthawira kwa Yehova

      • “Yehova ali mʼkachisi wake wopatulika” (4)

      • Mulungu amadana ndi aliyense wokonda chiwawa (5)

  • 12

    • Yehova amanyamuka nʼkuchitapo kanthu

      • Mawu a Mulungu ndi oyera (6)

  • 13

    • Kuyembekezera chipulumutso cha Yehova

      • “Mpaka liti, inu Yehova?” (1, 2)

      • Yehova amapereka mphoto yaikulu (6)

  • 14

    • Zimene opusa amachita

      • “Kulibe Yehova” (1)

      • “Palibe aliyense amene akuchita zabwino” (3)

  • 15

    • Ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti ya Yehova?

      • Amalankhula zoona mumtima mwake (2)

      • Iye sanena miseche (3)

      • Amakwaniritsa zimene analonjeza ngakhale kuti ndi zopweteka kwa iye (4)

  • 16

    • Zabwino zonse zimachokera kwa Yehova

      • “Yehova ndi gawo langa” (5)

      • ‘Maganizo amumtima mwanga amandiuza zoyenera kuchita’ (7)

      • ‘Yehova ali kudzanja langa lamanja’ (8)

      • “Simudzandisiya mʼManda” (10)

  • 17

    • Pemphero lopempha chitetezo

      • “Mwafufuza mtima wanga” (3)

      • “Mumthunzi wa mapiko anu” (8)

  • 18

    • Kutamanda Mulungu chifukwa cha chipulumutso chake

      • “Yehova ndi thanthwe langa” (2)

      • Yehova ndi wokhulupirika kwa okhulupirika (25)

      • Njira ya Mulungu ndi yangwiro (30)

      • “Kudzichepetsa kwanu nʼkumene kumandikweza” (35)

  • 19

    • Zimene Mulungu analenga komanso chilamulo zimachitira umboni

      • “Zinthu zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu” (1)

      • Chilamulo changwiro cha Mulungu chimabwezeretsa mphamvu (7)

      • “Machimo amene ndachita mosadziwa” (12)

  • 20

    • Kupulumutsidwa kwa mfumu yodzozedwa ya Mulungu

      • Ena amadalira magaleta ndi mahatchi, “koma ife timadalira dzina la Yehova” (7)

  • 21

    • Mfumu imene imadalira Yehova idzadalitsidwa

      • Mfumu inapatsidwa moyo wautali  (4)

      • Adani a Mulungu adzagonjetsedwa (8-12)

  • 22

    • Kuchoka mʼmavuto nʼkuyamba kutamanda Mulungu

      • “Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?” (1)

      • “Akuchita maere pa zovala zanga” (18)

      • Tamandani Mulungu mumpingo (22, 25)

      • Dziko lonse lilambire Mulungu (27)

  • 23

    • “Yehova ndi Mʼbusa wanga”

      • “Sindidzasowa kanthu” (1)

      • “Amanditsitsimula” (3)

      • “Kapu yanga ndi yodzaza bwino” (5)

  • 24

    • Mfumu yaulemerero yalowa mʼmageti

      • ‘Dziko lapansi ndi la Yehova’ (1)

  • 25

    • Pemphero lopempha kutsogoleredwa komanso kukhululukidwa

      • “Ndiphunzitseni njira zanu” (4)

      • “Ubwenzi wolimba ndi Yehova” (14)

      • “Mundikhululukire machimo anga onse” (18)

  • 26

    • Kuchita zinthu mokhulupirika

      • “Ndifufuzeni, Inu Yehova” (2)

      • Kupewa kugwirizana ndi anthu oipa (4, 5)

      • ‘Ndidzayenda mozungulira guwa lansembe la Mulungu’ (6)

  • 27

    • Yehova amateteza moyo wanga

      • Kuyamikira kachisi wa Mulungu (4)

      • Yehova amatisamalira ngakhale makolo athu atatisiya (10)

      • “Yembekezera Yehova” (14)

  • 28

    • Mulungu anayankha pemphero la amene analemba salimo

      • ‘Yehova ndi mphamvu yanga komanso chishango changa’ (7)

  • 29

    • Mawu a Yehova ndi amphamvu

      • Lambirani Mulungu mutavala zovala zopatulika zokongola (2)

      • “Mulungu waulemerero akugunda ngati bingu” (3)

      • Yehova amapatsa anthu ake mphamvu (11)

  • 30

    • Kulira kunasanduka chisangalalo

      • Mulungu amakomera mtima anthu kwa moyo wawo wonse (5)

