Salimo 33:1-22

  • Tamandani Mlengi

    • “Muimbireni nyimbo yatsopano” (3)

    • Zinthu zinalengedwa ndi mawu komanso mzimu wa Yehova (6)

    • Wosangalala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova (12)

    • Diso la Yehova limayangʼana anthu amene amamuopa (18)

33  Fuulani mosangalala chifukwa cha Yehova,+ olungama inu. Mʼpoyenera kuti olungama atamande Mulungu.   Yamikani Yehova poimba zeze.Muimbireni nyimbo zomutamanda ndi choimbira cha zingwe 10.   Muimbireni nyimbo yatsopano.+Imbani mwaluso choimbira cha zingwe ndipo muzifuula mosangalala.   Chifukwa mawu a Yehova ndi oona,+Ndipo chilichonse chimene amachita ndi chodalirika.   Iye amakonda chilungamo ndipo amaweruza mosakondera.+ Dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chokhulupirika cha Yehova.+   Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova,+Ndipo analenga zinthu zonse zakumwamba* ndi mpweya wamʼkamwa mwake.   Amasonkhanitsa madzi amʼnyanja ngati damu,+Amaika madzi amphamvu mʼnyumba zosungiramo zinthu.   Dziko lonse lapansi liope Yehova.+ Anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi achite naye mantha.   Chifukwa iye analankhula ndipo zinachitika.+Iye analamula ndipo zinakhalapo.+ 10  Yehova wasokoneza zolinga za mitundu ya anthu.+Walepheretsa mapulani* a mitundu ya anthu.+ 11  Koma zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale.+Maganizo amumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo. 12  Wosangalala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova,+Anthu amene iye wawasankha kuti akhale cholowa chake.+ 13  Yehova amayangʼana padziko lapansi, kuchokera kumwamba.Iye amaona ana onse a anthu.+ 14  Kuchokera kumalo amene amakhala,Amayangʼanitsitsa anthu amene akukhala padziko lapansi. 15  Iye ndi amene amaumba mitima ya anthu onse,Ndipo amafufuza ntchito zawo zonse.+ 16  Palibe mfumu imene inapulumuka chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo.+Munthu wamphamvu sapulumuka chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+ 17  Si nzeru kudalira hatchi chifukwa singapulumutse munthu,+Mphamvu zake zochuluka sizingapulumutse munthu 18  Taonani! Diso la Yehova limayangʼana anthu amene amamuopa,+Amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika, 19  Kuti awapulumutse ku imfa,Komanso kuwathandiza kuti akhale ndi moyo pa nthawi ya njala.+ 20  Tikuyembekezera Yehova. Iye ndi amene amatithandiza komanso ndi chishango chathu.+ 21  Mulungu amachititsa kuti mitima yathu isangalale,Chifukwa timadalira dzina lake loyera.+ 22  Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chikhale pa ife,+Pamene tikupitiriza kuyembekezera inu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “makamu ake onse.”
Kapena kuti, “maganizo.”