Salimo 142:1-7

  • Pemphero lopempha kuti apulumutsidwe kwa anthu amene akuwazunza

    • “Palibenso kulikonse kumene ndingathawire” (4)

    • ‘Inu ndinu malo okhawo amene ndili nawo’ (5)

Masikili.* Salimo ndiponso pemphero la Davide, pamene anali kuphanga.+ 142  Ndimafuulira Yehova kuti andithandize.+Ndimachonderera Yehova kuti andikomere mtima.   Ndimakhuthula nkhawa zanga pamaso pake.Ndimafotokoza mavuto anga pamaso pake+   Pamene mphamvu zanga zatha.* Ndikatero, mumayangʼanitsitsa njira yanga.+ Adani anga anditchera msamphaMʼnjira imene ndikuyenda.   Yangʼanani kudzanja langa lamanja ndipo muoneKuti palibe aliyense amene akusamala za ine.*+ Palibenso kulikonse kumene ndingathawire,+Ndipo palibe amene akundidera nkhawa.   Ndikuitana inu Yehova kuti mundithandize. Ndikunena kuti: “Inu ndinu malo anga othawirako,+Malo okhawo amene ndili nawo* mʼdziko la anthu amoyo.”   Mvetserani kulira kwanga kopempha thandizo,Chifukwa ndavutika kwambiri. Ndipulumutseni kwa anthu amene akundizunza,+Chifukwa iwo ndi amphamvu kuposa ine.   Nditulutseni mundende yamdimaKuti nditamande dzina lanu. Anthu olungama andizungulireChifukwa mumandichitira zabwino.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Pamene mtima wanga walefuka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akuzindikira kuti ndilipo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Gawo langa.”