  • 31

    • Kuthawira kwa Yehova

      • “Ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu” (5)

      • “Yehova Mulungu wa choonadi” (5)

      • Ubwino wa Mulungu ndi wochuluka (19)

  • 32

    • Osangalala ndi anthu amene machimo awo akhululukidwa

      • “Ndinaulula tchimo langa kwa inu” (5)

      • Mulungu amakupatsani nzeru (8)

  • 33

    • Tamandani Mlengi

      • “Muimbireni nyimbo yatsopano” (3)

      • Zinthu zinalengedwa ndi mawu komanso mzimu wa Yehova (6)

      • Wosangalala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova (12)

      • Diso la Yehova limayangʼana anthu amene amamuopa (18)

  • 34

    • Yehova amapulumutsa atumiki ake

      • “Tiyeni tonse tikweze dzina lake” (3)

      • Mngelo wa Yehova amateteza (7)

      • “Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino” (8)

      • ‘Palibe fupa lake ngakhale limodzi limene linathyoledwa’ (20)

  • 35

    • Pemphero lopempha kupulumutsidwa kwa adani

      • Adani athamangitsidwe (5)

      • Kutamanda Mulungu pakati pa anthu ambiri (18)

      • Kudedwa popanda chifukwa (19)

  • 36

    • Chikondi chokhulupirika cha Mulungu ndi chamtengo wapatali

      • Woipa saopa Mulungu (1)

      • Mulungu ndi kasupe wa moyo (9)

      • “Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, timaona kuwala” (9)

  • 37

    • Anthu amene amadalira Yehova zinthu zimawayendera bwino

      • Usakhumudwe chifukwa cha anthu oipa (1)

      • “Uzisangalala chifukwa cha Yehova” (4)

      • “Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako” (5)

      • “Ofatsa adzalandira dziko lapansi” (11)

      • Olungama sadzasowa chakudya (25)

      • Olungama adzakhala padziko lapansi kwamuyaya (29)

  • 38

    • Pemphero la munthu wovutika amene walapa

      • “Ndili ndi nkhawa komanso chisoni chachikulu” (6)

      • Yehova amayankha anthu amene amamuyembekezera (15)

      • “Tchimo langa linkandisowetsa mtendere” (18)

  • 39

    • Moyo ndi waufupi

      • Munthu ali ngati mpweya (5, 11)

      • “Musanyalanyaze misozi yanga” (12)

  • 40

    • Kuyamikira Mulungu amene palibe angafanane naye

      • Ntchito za Mulungu ndi zosawerengeka (5)

      • Mulungu sasangalala ndi nsembe zokha (6)

      • ‘Ndimasangalala kuchita zimene mumafuna’ (8)

  • 41

    • Pemphero la munthu amene akudwala pabedi lake

      • Mulungu amasamalira anthu amene akudwala (3)

      • Kuukiridwa ndi mnzanga wapamtima (9)

  • 42

    • Kutamanda Mulungu yemwe ndi Mpulumutsi Wamkulu

      • Kulakalaka Mulungu ngati mmene mbawala imalakalakira madzi (1, 2)

      • “Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga?” (5, 11)

      • “Yembekezera Mulungu” (5, 11)

  • 43

    • Mulungu yemwe ndi Woweruza amapulumutsa

      • ‘Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu’ (3)

      • “Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga?” (5)

      • “Yembekezera Mulungu” (5)

  • 44

    • Pemphero lopempha thandizo

      • “Ndi inu amene munatipulumutsa” (7)

      • Takhala ngati “nkhosa zokaphedwa” (22)

      • “Nyamukani kuti mutithandize!” (26)

  • 45

    • Ukwati wa mfumu yodzozedwa

      • Mawu osangalatsa (2)

      • “Mulungu ndi mpando wako wachifumu mpaka muyaya” (6)

      • Mfumu idzalakalaka kukongola kwa mkwatibwi (11)

      • Ana anu adzakhala akalonga padziko lonse lapansi (16)

  • 46

    • “Mulungu ndi pothawira pathu”

      • Ntchito zodabwitsa za Mulungu (8)

      • Mulungu akuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi (9)

  • 47

    • Mulungu ndi Mfumu yolamulira dziko lonse lapansi

      • ‘Yehova ndi wochititsa mantha’ (2)

      • Imbani nyimbo zotamanda Mulungu (6, 7)

  • 48

    • Ziyoni ndi mzinda wa Mfumu Yaikulu

      • Anthu padziko lonse amasangalala ndi phiri la Ziyoni (2)

      • Yenderani mzindawo ndi nsanja zake (11-13)

  • 49

    • Kudalira chuma nʼkupusa

      • Palibe munthu amene angawombole mnzake (7, 8)

      • Mulungu amawombola munthu ku Manda (15)

      • Chuma sichingapulumutse munthu ku imfa (16, 17)

  • 50

    • Mulungu amaweruza okhulupirika ndi oipa

      • Kuchita pangano ndi Mulungu pogwiritsa ntchito nsembe (5)

      • “Mulungu ndi Woweruza” (6)

      • Nyama zonse ndi za Mulungu (10, 11)

      • Mulungu amaulula anthu oipa (16-21)

  • 51

    • Pemphero la munthu wolapa

      • Wochimwa kuchokera pamene mayi anatenga pakati (5)

      • ‘Ndiyeretseni ku machimo anga’ (7)

      • “Lengani mtima wolungama mkati mwanga” (10)

      • Mulungu amasangalala ndi kudzimvera chisoni mumtima (17)

  • 52

    • Kukhulupirira chikondi cha Mulungu chokhulupirika

      • Chenjezo kwa anthu odzitama chifukwa chochita zoipa (1-5)

      • Anthu osaopa Mulungu amadalira chuma chawo (7)

  • 53

    • Zimene anthu opusa amachita

      • “Kulibe Yehova” (1)

      • “Palibe aliyense amene akuchita zabwino” (3)

  • 54

    • Pemphero lopempha kuthandizidwa pa nthawi youkiridwa ndi adani

      • “Mulungu ndi amene amandithandiza” (4)

  • 55

    • Pemphero loperekedwa pa nthawi imene waukiridwa ndi mnzako

      • Kunyozedwa ndi mnzako wapamtima (12-14)

      • “Umutulire Yehova nkhawa zako” (22)

  • 56

    • Pemphero loperekedwa pa nthawi yozunzidwa

      • “Ine ndimadalira Mulungu” (4)

      • “Misozi yanga mʼthumba lanu lachikopa” (8)

      • “Kodi munthu wamba angandichite chiyani?” (4, 11)

  • 57

    • Kupempha kuchitiridwa chifundo

      • Kuthawira pansi pa mapiko a Mulungu (1)

      • Adani adzagwera mumsampha wawo womwe (6)

  • 58

    • Pali Mulungu amene amaweruza dziko lapansi

      • Pemphero lopempha kuti anthu oipa alangidwe (6-8)

  • 59

    • Mulungu ndi chishango komanso malo othawirako

      • ‘Musasonyeze chifundo kwa anthu achiwembu’ (5)

      • “Ndidzaimba za mphamvu zanu” (16)

  • 60

    • Mulungu amagonjetsa adani

      • Chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake (11)

      • “Mulungu adzatipatsa mphamvu” (12)

  • 61

    • Mulungu ndi nsanja yolimba imene imateteza kwa adani

      • “Ndidzakhala mlendo mutenti yanu” (4)

  • 62

    • Chipulumutso chenicheni chimachokera kwa Mulungu

      • “Ndikuyembekezera Mulungu modekha” (1, 5)

      • ‘Mukhuthulireni Mulungu zonse zamumtima mwanu’ (8)

      • Anthu ali ngati mpweya (9)

      • Musamadalire chuma (10)

  • 63

    • Kulakalaka Mulungu

      • “Chikondi chanu chokhulupirika nʼchabwino kuposa moyo” (3)

      • “Ndakhutira ndi gawo labwino” (5)

      • Ndimaganizira mozama za Mulungu usiku (6)

      • ‘Ndimakhala pafupi kwambiri ndi Mulungu’ (8)

  • 64

    • Nditetezeni ku ziwembu zobisika

      • “Mulungu adzawalasa” (7)

  • 65

    • Mulungu amasamalira dziko lapansi

      • “Wakumva pemphero” (2)

      • ‘Wosangalala ndi munthu amene inu mwamusankha’ (4)

      • Mulungu ali ndi zinthu zambiri zabwino (11)

  • 66

    • Ntchito zochititsa mantha za Mulungu

      • ‘Bwerani mudzaone ntchito za Mulungu’ (5)

      • “Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa inu” (13)

      • Mulungu amamva mapemphero (18-20)

  • 67

    • Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi anthu adzaopa Mulungu

      • Njira za Mulungu zidzadziwika (2)

      • ‘Mitundu yonse ya anthu itamande Mulungu’ (3, 5)

      • “Mulungu adzatidalitsa” (6, 7)

  • 68

    • ‘Adani a Mulungu amwazikeʼ

      • “Bambo wa ana amasiye” (5)

      • Mulungu amapereka nyumba kwa anthu amene alibe wowathandiza (6)

      • Akazi amene akulengeza uthenga wabwino (11)

      • Mphatso za amuna (18)

      • ‘Yehova amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku’ (19)

  • 69

    • Pemphero lopempha kupulumutsidwa

      • “Kudzipereka kwanga panyumba yanu kuli ngati moto umene ukuyaka mumtima mwanga” (9)

      • “Ndiyankheni mwamsanga” (17)

      • “Anandipatsa vinyo wosasa kuti ndimwe” (21)

  • 70

    • Anapempha kuti amuthandize mwamsanga

      • “Ndithandizeni mwamsanga” (5)

  • 71

    • Achikulire amadalira Mulungu

      • Kudalira Mulungu kuyambira pa unyamata (5)

      • “Pa nthawi imene mphamvu zanga zatha” (9)

      • ‘Mulungu wakhala akundiphunzitsa kuyambira ndili mnyamata’ (17)

  • 72

    • Ulamuliro wamtendere wa mfumu ya Mulungu

      • “Wolungama zinthu zidzamuyendera bwino” (7)

      • Adzakhala ndi anthu omugonjera kuchokera kunyanja kukafika kunyanja (8)

      • Adzawapulumutsa kuti asachitiridwe zachiwawa (14)

      • Padziko lapansi padzakhala tirigu wochuluka (16)

      • Dzina la Mulungu lidzatamandidwa mpaka kalekale (19)

  • 73

    • Munthu woopa Mulungu anayambanso kuona zinthu moyenera

      • “Mapazi anga anangotsala pangʼono kusochera” (2)

      • “Ndinkavutika tsiku lonse” (14)

      • ‘Mpaka pamene ndinalowa mʼmalo opatulika a Mulungu’ (17)

      • Anthu oipa ali pamalo oterera (18)

      • Kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino (28)

  • 74

    • Pemphero lopempha kuti Mulungu akumbukire anthu ake

      • Anakumbukira zimene Mulungu anachita kuti awapulumutse (12-17)

      • “Kumbukirani mmene adani akunyozera” (18)

  • 75

    • Mulungu amaweruza mwachilungamo

      • Anthu oipa adzamwa zamʼkapu ya Yehova (8)

  • 76

    • Mulungu wagonjetsa adani a Ziyoni

      • Mulungu amapulumutsa anthu ofatsa (9)

      • Adani onyada adzachititsidwa manyazi (12)

  • 77

    • Pemphero la pa nthawi yamavuto

      • Kuganizira mozama ntchito za Mulungu (11, 12)

      • ‘Kodi pali mulungu winanso wamkulu amene angafanane ndi inu Mulungu?’ (13)

  • 78

    • Mulungu ankasamalira Aisiraeli koma iwo analibe chikhulupiriro

      • Mudzauze mʼbadwo wamʼtsogolo (2-8)

      • “Sanakhulupirire Mulungu” (22)

      • “Tirigu wochokera kumwamba” (24)

      • “Ankachititsa kuti Woyera wa Isiraeli amve chisoni” (41)

      • Kuchoka ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa (43-55)

      • ‘Iwo anapitiriza kuyesa Mulungu’ (56)

  • 79

    • Pemphero la pa nthawi imene anthu a mitundu ina anaukira anthu a Mulungu

      • ‘Anthu akutinyoza’ (4)

      • ‘Tithandizeni chifukwa cha dzina lanu’ (9)

      • “Bwezerani anthu oyandikana nafe maulendo 7” (12)

  • 80

    • Anapempha Mʼbusa wa Isiraeli kuti awabwezeretse mwakale

      • “Inu Mulungu, tibwezeretseni mwakale” (3)

      • Isiraeli ali ngati mtengo wampesa wa Mulungu (8-15)

  • 81

    • Anawalimbikitsa kuti akhale omvera

      • Musalambire milungu yachilendo (9)

      • ‘Zikanakhala bwino mukanamvera’ (13)

  • 82

    • Anapempha chiweruzo cholungama

      • Mulungu akuweruza “pakati pa milungu” (1)

      • “Tetezani anthu onyozeka” (3)

      • “Inu ndinu milungu” (6)

  • 83

    • Pemphero la pa nthawi imene adani akuwaukira

      • “Inu Mulungu, musakhale chete” (1)

      • Adani akhale ngati mapesi amene amauluka ndi mphepo (13)

      • Dzina la Mulungu ndi Yehova (18)

  • 84

    • Kulakalaka chihema chachikulu cha Mulungu

      • Mlevi ankalakalaka atakhala ngati mbalame (3)

      • “Tsiku limodzi mʼmabwalo anu” (10)

      • “Mulungu ndi dzuwa ndiponso chishango” (11)

  • 85

    • Pemphero lopempha kubwezeretsedwa

      • Mulungu adzanena za mtendere kwa anthu ake okhulupirika (8)

      • Chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika zidzakumana (10)

  • 86

    • Palibe mulungu amene angafanane ndi Yehova

      • Yehova ndi wokonzeka kukhululuka (5)

      • Mitundu yonse ya anthu idzalambira Yehova (9)

      • ‘Ndilangizeni za njira yanu’ (11)

      • “Ndithandizeni kuti ndiziopa dzina lanu ndi mtima wonse” (11)

  • 87

    • Ziyoni ndi mzinda wa Mulungu woona

      • Amene anabadwira mu Ziyoni (4-6)

  • 88

    • Pemphero lopempha kuti atetezedwe ku imfa

      • “Moyo wanga wayandikira ku Manda” (3)

      • ‘Mʼmawa uliwonse ndimapemphera kwa inu’ (13)

  • 89

    • Imbani za chikondi chokhulupirika cha Yehova

      • Anachita pangano ndi Davide (3)

      • Mbadwa za Davide zidzakhalapo mpaka kalekale (4)

      • Wodzozedwa wa Mulungu amanena kuti Mulungu ndi “Bambo” ake (26)

      • Nʼzotsimikizirika kuti pangano la Davide lidzakwaniritsidwa (34-37)

      • Munthu sangapulumutse moyo wake ku mphamvu ya Manda (48)

  • 90

    • Mulungu wamuyaya komanso munthu amene amakhala nthawi yochepa

      • Zaka 1,000 zili ngati dzulo (4)

      • Munthu amangokhala ndi moyo zaka 70 kapena 80 (10)

      • “Tiphunzitseni mmene tingagwiritsire ntchito bwino moyo wathu” (12)

  • 91

    • Kutetezedwa mʼmalo obisika a Mulungu

      • Kupulumutsidwa mumsampha wa wosaka mbalame (3)

      • Kuthawira pansi pa mapiko a Mulungu (4)

      • Kukhala otetezeka ngakhale anthu masauzande atagwa (7)

      • Adzalamula angelo kuti akuteteze (11)

  • 92

    • Yehova ndi wokwezeka mpaka kalekale

      • Ntchito zake ndi zazikulu komanso maganizo ake ndi ozama kwambiri (5)

      • ‘Olungama zinthu zidzawayendera bwino ngati mtengo’ (12)

      • Okalamba zinthu zidzapitirizabe kuwayendera bwino (14)

  • 93

    • Ulamuliro waulemerero wa Yehova

      • “Yehova wakhala Mfumu!” (1)

      • ‘Zikumbutso zanu ndi zodalirika kwambiri’ (5)

  • 94

    • Pemphero lopempha kuti Mulungu abwezere adani

      • “Kodi anthu oipa adzapitiriza kusangalala mpaka liti?” (3)

      • Kulangizidwa ndi Ya nʼkosangalatsa (12)

      • Mulungu sadzataya anthu ake (14)

      • “Akuyambitsa mavuto pogwiritsa ntchito malamulo” (20)

  • 95

    • Kulambira koona komanso kumvera

      • “Lero anthu inu mukamvera mawu ake” (7)

      • “Musaumitse mitima yanu” (8)

      • “Sadzalowa mumpumulo wanga” (11)

  • 96

    • “Imbirani Yehova nyimbo yatsopano”

      • Yehova ndi woyenera kutamandidwa kwambiri (4)

      • Milungu ya anthu a mitundu ina ndi yopanda pake (5)

      • Lambirani Mulungu mutavala zovala zokongola komanso zopatulika (9)

  • 97

    • Yehova ndi wokwezeka kuposa milungu ina yonse

      • “Yehova wakhala Mfumu!” (1)

      • Muzikonda Yehova nʼkumadana ndi zoipa (10)

      • Kuwala kwaunikira olungama (11)

  • 98

    • Yehova ndi Mpulumutsi komanso Woweruza wolungama

      • Chipulumutso cha Yehova chadziwika (2, 3)

  • 99

    • Yehova ndi Mfumu yoyera

      • Wakhala pampando wachifumu pamwamba pa akerubi (1)

      • Mulungu amene amakhululuka komanso kupereka chilango (8)

  • 100

    • Kuyamikira Mlengi

      • “Tumikirani Yehova mokondwera” (2)

      • ‘Mulungu ndi amene anatipanga’ (3)

  • 101

    • Wolamulira wochita zinthu mokhulupirika

      • ‘Wodzikweza sindidzamulekerera’ (5)

      • “Ndidzayangʼana anthu okhulupirika” (6)

  • 102

    • Pemphero la munthu woponderezedwa amene ali pa mavuto

      • “Ndili ngati mbalame imene ili yokhayokha” (7)

      • “Masiku a moyo wanga ali ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka” (11)

      • “Yehova adzamanganso Ziyoni” (16)

      • Yehova adzakhalapo kwamuyaya (26, 27)

  • 103

    • “Moyo wanga utamande Yehova”

      • Mulungu amatiikira kutali machimo athu (12)

      • Mulungu amasonyeza chifundo ngati bambo (13)

      • Mulungu amakumbukira kuti ndife fumbi (14)

      • Mpando wachifumu wa Yehova komanso ufumu wake (19)

      • Angelo amachita zimene Mulungu wanena (20)

  • 104

    • Kutamanda Mulungu chifukwa cha zinthu zodabwitsa zimene analenga

      • Dziko lapansi lidzakhalapo kwamuyaya (5)

      • Vinyo komanso chakudya zimasangalatsa munthu (15)

      • “Ntchito zanu ndi zochuluka” (24)

      • “Mukachotsa mzimu wawo, zimafa” (29)

  • 105

    • Zimene Yehova anachitira anthu ake posonyeza kuti ndi wokhulupirika

      • Mulungu amakumbukira pangano lake (8-10)

      • “Musakhudze odzozedwa anga” (15)

      • Mulungu anagwiritsa ntchito Yosefe amene anali kapolo (17-22)

      • Zozizwitsa zimene Mulungu anachita ku Iguputo (23-36)

      • Ulendo wa Aisiraeli wochoka ku Iguputo (37-39)

      • Mulungu anakumbukira zimene analonjeza Abulahamu (42)

  • 106

    • Aisiraeli sanasonyeze kuyamikira

      • Anaiwala mwamsanga zimene Mulungu anachita (13)

      • Anasinthanitsa ulemerero wa Mulungu ndi chifaniziro cha mwana wangʼombe (19, 20)

      • Sankakhulupirira malonjezo a Mulungu (24)

      • Anayamba kulambira Baala (28)

      • Ankapereka nsembe ana awo kwa ziwanda (37)

  • 107

    • Yamikani Mulungu chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa

      • Anawayendetsa mʼnjira yabwino (7)

      • Anathetsa ludzu komanso njala ya anthu (9)

      • Anawatulutsa mumdima (14)

      • Ankalamula kuti achire (20)

      • Amateteza anthu osauka kuti asaponderezedwe (41)

  • 108

    • Pemphero lopempha kuti awathandize kugonjetsa adani

      • Chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake (12)

      • “Mulungu adzatipatsa mphamvu” (13)

  • 109

    • Pemphero la munthu amene ali pa mavuto

      • ‘Udindo wake utengedwe ndi munthu wina’ (8)

      • Mulungu amaima pafupi ndi munthu wosauka (31)

  • 110

    • Mfumu komanso wansembe ngati Melekizedeki

      • ‘Ukalamulire pakati pa adani ako’ (2)

      • Achinyamata odzipereka ali ngati mame (3)

  • 111

    • Tamandani Yehova chifukwa cha ntchito zake zazikulu

      • Dzina la Mulungu ndi loyera komanso lochititsa mantha (9)

      • Kuopa Yehova ndi nzeru (10)

  • 112

    • Munthu wolungama amaopa Yehova

      • “Munthu amene amakongoza ena mosaumira, zinthu zimamuyendera bwino” (5)

      • “Wolungama adzakumbukiridwa mpaka kalekale” (6)

      • Wowolowa manja amathandiza anthu osauka (9)

  • 113

    • Mulungu amene ali kumwamba amadzutsa munthu wonyozeka

      • Dzina la Yehova litamandidwe mpaka kalekale (2)

      • Mulungu amatsika mʼmunsi  (6)

  • 114

    • Kupulumutsidwa kwa Aisiraeli kuchoka ku Iguputo

      • Nyanja inathawa (5)

      • Mapiri anadumphadumpha ngati nkhosa zamphongo (6)

      • Mwala wa nsangalabwi unakhala kasupe (8)

  • 115

    • Ulemerero uyenera kuperekedwa kwa Mulungu yekha

      • Mafano opanda moyo (4-8)

      • Dziko lapansi linaperekedwa kwa anthu (16)

      • “Akufa satamanda Ya” (17)

  • 116

    • Nyimbo yoyamikira

      • “Yehova ndidzamubwezera chiyani?” (12)

      • “Ndidzamwa zamʼkapu yachipulumutso” (13)

      • “Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova” (14, 18)

      • Imfa ya anthu okhulupirika ndi yopweteka kwambiri (15)

  • 117

    • Anthu a mitundu yonse akupemphedwa kuti atamande Yehova

      • Chikondi chokhulupirika cha Mulungu nʼchachikulu (2)

  • 118

    • Yamikani Yehova chifukwa wapambana

      • ‘Ndinaitana Ya ndipo anandiyankha’ (5)

      • “Yehova ali kumbali yanga” (6, 7)

      • Mwala wokanidwa wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona (22)

      • “Amene akubwera mʼdzina la Yehova” (26)

  • 119

    • Kuyamikira mawu amtengo wapatali a Mulungu

      • “Kodi wachinyamata angakhale bwanji woyera pa moyo wake?” (9)

      • “Ndimakonda kwambiri zikumbutso zanu” (24)

      • “Mawu anu ndi chiyembekezo changa” (74, 81, 114)

      • “Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!” (97)

      • “Wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse” (99)

      • “Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga” (105)

      • “Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha” (160)

      • Amene amakonda chilamulo cha Mulungu amakhala ndi mtendere (165)

  • 120

    • Mlendo akulakalaka mtendere

      • ‘Ndipulumutseni ku lilime lachinyengo’ (2)

      • “Ine ndimakonda mtendere” (7)

  • 121

    • Yehova amateteza anthu ake

      • “Thandizo langa limachokera kwa Yehova” (2)

      • Yehova samagona (3, 4)

  • 122

    • Pemphero lopempherera mtendere wa Yerusalemu

      • Anasangalala pamene ankapita kunyumba ya Yehova (1)

      • Mzinda womangidwa ngati chinthu chimodzi chogwirizana (3)

  • 123

    • Kupempha Yehova kuti awakomere mtima

      • ‘Monga atumiki ake, tikuyangʼana kwa Yehova’ (2)

      • “Tanyozeka kwambiri” (3)

  • 124

    • “Yehova akanapanda kukhala nafe”

      • Kuthawa pamsampha wothyoka (7)

      • “Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova” (8)

  • 125

    • Yehova amateteza anthu ake

      • “Mofanana ndi mapiri amene azungulira Yerusalemu” (2)

      • “Mu Isiraeli mukhale mtendere” (5)

  • 126

    • Kubwezeretsedwa kosangalatsa kwa Ziyoni

      • “Yehova watichitira zazikulu” (3)

      • Kusiya kulira nʼkuyamba kusangalala (5, 6)

  • 127

    • Popanda Mulungu, chilichonse nʼchopanda phindu

      • “Yehova akapanda kumanga nyumba” (1)

      • Ana ndi mphoto yochokera kwa Mulungu (3)

  • 128

    • Woopa Yehova amasangalala

      • Mkazi wokhala ngati mtengo wa mpesa wobereka zipatso (3)

      • “Uone zinthu zikuyenda bwino mu Yerusalemu” (5)

  • 129

    • Kuukiridwa koma osagonjetsedwa

      • Odana ndi Ziyoni achititsidwa manyazi (5)

  • 130

    • “Pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu”

      • “Mukanakhala kuti mumayangʼanitsitsa zolakwa” (3)

      • Yehova amakhululuka ndi mtima wonse (4)

      • “Ndikuyembekezera Yehova ndi mtima wonse” (6)

  • 131

    • Wokhutira ngati mwana amene anamusiyitsa kuyamwa

      • “Sindilakalaka zinthu zapamwamba kwambiri” (1)

  • 132

    • Anasankha Davide komanso Ziyoni

      • “Musakane wodzozedwa wanu” (10)

      • Ansembe a ku Ziyoni adzawaveka chipulumutso (16)

  • 133

    • Kukhala pamodzi mogwirizana

      • Ngati mafuta pamutu wa Aroni (2)

      • Ngati mame a ku Herimoni (3)

  • 134

    • Kutamanda Mulungu usiku

      • “Muzikhala oyera mukamapemphera mutakweza manja anu” (2)

  • 135

    • Tamandani Ya chifukwa ndi wamkulu

      • Zizindikiro komanso zodabwitsa ku Iguputo (8, 9)

      • “Dzina lanu lidzakhalapo kwamuyaya” (13)

      • Mafano opanda moyo (15-18)

  • 136

    • Chikondi chokhulupirika cha Yehova chidzakhalapo mpaka kalekale

      • Kumwamba ndi dziko lapansi zinapangidwa modabwitsa (5, 6)

      • Farao anafera pa Nyanja Yofiira (15)

      • Mulungu amakumbukira anthu amene afooka (23)

      • Chakudya cha chamoyo chilichonse (25)

  • 137

    • Mʼmphepete mwa mitsinje ya ku Babulo

      • Palibe nyimbo za ku Ziyoni zimene zinaimbidwa (3, 4)

      • Babulo adzawonongedwa (8)

  • 138

    • Mulungu amatisamalira ngakhale kuti ndi wapamwamba

      • ‘Munayankha pemphero langa’ (3)

      • ‘Ngakhale nditakumana ndi mavuto, inu mumandipulumutsa’ (7)

  • 139

    • Mulungu amadziwa bwino atumiki ake

      • Palibe amene angathawe mzimu wa Mulungu (7)

      • “Munandipanga modabwitsa” (14)

      • “Maso anu anandiona ngakhale pamene ndinali mluza” (16)

      • “Munditsogolere mʼnjira yamuyaya” (24)

  • 140

    • Yehova ndi Mpulumutsi wamphamvu

      • Anthu oipa ali ngati njoka (3)

      • Anthu ankhanza adzagwa (11)

  • 141

    • Pemphero lopempha kuti atetezedwe

      • “Pemphero langa likhale ngati zofukiza” (2)

      • Kudzudzulidwa ndi munthu wolungama kuli ngati mafuta (5)

      • Oipa adzagwera mʼmaukonde awo omwe (10)

  • 142

    • Pemphero lopempha kuti apulumutsidwe kwa anthu amene akuwazunza

      • “Palibenso kulikonse kumene ndingathawire” (4)

      • ‘Inu ndinu malo okhawo amene ndili nawo’ (5)

  • 143

    • Kuyembekezera Mulungu ngati dziko louma limene likuyembekezera kuti mvula igwe

      • ‘Ndimaganizira ntchito zanu’ (5)

      • “Ndiphunzitseni kuchita zimene mumafuna” (10)

      • ‘Mzimu wanu umene ndi wabwino unditsogolere’ (10)

  • 144

    • Pemphero lopempha kupulumutsidwa

      • ‘Munthu ndi ndani?’ (3)

      • ‘Adani achite mantha’ (6)

      • Osangalala ndi anthu a Yehova (15)

  • 145

    • Kutamanda Mulungu, Mfumu yaikulu

      • ‘Ndidzalengeza za ukulu wa Mulungu’ (6)

      • “Yehova ndi wabwino kwa anthu onse” (9)

      • “Okhulupirika anu adzakutamandani” (10)

      • Ufumu wamuyaya wa Mulungu (13)

      • Dzanja la Mulungu limakwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse (16)

  • 146

    • Kudalira Mulungu, osati anthu

      • Munthu akafa zimene amaganiza zimatheratu (4)

      • Mulungu amadzutsa anthu amene awerama (8)

  • 147

    • Kutamanda Mulungu chifukwa cha ntchito zachikondi komanso zamphamvu

      • Amachiritsa anthu osweka mtima (3)

      • Amatchula dzina nyenyezi iliyonse (4)

      • Amapereka sinowo ngati ubweya wa nkhosa (16)

  • 148

    • Chilengedwe chonse chitamande Yehova

      • “Mutamandeni, inu angelo ake onse” (2)

      • ‘Mutamandeni, inu dzuwa, mwezi ndi nyenyezi’ (3)

      • Ana komanso achikulire atamande Mulungu (12, 13)

  • 149

    • Nyimbo yotamanda Mulungu chifukwa chopambana

      • Mulungu amasangalala ndi anthu ake (4)

      • Ulemerero ndi wa anthu onse okhulupirika a Mulungu (9)

  • 150

    • Chamoyo chilichonse chitamande Ya

      • Aleluya! (1, 6)